Kwa Aroma
16 Ndikufuna kukudziwitsani za mlongo wathu Febe, amene akutumikila mu mpingo wa ku Kenkereya. 2 Mulandileni mwa Ambuye mmene mumalandilila oyelawo. Ndipo mum’patse thandizo lililonse limene angafunikile, cifukwa nayenso anateteza abale ambili, kuphatikizapo ine.
3 Mundipelekele moni kwa Purisika ndi Akula, anchito anzanga potumikila Khristu Yesu. 4 Iwo anaika miyoyo yawo paciopsezo cifukwa ca ine, ndipo si ine ndekha amene ndikuwayamikila, nayonso mipingo ya anthu a mitundu ina ikuwayamikila. 5 Ndikupelekanso moni ku mpingo umene umasonkhana m’nyumba yawo. Moni kwa wokondedwa wanga Epeneto, amene ndi cipatso coyambilila ca Khristu ku Asia. 6 Moni kwa Mariya, amene wagwila nchito mwakhama pokuthandizani. 7 Moni kwa Anduroniko ndi Yuniya, amene ndi acibale anga komanso akaidi anzanga. Amenewa ndi amuna odziwika kwambili kwa atumwi, ndiponso akhala ogwilizana ndi Khristu kwa nthawi yaitali kuposa ine.
8 Mundipelekele moni kwa Ampiliato, wokondedwa wanga mwa Ambuye. 9 Moni kwa Uribano, wanchito mnzathu mwa Khristu, komanso kwa wokondedwa wanga Sitaku. 10 Moni kwa Apele, wokhulupilika mwa Khristu. Moni kwa anthu a m’banja la Arisitobulo. 11 Moni kwa wacibale wanga Herodiona. Moni kwa anthu a m’banja la Narikiso omwe ndi otsatila a Ambuye. 12 Moni kwa Turufena ndi Turufosa, azimayi amene akugwila nchito mwakhama potumikila Ambuye. Moni kwa Peresida, wokondedwa wathu, amene wagwila nchito mwakhama potumikila Ambuye. 13 Moni kwa Rufu, wosankhidwa mwa Ambuye. Komanso kwa amayi ake amenenso ndi amayi anga. 14 Moni kwa Asunkirito, Felego, Heme, Pateroba, Heremase, ndiponso abale amene ali nawo limodzi. 15 Moni kwa Filologo ndi Yuliya, Nerea ndi mlongo wake komanso Olumpa ndi oyela onse amene ali nawo limodzi. 16 Mupatsane moni mwacikondi. Mipingo yonse ya Khristu ikupeleka moni.
17 Tsopano abale, ndikukulimbikitsani kuti musamale ndi anthu amene amabweletsa magawano komanso kucita zinthu zopunthwitsa ena. Izi ndi zosemphana ndi zimene munaphunzila, conco muziwapewa. 18 Pakuti anthu otelo si akapolo a Ambuye wathu Khristu, koma a zilakolako* zawo. Ndipo amagwilitsa nchito mawu okopa ndiponso acinyengo kuti apusitse anthu osalakwa. 19 Anthu onse akudziwa kuti ndinu omvela, ndipo ndine wokondwa kwambili cifukwa ca inu. Ndikufuna kuti mukhale anzelu pa zabwino, koma osadziwa kanthu pa zoipa. 20 Mulungu amene amapeleka mtendele adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu posacedwapa. Cisomo ca Ambuye wathu Yesu cikhale nanu.
21 Wanchito mnzanga Timoteyo akupeleka moni. Nawonso acibale anga amene ndi Lukiyo, Yasoni, ndi Sosipato akupeleka moni.
22 Ine Teritio, amene ndalemba kalatayi, ndikuti moni mwa Ambuye.
23 Gayo, amene ndikukhala kunyumba kwake, komanso amene mpingo umasonkhana ku nyumba kwake, akupeleka moni. Erasito msungicuma* wa mzinda akupeleka moni. Nayenso Kwarito m’bale wake akupeleka moni. 24* ——
25 Mulungu angakulimbitseni pogwilitsa nchito uthenga wabwino umene ndikulengeza, ndiponso uthenga wonena za Yesu Khristu umene ukulalikidwa. Uthengawu ndi wogwilizana ndi zimene zaululidwa zokhudza cinsinsi copatulika cimene cakhala cobisika kwa nthawi yaitali. 26 Koma tsopano cinsinsi cimeneci caululidwa, ndipo anthu a mitundu yonse acidziwa kudzela m’Malemba aulosi. Izi n’zogwilizana ndi lamulo la Mulungu wamuyaya. Kuti anthu a mitundu yonse azimumvela mwa cikhulupililo. 27 Kwa Mulungu yekhayo amene ndi wanzelu, kukhale ulemelelo kwamuyaya kudzela mwa Yesu Khristu. Ameni.