Kwa Aroma
9 Ndikunena zoona mogwilizana ndi Khristu, sindikunama ayi. Cikumbumtima canga cikundicitila umboni mogwilizana ndi mzimu woyela, 2 kuti ndikumva cisoni kwambili ndi kupweteka kosalekeza mu mtima mwanga. 3 Ndikanakonda kuti ine ndilekanitsidwe ndi Khristu monga munthu wotembeleledwa kaamba ka abale anga, anthu a mtundu wanga, 4 amene ndi Aisiraeli. Mulungu anawatenga iwo kuti akhale ana ake ndipo anawapatsa ulemelelo, mapangano, Cilamulo, utumiki wopatulika, ndi malonjezo. 5 Iwo ndi ana a makolo athu akale. Ndipo Khristu anabadwa ngati munthu kucokela kwa iwo. Mulungu, amene ndi wamkulu pa zinthu zonse, atamandike kwamuyaya. Ameni.
6 Komabe sikuti mawu a Mulungu sanakwanilitsidwe ayi. Cifukwa si onse amene ndi mbadwa* za Aisiraeli amene ndi “Aisiraeli enieni.” 7 Ndipo si onse amene ndi ana, cabe cifukwa ndi mbadwa* za Abulahamu. Koma Malemba amati, amene adzachedwa kuti “Mbadwa* zako adzacokela mwa Isaki.” 8 Izi zikutanthauza kuti si ana akuthupi amene ndi ana enieni a Mulungu, koma ana obadwa mogwilizana ndi lonjezolo ndi amene amawelengeledwa kuti ndi mbadwa.* 9 Pakuti lonjezo lija linati: “Panthawi ngati ino, ndidzabwela ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.” 10 Lonjezolo silinapelekedwe pa nthawi yokhayo. Koma linapelekedwanso pamene Rabeka anakhala ndi pakati pa ana amapasa kucokela kwa munthu mmodzi Isaki, kholo lathu lija. 11 Mapasawo asanabadwe komanso asanacite ciliconse cabwino kapena coipa, Mulungu anaonetsa kuti colinga cake cidzadalila iye amene amaitana, osati zocita za munthu. 12 Iye anauza Rabeka kuti: “Wamkulu adzakhala kapolo kwa wamngʼono.” 13 Mogwilizana ndi zimene Malemba amakamba kuti: “Ndinakonda Yakobo, koma Esau ndinadana naye.”
14 Ndiye tikambe kuti ciyani pamenepa? Kodi Mulungu alibe cilungamo? Ayi ndithu! 15 Cifukwa iye anauza Mose kuti: “Ine ndidzaonetsa cifundo kwa munthu aliyense amene ndafuna kumuonetsa cifundo, ndipo amene ndikufuna kumukomela mtima ndidzamukomela mtima.” 16 Conco sizidalila kufuna kwa munthu kapena khama lake,* koma Mulungu amene ndi wacifundo. 17 Ponena za Farao, Malemba amati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikuonetse mphamvu zanga komanso kuti dzina langa lilengezedwe pa dziko lonse lapansi.” 18 Conco iye amacitila cifundo munthu aliyense amene wafuna kumucitila cifundo, koma amalola munthu aliyense amene wafuna kuumitsa mtima wake kuti auumitse.
19 Conco ungandiuze kuti: “N’cifukwa ciyani Mulungu akupezabe anthu zifukwa? Kodi ndani akutsutsa cifunilo cake?” 20 Munthu iwe, ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu? Kodi cinthu coumbidwa cingauze munthu amene anaciumba kuti, “Unandipangilanji conci?” 21 Kodi simukudziwa kuti woumba mbiya ali ndi ufulu woumba ciwiya cina kukhala ca nchito yolemekezeka, cina kukhala ca nchito yonyozeka kucokela ku dothi limodzimodzi? 22 Ndiye bwanji ngati Mulungu anafuna kuonetsa mkwiyo wake kuti mphamvu zake zidziwike, ndipo analekelela moleza mtima kwambili anthu oyenela kuwonongedwa amene anamukwiyitsa?* 23 Ndiponso bwanji ngati anacita zimenezo kuti aonetse kukula kwa ulemelelo wake kwa anthu oyenela kuwacitila cifundo,* amene anawakonzelatu kuti alandile ulemelelo, 24 ndipo anthu ake ndi ife amene anatiitana osati kucokela kwa Ayuda okha, koma kucokelanso ku mitundu ina? 25 Ndi zofanananso ndi zimene ananena mʼbuku la Hoseya kuti: “Aja amene si anthu anga ndidzawachula kuti ‘anthu anga,’ ndipo mkazi amene sanali kukondedwa ndidzamuchula kuti ‘wokondedwa.’ 26 Kumene analikuuzidwa kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ kumeneko adzauzidwa kuti, ‘Ndinu ana a Mulungu wamoyo.’”
27 Komanso, Yesaya analengeza zokhudza Isiraeli kuti: “Ngakhale kuti ana a Isiraeli adzakhala ambili monga mcenga wakunyanja, ndi ocepa cabe amene adzapulumuke. 28 Cifukwa Yehova adzaweluza milandu pa dziko lapansi n’kuitsiliza mwamsanga.” 29 Ndiponso malinga ndi zimene Yesaya ananenelatu, “Yehova wa magulu ankhondo akanapanda kutisiyila mbadwa,* tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora.”
30 Ndiye tikambe kuti ciyani pamenepa? Tikambe kuti anthu a mitundu ina ngakhale kuti sanatsatile cilungamo, iwo anapeza cilungamo cimene cimabwela cifukwa ca cikhulupililo. 31 Koma ngakhale kuti Aisiraeli anali kutsatila lamulo la cilungamo, sanakwanitse kulitsatila lamulo limenelo. 32 Cifukwa ciyani? Cifukwa cakuti anali kulitsatila mwa zocita zawo, koma osati mwa cikhulupililo. Iwo anapunthwa “pa mwala wopunthwitsa” 33 mogwilizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Taonani! Ine ndikuika mu Ziyoni mwala wopunthwitsa ndiponso thanthwe lokhumudwitsa, koma munthu wokhulupilila mwalawo sadzakhumudwa.”