Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Yohane
7 Izi zitatha, Yesu anapitiliza kugwila nchito yake* mu Galileya. Iye sanafune kucita zimenezi mu Yudeya, cifukwa Ayuda anali kufuna kumupha. 2 Komabe cikondwelelo ca Misasa ca Ayuda cinali citayandikila. 3 Conco abale ake anamuuza kuti: “Cokani kuno mupite ku Yudeya kuti ophunzila anu nawonso akaone nchito zimene mukucita. 4 Cifukwa palibe munthu amene amacita ciliconse mobisa ngati akufuna kuti anthu amudziwe. Ngati mukucita zinthu zimenezi, dzionetseni poyela ku dzikoli.” 5 Koma abale akewo sanali kukhulupilila mwa iye. 6 Conco Yesu anawauza kuti: “Ine nthawi yanga sinafike, koma kwa inu nthawi iliyonse ndi yoyenela. 7 Dzikoli lilibe cifukwa cokudelani, koma ine limadana nane cifukwa ndimacitila umboni kuti nchito zake ndi zoipa. 8 Inu pitani kucikondweleloko, koma ine sindipitako cifukwa nthawi yanga ikalibe kukwana.” 9 Iye atawauza zimenezi, anakhalabe ku Galileya.
10 Koma pamene abale ake ananyamuka kupita kucikondweleloco, nayenso anapita. Osati moonekela, koma mwakabisila. 11 Conco Ayuda anayamba kumufunafuna kucikondweleloco n’kumafunsa kuti: “Kodi munthu uja ali kuti?” 12 Ndipo anthu oculuka m’khamulo anali kunong’onezana zinthu zambili zokhudza iye. Ena anali kukamba kuti: “Munthu amene uja ndi wabwino.” Koma ena anali kukamba kuti: “Iyayi, iye akusoceletsa khamuli.” 13 Koma palibe amene anali kukamba za iye poyela cifukwa anthuwo anali kuopa Ayuda.
14 Cikondweleloco citafika pakati, Yesu analowa m’kacisi n’kuyamba kuphunzitsa. 15 Ayudawo anadabwa kwambili, ndipo anafunsa kuti: “Kodi munthu ameneyu anawadziwa bwanji Malemba* popeza sanapite ku sukulu?”* 16 Yesu anayankha kuti: “Zimene ndimaphunzitsa sizanga ayi, koma ndi za iye amene anandituma. 17 Ngati munthu afuna kucita cifunilo ca Mulungu, adzadziwa ngati zimene ine ndimaphunzitsa zimacokela kwa Mulunguyo, kapena ngati ndimakamba zongoganiza pa ine ndekha. 18 Aliyense amene amakamba za m’maganizo mwake amadzifunila ulemelelo, koma aliyense wofunila ulemelelo iye amene anamutuma, ameneyo ndi woona ndipo mwa iye mulibe cinyengo. 19 Mose anakupatsani Cilamulo si conco? Koma palibe ngakhale mmodzi wa inu amene amamvela Cilamuloco. Nanga n’cifukwa ciyani mukufuna kundipha?” 20 Khamulo linayankha kuti: “Uli ndi ciwanda iwe. Ndani akufuna kukupha?” 21 Yesu anawayankha kuti: “Ndangocita cinthu cimodzi cokha, koma nonse mwadabwa. 22 Pa cifukwa cimeneci, Mose anakupatsani mdulidwe. Sikuti unacokela kwa Mose ayi, koma unacokela kwa makolo akale, ndipo inu mumacita mdulidwe kwa munthu pa sabata. 23 Ngati munthu mumamucita mdulidwe pa sabata n’colinga cakuti Cilamulo ca Mose cisaphwanyidwe, kodi ine mwandikwiyila cifukwa cakuti ndacilitsa munthu pa tsiku la sabata? 24 Lekani kuweluza moyang’ana maonekedwe akunja, koma weluzani ndi ciweluzo colungama.”
25 Ndiyeno anthu ena okhala mu Yerusalemu anayamba kukamba kuti: “Uyu ndiye munthu amene anthu ena akufuna kumupha, si conco? 26 Koma onani! Iye akulankhula poyela, ndipo iwo sakumuuza ciliconse. Kodi olamulilawa afika potsimikiza kuti ameneyu ndi Khristudi? 27 Ayi, ife tidziwa kumene munthuyu akucokela. Koma Khristu akadzabwela palibe adzadziwa kumene wacokela.” 28 Kenako pamene Yesu anali kuphunzitsa m’kacisi, anafuula kuti: “Inu mundidziwa, ndipo kumene ndimacokela mumadziwakonso. Ine sindinabwele mwa kufuna kwanga, koma amene anandituma ndi weniweni, ndipo inuyo simum’dziwa. 29 Ine ndimudziwa cifukwa ndine nthumwi yake. Ndipo ameneyo ndiye anandituma.” 30 Conco iwo anayamba kufunafuna njila yomugwilila, koma palibe anakwanitsa kutelo cifukwa nthawi yake inali isanafike. 31 Komabe ambili m’khamulo anamukhulupilila ndipo anali kukamba kuti: “Kodi Khristu akadzabwela adzacita zizindikilo zoposa zimene munthu uyu wacita?”
32 Afarisi anamva zimene anthu m’khamulo anali kunong‘onezana ponena za iye. Ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma alonda kuti akamugwile.* 33 Ndiyeno Yesu anakamba kuti: “Ndikhalabe nanu kwa kanthawi ndisanapite kwa amene anandituma. 34 Mudzandifunafuna koma simudzandipeza, ndipo kumene ndidzapite, inu simudzakwanitsa kufikako.” 35 Conco Ayudawo anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu afuna kupita kuti kumene sitingamupeze? Kodi mwina afuna kupita kwa Ayuda amene anamwazikana pakati pa Agiriki kuti akaphunzitse Agirikiwo? 36 Kodi atanthauzanji pokamba kuti, ‘Mudzandifunafuna koma simudzandipeza, ndipo kumene ndidzapite inu simudzakwanitsa kufikako’?”
37 Pa tsiku lothela, tsiku lalikulu la cikondweleloco, Yesu anaimilila n’kuufula kuti: “Ngati pali wina amene ali ndi ludzu abwele kwa ine adzamwe madzi. 38 Monga mmene malemba amanenela, aliyense woika cikhulupililo mwa ine, ‘Mkati mwake mudzatuluka mitsinje ya madzi amoyo.’” 39 Koma Yesu anakamba izi ponena za mzimu woyela umene anthu oika cikhulupililo mwa iye anali pafupi kulandila. Panthawiyo, anthu anali asanalandile mzimu cifukwa Yesu anali asanalandile ulemelelo. 40 Ena m’khamulo amene anamva mawu amenewa, anayamba kukamba kuti: “Ndithudi uyu ndi Mneneli.” 41 Ena anali kukamba kuti: “Uyu ndi Khristu.” Koma ena anali kukamba kuti: “Kodi Khristu angacokele mu Galileya? 42 Kodi sikuti malemba amanena kuti Khristu adzacokela mu m’badwo wa Davide komanso ku Betelehemu, mudzi umene Davide anali kukhala?” 43 Conco khamulo linagawikana pa nkhani yokhudza iye. 44 Ena a iwo anafuna kumugwila,* koma palibe ngakhale mmodzi amene anakwanitsa kutelo.
45 Ndiyeno alondawo atabwelako, ansembe aakulu ndi Afarisi anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani simunabwele naye?” 46 Alondawo anayankha kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” 47 Afarisi anayankha kuti: “Kodi inunso mwasoceletsedwa? 48 Palibe wolamulila kapena Mfarisi ngakhale mmodzi amene waika cikhulupililo mwa iye, alipo kapena? 49 Koma khamu la anthu limene silidziwa Cilamulo ndi lotembeleledwa.” 50 Nikodemo amene anafikila Yesu kumbuyoku, komanso amene anali mmodzi wa Afarisi, anawauza kuti: 51 “Malamulo athu salola kuweluza munthu asanafotokoze mbali yake, komanso tisanadziwe zimene iye anacita, si conco?” 52 Iwo anamuyankha kuti: “Kodi iwenso ndiwe wocokela ku Galileya? Fufuza ndipo sudzapeza pamene pamati mu Galileya mudzatuluka mneneli.”*