Kwa Aefeso
6 Inu ana, muzimvela makolo anu mwa Ambuye, cifukwa kucita zimenezi n’koyenela. 2 “Muzilemekeza atate anu ndi amai anu.” Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Lonjezo lake ndi lakuti: 3 “Kuti zinthu zikuyendeleni bwino, ndiponso kuti mukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.” 4 Inu atate, musamakwiyitse ana anu, koma pitilizani kuwalela mwa kuwapatsa malangizo,* komanso kuwaphunzitsa malinga n’zimene Yehova amanena.
5 Inu akapolo, muzimvela ambuye anu. Muziwaopa ndi kuwalemekeza mocokela pansi pa mtima, ngati mmene mumacitila ndi Khristu. 6 Musacite zimenezi mwaciphamaso, cabe pofuna kukondweletsa anthu, koma ngati akapolo a Khristu amene akucita cifunilo ca Mulungu ndi mtima wonse. 7 Muzitumikila ambuye anu ndi mtima wonse ngati mukutumikila Yehova osati anthu, 8 popeza mukudziwa kuti ciliconse cimene munthu angacite, Yehova adzamupatsa mphoto, kaya munthuyo ndi kapolo kapena mfulu. 9 Inunso ambuye, muzicitila akapolo anu cimodzi-modzi. Musamawaopsyeze cifukwa mukudziwa kuti Ambuye wawo komanso wanu, ali kumwamba, ndipo alibe tsankho.
10 Pomaliza ndikuti, pitilizani kupeza mphamvu mwa Ambuye komanso mu nyonga zake zazikulu. 11 Bvalani zida zonse za nkhondo zocokela kwa Mulungu kuti musagonje polimbana ndi macenjela a* Mdyelekezi. 12 Pakuti sitikulimbana* ndi anthu a thupi la magazi ndi nyama ai. Koma tikulimbana ndi maboma, maulamulilo, olamulila dziko a mu mdimawu, komanso makamu a mizimu yoipa m’malo a kumwamba. 13 Pa cifukwa cimeneci, nyamulani zida zonse za nkhondo zocokela kwa Mulungu, kuti pa tsiku loipa musadzagonje, ndiponso kuti mukakwanitsa kucita zonse bwino-bwino, mudzathe kulimba.
14 Conco, khalani olimba, mutamanga kwambili coonadi m’ciuno mwanu ngati lamba, mutabvala codzitetezela pacifuwa cacilungamo, 15 komanso mutabvala nsapato kumapazi anu pokonzekela kulengeza uthenga wabwino wamtendele. 16 Kuonjezela apo, nyamulani cishango cacikulu cacikhulupililo, cimene mudzathe kuzimitsila naco mibvi yonse yoyaka moto ya woipayo. 17 Komanso bvalani cisoti ca cipulumutso, ndipo nyamulani lupanga la mzimu, lomwe ndi mau a Mulungu. 18 Pamene mukucita zimenezi, muzipemphela pa cocitika ciliconse mu mzimu, pogwilitsa nchito pemphelo ndi pembedzelo la mtundu uliwonse. Kuti zimenezi zitheke, khalani maso ndipo nthawi zonse muzipemphelela oyela onse mopembedzela. 19 Inenso muzindipemphelela kuti ndikayamba kulankhula, ndizipeza mau oyenelela kuti ndizitha kulankhula molimba mtima ndikamalalikila za cinsinsi copatulika ca uthenga wabwino, 20 umene ndine kazembe wake womangidwa ndi unyolo. Muzindipemphelela kuti ndizilankhula za uthengawo molimba mtima ngati mmene ndiyenela kucitila.
21 Tsopano kuti mudziwenso mmene zinthu zikuyendela pa umoyo wanga ndi mmene ndilili, Tukiko, m’bale wokondedwa ndiponso mtumiki wokhulupilika wa Ambuye, adzakufotokozelani zonse. 22 Ndi cimene ndamutumizila kwa inu kuti mudziwe za umoyo wathu, ndiponso kuti atonthoze mitima yanu.
23 Mtendele, cikondi, ndiponso cikhulupililo cocokela kwa Mulungu Atate ndi kwa Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu abale. 24 Cisomo cikhale pa onse amene ali ndi cikondi ceniceni pa Ambuye wathu Yesu Khristu.