Kwa Aroma
2 Conco kaya ndiwe ndani, ngati umaweluza ena, ulibe cifukwa comveka codzilungamitsila. Pakuti ukamaweluza ena, umakhala ukudzitsutsa wekha, cifukwa iwenso umacita zomwezo. 2 Ndipo tikudziwa kuti Mulungu akamaweluza anthu amene amacita zimenezi kuti ndi oyenela kulandila cilango, amawaweluza mogwilizana ndi coonadi.
3 Koma kodi iwe ukamaweluza anthu amene amacita zinthu zimene iwenso umacita, kodi uganiza kuti udzacithawa ciweluzo ca Mulungu? 4 Kodi sudziwa kuti Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu, sakukukwiyila msanga, ndipo akukulezela mtima n’colinga coti ulape? 5 Koma cifukwa ca unkhutukumve wako ndi mtima wako wosafuna kulapa, ukuputa mkwiyo wa Mulungu umene udzaonekela pa tsiku la mkwiyo wake podzaulula ciweluzo cake colungama. 6 Iye adzaweluza aliyense malinga ndi zocita zake. 7 Adzapeleka moyo wosatha kwa anthu amene akufunafuna ulemelelo, ulemu ndi moyo wosawonongeka mwa kupilila pocita nchito zabwino. 8 Koma anthu okonda mikangano, amene satsatila coonadi koma amacita zosalungama, Mulungu adzawaonetsa mkwiyo wake. 9 Munthu aliyense wocita zinthu zoipa adzakumana ndi masautso komanso zowawa, kaya akhale Myuda kapena Mgiriki. 10 Koma munthu aliyense wocita zabwino, adzalandila ulemelelo, ulemu ndi mtendele, coyamba kwa Myuda kenako kwa Mgiriki. 11 Cifukwa Mulungu alibe tsankho.
12 Anthu onse amene anacimwa popanda kudziwa Cilamulo, adzafa popanda kudziwa Cilamulo. Koma onse amene anacimwa akudziwa Cilamulo, adzaweluzidwa mogwilizana ndi Cilamuloco. 13 Pakuti anthu amene amangomva cabe Cilamulo si olungama pamaso pa Mulungu, koma amene amacita zimene Cilamulo cimanena ndi amene adzaonedwe kuti ndi olungama. 14 Pakuti anthu a mitundu ina amene alibe Cilamulo, akamacita mwacibadwa zinthu za m’Cilamulo, ngakhale kuti alibe Cilamulo amaonetsa kuti ali ndi Cilamulo mu mtima mwawo. 15 Iwo amaonetsa kuti mfundo za m’Cilamulo zinalembedwa m’mitima yawo, ndipo cikumbumtima cawo cimawacitila umboni. Anthuwa maganizo awo amawatsutsa kapena kuwatsimikizila kuti acita zoyenela. 16 Zimenezi zidzacitika pa tsiku limene Mulungu, kudzela mwa Khristu Yesu, adzaweluza zinthu zobisika zimene anthu amacita mogwilizana ndi uthenga wabwino umene ndimalalikila.
17 Ena a inu ndinu Ayuda mwa dzina cabe, ndipo mumadalila Cilamulo, ndiponso mumanyadila kuti muli pa ubwenzi ndi Mulungu. 18 Mumadziwa cifunilo ca Mulungu komanso mumavomeleza zinthu zabwino kwambili cifukwa n’zimene munaphunzitsidwa* m’Cilamulo. 19 Mumakhulupilila kuti mungatsogolele akhungu komanso kuunikila anthu amene ali mu mdima. 20 Mumaganiza kuti mungawongolele anthu opanda nzelu, komanso mungaphunzitse ana cifukwa mumamvetsa komanso kudziwa coonadi copezeka m’Cilamulo. 21 Kodi iwe amene umaphunzitsa ena, bwanji sudziphunzitsa wekha? Iwe amene umalalikila kuti, “Usabe,” kodi umabanso? 22 Iwe amene umati, “Usacite cigololo,” kodi umacitanso cigololo? Iwe amene umanyansidwa ndi mafano, umabanso za mu akacisi a mafano? 23 Iwe amene umanyadila Cilamulo, kodi umanyoza Mulungu mwa kuphwanya Cilamulo? 24 Pakuti “dzina la Mulungu likunyozedwa pakati pa anthu a mitundu ina cifukwa ca inu,” monga mmene Malemba amanenela.
25 Mdulidwe umakhala waphindu pokhapokha ngati iweyo umatsatila Cilamulo. Koma ngati umaphwanya Cilamulo, mdulidwe wako umakhala wopanda phindu. 26 Conco ngati munthu wosadulidwa akutsatila mfundo zolungama za Cilamulo, ndiye kuti kusadulidwa kwake kudzaoneka ngati kudulidwa, si conco kodi? 27 Munthu wosadulidwa kuthupi akamatsatila Cilamulo, iye adzakuweluza mwa kucita zimene Cilamulo cimanena. Adzakuweluza iwe amene umaphwanya Cilamulo ngakhale kuti uli ndi malamulo olembedwa ndiponso ndiwe wodulidwa. 28 Amene ndi Myuda kunja kokha si Myuda weniweni, ndiponso mdulidwe wakunja kokha wocitidwa pa thupi si mdulidwe weniweni. 29 Kukhala Myuda weniweni kuli mumtima, ndipo mdulidwe wake ndi wa mumtima wocitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa. Munthu wotelo amatamandidwa ndi Mulungu, osati anthu.