Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
8 Posakhalitsa, Yesu anayamba kuyenda mzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi, akumalalikila ndi kulengeza uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu. Ndipo atumwi 12 aja anali naye. 2 Analinso ndi azimayi ena omwe anawatulutsa mizimu yonyansa ndi kuwacilitsa matenda awo. Maina awo anali Mariya wochedwanso Mmagadala, amene anamutulutsa ziwanda 7; 3 Jowana mkazi wa Kuza amene anali woyang’anila nyumba ya Herode, Suzana, ndi azimayi ena ambili amene anali kutumikila Yesu ndi atumwiwo pogwilitsa nchito zinthu zawo.
4 Tsopano khamu lalikulu la anthu litasonkhana pamodzi ndi amene anali kumulondola kucokela m’mizinda yosiyanasiyana, anawafotokozela fanizo lakuti: 5 “Munthu wina anapita kukafesa mbewu. Pamene anali kufesa mbewuzo, zina zinagwela m’mbali mwa msewu, ndipo mbalame zinabwela n’kuzidya. 6 Zina zinagwela pa thanthwe,* ndipo zitamela zinauma cifukwa panalibe cinyontho. 7 Mbewu zina zinagwela pa minga, ndipo minga zimene zinakulila pamodzi ndi mbewuzo zinalepheletsa mbewuzo kukula. 8 Koma zina zinagwela pa nthaka yabwino, ndipo zitamela zinabala zipatso kuwilikiza maulendo 100.” Iye atakamba izi, analankhula mokweza kuti: “Amene ali ndi matu akumva, amve!”
9 Koma ophunzila ake anamufunsa tanthauzo la fanizo limeneli. 10 Iye anati: “Inu mwapatsidwa mwayi womvetsa zinsinsi za Ufumu wa Mulungu. Koma kwa enawa, zonse ndi mafanizo cabe, kuti ngakhale aone, kuona kwawo kukhale kopanda phindu, ndipo ngakhale amve, kumva kwawo kukhale kopanda phindu. 11 Tsopano tanthauzo la fanizoli ndi ili: Mbewu ndi mawu a Mulungu. 12 Mbewu zogwela m’mbali mwa msewu zija ndi anthu amene amamva mawu, koma Mdyelekezi amabwela n’kucotsa mawuwo m’mitima yawo n’colinga cakuti asakhulupilile ndi kupulumutsidwa. 13 Mbewu zogwela pa thanthwe zija ndi anthu amene amamva mawu, ndipo amawalandila mwacimwemwe. Koma mawuwo sazika mizu mwa iwo ayi. Iwo amakhulupilila kwa kanthawi, koma nthawi yoyesedwa ikafika amagwa. 14 Mbewu zimene zimagwela pa minga ndi anthu amene amamva mawu, koma amatengeka ndi nkhawa, cuma, komanso zosangalatsa za moyo uno, moti amalephela kukula ndipo zipatso zawo sizikhwima. 15 Koma mbewu zimene zinagwela pa nthaka yabwino ndi anthu a mtima wabwino, amene pambuyo pomva mawu, amawasunga ndipo amabala zipatso mopilila.
16 “Palibe munthu amene amati akayatsa nyale, amaibwinikila ndi ciwiya kapena kuiika kunsi kwa bedi. Koma amaiika pa coikapo nyale kuti olowa m’nyumbamo aziona kuwala. 17 Pakuti palibe cobisika cimene sicidzaululika. Palibenso ciliconse cobisidwa mosamalitsa cimene sicidzadziwika kapena kuonekela poyela. 18 Conco, muzimvetsela mosamala kwambili, cifukwa aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zoculuka. Koma aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene amaganiza kuti ali nazo.”
19 Tsopano amayi ake ndi abale ake anabwela kwa iye. Koma sanathe kufika pafupi naye cifukwa ca khamu la anthu. 20 Conco, iye anauzidwa kuti: “Mayi anu ndi abale anu aimilila panja, afuna kuonana nanu.” 21 Iye anawayankha kuti: “Mayi anga ndi abale anga ndi awa amene amamvetsela mawu a Mulungu ndi kucita zimene mawuwo amanena.”
22 Tsiku lina, Yesu ndi ophunzila ake anakwela m’bwato, ndipo anauza ophunzilawo kuti: “Tiyeni tiwolokele ku tsidya lina la nyanja.” Conco anayamba kupalasila kumeneko. 23 Koma pamene iwo anali kupalasila kumeneko, Yesu anagona. Ndipo pa nyanjapo panauka namondwe woopsa, moti madzi anayamba kulowa m’bwatomo, ndipo bwatolo linatsala pang’ono kumila. 24 Pamenepo iwo anapita kukamuutsa n’kumuuza kuti: “Mlangizi, Mlangizi, tikufa!” Iye atamva zimenezi, ananyamuka n’kudzudzula mphepoyo ndi mafunde amphamvuwo, ndipo zinaleka. Kenako panakhala bata. 25 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Cikhulupililo canu cili kuti?” Koma iwo anacita mantha ndipo anadabwa kwambili, moti anayamba kufunsana kuti: “Kodi ameneyu ndani makamaka? Cifukwa akulamula ngakhale mphepo ndi madzi, ndipo zikumumvela!”
26 Ndiyeno iwo anakoceza bwato lawo m’mbali mwa nyanja, m’cigawo ca Agerasa, cimene n’copenyana ndi Galileya. 27 Yesu atatuluka m’bwato n’kufika kumtunda, anakumana ndi munthu wina wogwidwa ndi ciwanda wocokela mumzindawo. Kwa nthawi ndithu, munthuyo anali kukhala wosavala, ndipo sanali kukhala m’nyumba koma kumanda.* 28 Iye ataona Yesu, anakuwa n’kugwada pamaso pake, ndipo anafuula mokweza kuti: “Mufuna ciyani kwa ine, inu Yesu, Mwana wa Mulungu Wapamwambamwamba? Ndikukucondelelani kuti musandizunze ayi.” 29 (Pakuti Yesu anali atauza mzimu wonyansawo kuti utuluke mwa munthuyo. Nthawi zambili, mzimuwo unali kumugwila* mwamphamvu, ndipo mobwelezabweleza anali kumumanga ndi macheni, kumuika m’matangadza, komanso kumulonda. Koma anali kudula macheniwo n’kuthawila kumalo opanda anthu motsogoleledwa ndi ciwandaco.) 30 Yesu anamufunsa kuti: “Dzina lako ndani?” Iye anati: “Ndine Khamu.” Anatelo cifukwa mwa iye munali mutalowa ziwanda zambili. 31 Koma ziwandazo zinali kumucondelela Yesu kuti asazilamule kuti zipite kuphompho. 32 Tsopano gulu lalikulu la nkhumba linali kudya kumeneko paphili. Conco, ziwandazo zinamucondelela kuti azilole zikalowe m’nkhumbazo, ndipo anazilola. 33 Pamenepo ziwandazo zinatuluka mwa munthuyo n’kukalowa m’nkhumbazo. Zitatelo, nkhumbazo zinathamangila ku phompho mpaka kukagwela m’nyanja ndipo zinamila. 34 Koma owetela nkhumbazo ataona zimene zinacitikazo, anathawa n’kukafotokozela anthu mumzinda ndi m’midzi.
35 Ndiyeno anthu anapita kukaona zimene zinacitikazo. Atafika kwa Yesu, anapeza kuti munthu uja amene anatulutsidwa ziwanda ali khale ku mapazi a Yesu, atavala komanso maganizo ake ali bwinobwino. Iwo anacita mantha. 36 Amene anaona zimene zinacitikazo, anawafotokozela mmene munthu wogwidwa ndi ziwandayo anacilitsidwila. 37 Kenako gulu lalikulu la anthu ocokela m’madela ozungulila cigawo ca Agerasa linapempha Yesu kuti acoke m’cigawoco, cifukwa anagwidwa ndi mantha aakulu. Zitatelo, iye anapita kukakwela bwato n’kucoka. 38 Komabe, munthu amene anam’tulutsa ziwanda uja anacondelela Yesu mobwelezabweleza kuti apite naye. Koma Yesu anamubweza n’kunena kuti: 39 “Pita kwanu, ndipo uzifotokoza zimene Mulungu wakucitila.” Conco iye anacoka n’kuyamba kulengeza mumzinda wonsewo zimene Yesu anamucitila.
40 Yesu atafika ku Galileya, khamu la anthu linamulandila bwino cifukwa anali kumuyembekezela. 41 Koma kunabwela munthu wina dzina lake Yairo, ndipo munthu ameneyo anali mtsogoleli wa sunagoge. Iye anagwada pa mapazi a Yesu n’kuyamba kumucondelela kuti apite kunyumba kwake, 42 cifukwa mwana wake wamkazi mmodzi yekhayo, wa zaka pafupifupi 12 anali pafupi kumwalila.
Pamene Yesu anali kupita kumeneko, khamu la anthu linali kumupanikiza. 43 Tsopano panali mayi wina wodwala matenda otaya magazi kwa zaka 12, ndipo palibe amene anakwanitsa kumucilitsa. 44 Mayiyo anayandikila Yesu kumbuyo n’kugwila ulusi wopota wa covala cake cakunja, ndipo nthawi yomweyo matenda ake otaya magazi anatha. 45 Conco Yesu anafunsa kuti: “Ndani wandigwila?” Pamene onse anali kukana, Petulo anati: “Mlangizi, simukuona kuti khamuli lakuzungulilani ndipo likukupanikizani?” 46 Koma Yesu anati: “Munthu wina wandigwila. Ndadziwa cifukwa mphamvu yatuluka mwa ine.” 47 Mayiyo ataona kuti wadziwika, anapita kwa Yesu n’kugwada pamaso pake akunjenjemela. Ndipo anafotokoza pamaso pa anthu onsewo cifukwa cake anamugwila, komanso mmene anacilila nthawi yomweyo. 48 Koma Yesu anauza mayiyo kuti: “Mwanawe, cikhulupililo cako cakucilitsa. Pita mu mtendele.”
49 Ali mkati molankhula, kunabwela mthenga wocokela kunyumba ya mtsogoleli wa sunagoge uja. Iye anati: “Mwana wanu wamwalila. Musamuvutitse Mphunzitsiyu.” 50 Yesu atamva zimenezi, anauza Yairo kuti: “Usacite mantha. Ungokhala ndi cikhulupililo ndipo mwana wako akhalanso ndi moyo.”* 51 Atafika kunyumbako, iye sanalole aliyense kulowa naye, kupatulapo Petulo, Yohane, Yakobo, komanso tate ndi mayi a mtsikanayo. 52 Koma anthu onse anali kulila ndi kudziguguda pa cifuwa mwacisoni kaamba ka mwanayo. Conco iye anati: “Tontholani, cifukwa mwanayu sanamwalile koma wagona.” 53 Anthuwo atamva zimenezi, anayamba kumuseka monyodola cifukwa anadziwa kuti mwanayo wamwaliladi. 54 Koma Yesu anamugwila dzanja n’kumuitana kuti: “Mwanawe, uka!” 55 Zitatelo, mzimu* wa mtsikanayo unabwelela mwa iye, ndipo nthawi yomweyo anauka. Kenako Yesu anawauza kuti am’patse cakudya mtsikanayo. 56 Makolo a mtsikanayo anakondwela kwambili, koma iye anawauza kuti asauzeko aliyense zimene zinacitikazo.