Kwa Aefeso
3 Cotelo, ine Paulo, ndili m’ndende cifukwa ndili kumbali ya Khristu Yesu komanso cifukwa cothandiza inu, anthu a mitundu ina—. 2 Ndithudi, munamva kuti ndinalandila udindo wokuthandizani kuti mupindule ndi cisomo ca Mulungu, 3 ndiponso kuti anandibvumbulila cinsinsi copatulika, malinga ndi zimene ndinalemba mwacidule m’mbuyomu. 4 Conco mukawelenga izi, mudzatha kuzindikila kuti ndimacimvetsa bwino cinsinsi copatulika conena za Khristu. 5 M’mibadwo ya m’mbuyo, cinsinsi cimeneci sicinabvumbulidwe kwa ana a anthu mmene Mulungu wacibvumbulila pano kwa atumwi ndi aneneli ake oyela kudzela mwa mzimu. 6 Cinsinsi cimeneci n’cakuti anthu a mitundu ina amene ali mu mgwilizano ndi Khristu Yesu, adzalandile colowa cimene Khristu adzalandile, ndipo adzakhala mbali ya thupi. Iwo adzalandilanso zinthu zimene Mulungu watilonjeza cifukwa ca uthenga wabwino. 7 Ndinakhala mtumiki wa zimenezi malinga ndi mphatso yaulele ya cisomo ca Mulungu, imene anandipatsa kudzela mu mphamvu yake.
8 Cisomo cimeneci cinaonetsedwa kwa ine munthu wamng’ono pondiyelekezela ndi wamng’ono kwambili pa oyela onse. Anandicitila cisomo cimeneci kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa anthu a mitundu ina wonena za cuma copanda polekezela ca Khristu, 9 ndiponso kuti ndithandize aliyense kuona mmene cinsinsi copatulikaco cikuyendetsedwela. Kwa zaka zambili Mulungu amene analenga zinthu zonse, wakhala akubisa cinsinsici. 10 Zinatelo kuti kupitila mumpingo, maboma ndi maulamulilo amene ali m’malo akumwamba, tsopano adziwe mbali zosiyana-siyana za nzelu za Mulungu. 11 Izi n’zogwilizana ndi colinga camuyaya cimene iye anakhala naco cokhudza Khristu, yemwe ndi Yesu Ambuye wathu. 12 Kudzela mwa iye, tili ndi ufulu wa kulankhula umenewu, ndiponso timatha kufika kwa Mulungu mosabvuta komanso mwa cidalilo, popeza timakhulupilila Yesu. 13 Cotelo ndikukupemphani kuti musabwelele m’mbuyo poona masautso amene ndikukumana nao cifukwa ca inu, pakuti masautsowa adzakubweletselani ulemelelo.
14 Pa cifukwa cimeneci ndikugwada kwa Atate, 15 amene amapangitsa banja lililonse kumwamba ndi padziko lapansi kuti likhale ndi dzina. 16 Ndikupempha kuti Mulungu amene ali ndi ulemelelo waukulu, akuloleni kuti munthu wanu wamkati akhale wamphamvu posewenzetsa mphamvu imene mzimu wake umapeleka. 17 Ndikupemphanso kuti mwa cikhulupililo canu, m’mitima yanu mukhale Khristu komanso cikondi. Muzike mizu ndiponso mukhale okhazikika pamaziko ake, 18 n’colinga coti inu limodzi ndi oyela onse muthe kumvetsa bwino mulifupi, mulitali, kukwela, ndi kuzama kwa coonadi, 19 komanso kuti mudziwe cikondi ca Khristu cimene cimaposa kudziwa zinthu, kuti mudzazidwe ndi makhalidwe onse amene Mulungu amapeleka.
20 Tsopano kwa iye amene angathe kucita zazikulu kwambili kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza, malinga ndi mphamvu yake imene ikugwila nchito mwa ife, 21 kwa iye kukhale ulemelelo kudzela ku mpingo komanso kupitila mwa Khristu Yesu, kumibadwo yonse mpaka muyaya. Ameni.