Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
6 Tsiku lina pa Sabata, Yesu anali kudutsa m’minda ya tiligu, ndipo ophunzila ake anali kubudula ngala za tiligu, kuzifilikita m’manja mwawo n’kumadya. 2 Afarisi ena ataona izi anati: “N’cifukwa ciyani mukucita zosaloleka pa Sabata?” 3 Koma Yesu anawayankha kuti: “Kodi simunawelengepo zimene Davide anacita pamene iye ndi amuna omwe anali naye anamva njala? 4 Kodi si paja analowa m’nyumba ya Mulungu n’kulandila mitanda ya mkate wacionetselo ndipo anadya n’kupatsako amuna amene anali naye, umene sikunali kololeka munthu aliyense kudya koma ansembe okha?” 5 Kenako anawauza kuti: “Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa Sabata.”
6 Tsiku linanso pa Sabata, iye analowa m’sunagoge n’kuyamba kuphunzitsa. Ndipo mmenemo munali munthu wina wopuwala* dzanja lamanja. 7 Tsopano alembi ndi Afarisi anali kumuyang’anitsitsa Yesu kuti aone ngati amucilitse munthuyo pa Sabata. Colinga cawo cinali cakuti amuimbe mlandu. 8 Koma iye anadziwa maganizo awo. Conco anauza munthu wopuwala* dzanjayo kuti: “Nyamuka, dzaimilile pakatipa.” Munthuyo ananyamuka n’kubwela pamenepo. 9 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Ndikufunseni funso amunanu. Kodi cololeka n’citi pa Sabata, kucita cabwino kapena coipa? Kupulumutsa moyo kapena kuupha?” 10 Yesu atawayang’ana onsewo, anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi, ndipo linakhala bwino. 11 Koma iwo anakwiya koopsa, ndipo anayamba kukambilana zimene angamucite Yesu.
12 Tsiku lina Yesu anapita ku phili kukapemphela, ndipo anapemphela kwa Mulungu usiku wonse. 13 Kutaca anaitana ophunzila ake, ndipo anasankhapo ophunzila 12, amenenso anawacha atumwi. 14 Anasankha Simoni, amene anamupatsanso dzina lakuti Petulo, Andireya m’bale wake, Yakobo, Yohane, Filipo, Batulomeyo, 15 Mateyo, Thomasi, Yakobo mwana wa Alifeyo, Simoni wochedwa “wokangalika,” 16 Yudasi mwana wa Yakobo, komanso Yudasi Isikariyoti, amene anadzapeleka Yesu.
17 Ndiyeno anatsika nawo n’kuimilila pa malo afulati. Panalinso khamu lalikulu la ophunzila ake, komanso cigulu ca anthu ocokela ku Yudeya konse, ku Yerusalemu konse, komanso a kumbali kwa nyanja ya ku Turo ndi ku Sidoni. Anthu onsewo anabwela kudzamumvetsela komanso kuti adzacilitsidwe matenda awo. 18 Ngakhale amene anali kuvutitsidwa ndi mizimu yonyansa anacilitsidwa. 19 Ndipo khamu lonselo linali kufuna kumukhudza cifukwa mphamvu zinali kutuluka mwa iye, moti anthu onsewo anali kucila.
20 Ndiyeno iye atayang’ana ophunzila ake, anayamba kukamba kuti:
“Ndinu acimwemwe inu osauka, cifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wanu.
21 “Ndinu acimwemwe inu anjala palipano, cifukwa mudzakhuta.
“Ndinu acimwemwe inu amene mukulila palipano, cifukwa mudzaseka.
22 “Ndinu acimwemwe anthu akamadana nanu, akamakusalani, akamakunyozani, komanso akamaipitsa* dzina lanu cifukwa ca Mwana wa munthu. 23 Zotelezi zikakucitikilani, kondwelani ndipo lumphani mwacimwemwe, cifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, popeza zimenezi n’zimene makolo awo akale anali kucitila aneneli.
24 “Koma tsoka kwa inu olemela, cifukwa mwalandililatu zonse zokusangalatsani.
25 “Tsoka kwa inu okhuta palipano, cifukwa mudzamva njala.
“Tsoka kwa inu amene mukuseka palipano, cifukwa mudzamva cisoni ndipo mudzalila.
26 “Muli ndi tsoka inu amene anthu onse amakukambilani zabwino, cifukwa n’zimene makolo awo akale anacitila aneneli onyenga.
27 “Koma inu amene mukumvetsela ndikukuuzani kuti: Pitilizani kukonda adani anu, kucitila zabwino anthu odana nanu, 28 kudalitsa amene amakutembelelani, komanso kupemphelela amene amakunyozani. 29 Munthu amene wakumenya ku tsaya limodzi, mupatsenso linalo. Ndipo munthu amene wakulanda covala cako cakunja, usamuletse kutenganso covala camkati. 30 Munthu aliyense akakupempha cinthu mupatse, ndipo munthu amene wakulanda zinthu zako usamuuze kuti akubwezele.
31 “Komanso zimene mumafuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.
32 “Ngati mumakonda anthu okhawo amene amakukondani, kodi mudzapeza phindu lanji? Pakuti ngakhale ocimwa amakonda anthu amene amawakonda. 33 Ndipo ngati mumacitila zabwino anthu okhawo amene amakucitilani zabwino, kodi mudzapeza phindu lanji? Pakuti ngakhale ocimwa amacita cimodzimodzi. 34 Komanso ngati mumabweleketsa* anthu okhawo amene muyembekezela kuti angakubwezeleni, kodi pali phindu lanji? Pakuti ngakhale ocimwa amabweleketsa ocimwa anzawo kuti adzawabwezele. 35 Mosiyana ndi amenewo, inuyo pitilizani kukonda adani anu ndi kucita zabwino, komanso kubweleketsa popanda kuyembekezela kanthu. Mukatelo, mudzalandila mphoto yaikulu, ndipo mudzakhala ana a Wapamwambamwamba, cifukwa iye ndi wokoma mtima kwa osayamikila ndi oipa. 36 Pitilizani kukhala acifundo monga Atate wanu amenenso ndi wacifundo.
37 “Komanso, lekani kuweluza ena, ndipo inunso simudzaweluzidwa. Lekani kutsutsa ena, ndipo inunso simudzatsutsidwa. Pitilizani kukhululukila ena,* ndipo inunso mudzakhululukidwa.* 38 Khalani opatsa, ndipo inunso anthu adzakupatsani. Iwo adzakukhuthulilani muyeso wabwino pa malaya anu, wosindilika, wokhuchumuka, komanso wosefukila. Pakuti muyeso umene mukupimila ena, inunso adzakupimilani womwewo.”
39 Ndiyeno anawauzanso fanizo lakuti: “Munthu wakhungu sangatsogolele wakhungu mnzake, angatelo ngati? Ngati angatelo, onse adzagwela m’dzenje, si conco? 40 Wophunzila saposa mphunzitsi wake, koma munthu aliyense wophunzitsidwa bwino adzafanana ndi mphunzitsi wake. 41 Nanga n’cifukwa ciyani ukuyang’ana kacitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaona mtanda wa mtenje wa nyumba umene uli m’diso lako? 42 Ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘M’bale, leka ndikucotse kacitsotso kamene kali m’diso lako,’ pamene iwe sukuona mtanda wa mtenje wa nyumba umene uli m’diso lako? Wonyenga iwe! Coyamba, cotsa mtanda wa nyumba umene uli m’diso lakowo. Ukatelo, udzatha kuona bwinobwino mmene ungacotsele kacitsotso kamene kali m’diso la m’bale wako.
43 “Kulibe mtengo wabwino umene umabala zipatso zoipa, ndipo kulibe mtengo woipa umene umabala zipatso zabwino. 44 Pakuti mtengo uliwonse umadziwika ndi zipatso zake. Mwacitsanzo, anthu sathyola nkhuyu mu mtengo wa minga, kapena kudula mphesa pa citsamba ca minga. 45 Munthu wabwino amatulutsa zabwino m’cuma cabwino ca mumtima mwake, koma munthu woipa amatulutsa zoipa m’cuma cake coipa. Pakuti pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima.
46 “Nanga n’cifukwa ciyani mumandichula kuti ‘Ambuye! Ambuye!’ koma osacita zimene ndimanena? 47 Aliyense wobwela kwa ine ndi kumvetsela mawu anga komanso kuwacita, ndikuuzani amene amafanana naye: 48 Iye ali ngati munthu amene pomanga nyumba, anakumba mozama kwambili n’kuyala maziko pa thanthwe. Mtsinje utasefukila, madzi anawomba nyumbayo. Koma sinagwedezeke cifukwa inali yomangidwa bwino. 49 Koma munthu amene amamva mawu osacitapo kanthu, ali ngati munthu amene anamanga nyumba yopanda maziko. Madzi a mtsinje ataiwomba, nyumbayo inagwa nthawi yomweyo, ndipo kuwonongeka kwake kunali kwakukulu.”