Kwa Afilipi
3 Pomaliza abale anga, pitilizani kusangalala mwa Ambuye. Kulemba zinthu zimene ndinakulembelani kale si bvuto kwa ine, koma ndi citetezo kwa inu.
2 Cenjelani ndi agalu, cenjelani ndi anthu amene amabvulaza anzao, komanso cenjelani ndi anthu amene amacita mdulidwe. 3 Ife amene tikucita utumiki wopatulika motsogoleledwa ndi mzimu wa Mulungu, tinacita mdulidwe weniweni. Timadzitamandila mwa Khristu Yesu ndipo sitidalila zinthu za kuthupi. 4 Ngakhale n’telo, kuposa wina aliyense, ine ndili ndi zifukwa zodalila zinthu za kuthupi.
Ngati alipo wina amene akuganiza kuti ali ndi zifukwa zodalila zinthu za kuthupi, ine ndikumuposa ameneyo. Ndikutelo cifukwa 5 ndinadulidwa pa tsiku la 8, ndine wa mtundu wa Isiraeli, wa fuko la Benjamini, komanso ndine Mheberi wobadwa kwa Aheberi. Pa za malamulo, ndine Mfarisi. 6 Pa nkhani ya kudzipeleka ndinali kuzunza mpingo. Pa nkhani yocita cilungamo potsatila malamulo, ndinaonetsa kuti ndilibe cifukwa condinenezela. 7 Ngakhale n’telo, zinthu zimene zinali zaphindu kwa ine ndikuziona kuti ndi zopanda phindu* cifukwa ca Khristu. 8 Kuonjezela pamenepo, ndimaona kuti zinthu zonse ndi zopanda phindu cifukwa ca cidziwitso cimene ndakhala naco pa Khristu Yesu Ambuye wanga, cimene ndi cinthu camtengo wapatali kwa ine. Cifukwa ca iye, ndinalolela kutaya zinthu zonse, ndipo ndimaziona ngati mulu wa zinyalala. Ndinatelo kuti ndikhale pa ubwenzi weniweni ndi Khristu, 9 komanso kuti ndikhale mu mgwilizano ndi iye. Komabe sikuti ndine wolungama cifukwa cakuti ndikucita zonse motsatila Cilamulo, koma cifukwa cakuti ndimakhulupilila Khristu. Cilungamoci n’cocokela kwa Mulungu, ndipo cimabwela cifukwa ca cikhulupililo. 10 Cimene ndikufuna n’cakuti ndimudziwe komanso kuti ndidziwe mphamvu za amene anamuukitsa kwa akufa. Ndikulolela kuti ndibvutike ngati mmene iye anabvutikila, ngakhale kufa ngati mmene iye anafela. 11 Ndikuyesetsa kucita zimenezi kuti ngati n’kotheka ndikapeze mwai wodzauka kwa akufa pa kuuka koyamba.
12 Sindikunena kuti ndalandila kale mphotoyo ai, kapena kuti ndakhala kale wangwilo ainso. Koma ndikuyesetsabe kuti ndikapeze mphoto cifukwa ndikudziwa kuti ndi cimene Khristu Yesu anandisankhila. 13 Abale, ine sindikudziona ngati ndalandila kale mphotoyo ai. Koma pali cimodzi cokha cimene ndikucita: Ndikuiwala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo. 14 Ndikuyesetsa kuti ndikapate mphoto ya ciitano ca Mulungu copita kumwamba, codzela mwa Khristu Yesu. 15 Conco, tiyeni tonse amene ndife acikulile* ku uzimu tikhale ndi maganizo amenewa. Ndipo ngati maganizo anu ndi osiyana ndi amenewa pambali ina iliyonse, Mulungu adzakuululilani maganizo oyenelawo. 16 Ndiye kaya tapita patsogolo motani, tiyeni tisaleke kupita patsogolo mwa kupitiliza kucita zimene tikucitazo.
17 Abale, nonsenu muziyesetsa kutengela citsanzo canga, ndipo muzionetsetsa amene akucita zinthu motengela citsanzo cimene tinakupatsani. 18 Pali anthu ambili amene akucita zinthu ngati adani a mtengo wozunzikilapo* wa Khristu. Kale ndinali kuwachula kawili-kawili, koma pano ndimawachula ndikugwetsa misozi. 19 Mapeto a anthu amenewa ndi cionongeko, ndipo mulungu wao ndi mimba zao. Iwo amanyadila zinthu zocititsa manyazi, ndipo mtima wao uli pa zinthu za dziko lapansi. 20 Koma ife ndife nzika za kumwamba, ndipo tikuyembekezela mwacidwi mpulumutsi wocokela kumeneko yemwe ndi Ambuye Yesu Khristu. 21 Iye adzasintha thupi lonyozekali kuti lidzafanane ndi thupi lake laulemelelo. Adzatelo pogwilitsa nchito mphamvu zake zazikulu zimene zimamuthandiza kugonjetsa zinthu zonse kuti zikhale pansi pake.