Kwa Aefeso
2 Kuonjezela apo, Mulungu anapangitsa kuti mukhale amoyo ngakhale kuti munali akufa cifukwa ca zolakwa zanu komanso macimo anu. 2 Pa nthawi ina munali kuyenda m’zimenezo malinga ndi nthawi* ya m’dzikoli, pomvela wolamulila wa mpweya umene umalamulila zocita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe kameneka, tsopano kakugwila nchito mwa ana osamvela. 3 Inde pa nthawi ina pamene tinali kukhala pakati pao, tinali kucita zinthu motsatila zilakolako za thupi lathu. Tinali kucita zofuna za thupi ndi maganizo athu, ndipo mwacibadwa tinali ana oyenela kulandila mkwiyo wa Mulungu, mofanana ndi ena onse. 4 Koma popeza Mulungu ndi wacifundo cacikulu, komanso cifukwa ca cikondi cake cacikulu cimene anationetsa, 5 anapangitsa kuti tikhale amoyo limodzi ndi Khristu, ngakhale kuti tinali akufa cifukwa ca macimo athu. Ndipotu inu mwapulumutsidwa cifukwa ca cisomo cake. 6 Kuonjezela apo, Mulungu anatiukitsa limodzi, ndi kutikhazika limodzi m’malo akumwamba mu mgwilizano ndi Khristu Yesu. 7 Anatelo kuti mu nthawi zimene zikubwela, iye adzationetse cuma copambana ca cisomo cake m’cigwilizano ndi Khristu Yesu.
8 Mwa cisomo cimeneci, inu mwapulumutsidwa kudzela m’cikhulupililo. Sikuti zimenezi zatheka cifukwa ca khama lanu ayi, koma ndi mphatso ya Mulungu. 9 Zimenezi sizinatheke cifukwa ca nchito, kuti munthu asakhale ndi cifukwa codzitamandila. 10 Ife ndife nchito ya manja a Mulungu. Iye ndi amene anatilenga, ndipo tili mu mgwilizano ndi Khristu Yesu kuti ticite nchito zabwino, zimene Mulungu anakonzelatu kuti tiyendemo.
11 Conco, muzikumbukila kuti panthawi ina, inunso munali anthu a mitundu ina. Anthu “odulidwa” anali kukuchulani kuti anthu “osadulidwa.” Mdulidwe umenewu umacitika pa thupi ndi manja a anthu. 12 Panthawi imeneyo Khristu simunali kumudziwa. Munali otalikilana ndi mtundu wa Isiraeli, ndipo simunali nao m’zipangano za lonjezo. Munalibe ciyembekezo, ndipo Mulungu simunali kumudziwa m’dzikoli. 13 Koma tsopano popeza muli mu mgwilizano ndi Khristu Yesu, inu amene pa nthawi ina munali kutali, mwabwela pafupi cifukwa ca magazi ake. 14 Pakuti iye ndiye mtendele wathu, iye amene anaphatikiza magulu awili aja kukhala gulu limodzi, n’kugwetsa cipupa cowalekanitsa comwe cinali pakati pao. 15 Ndi thupi lake anacotsapo cinthu coyambitsa cidani comwe ndi Cilamulo, cokhala ndi malamulo komanso malangizo. Anacicotsapo kuti magulu awili omwe ali mu mgwilizano ndi iye akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kuti akhazikitse mtendele. 16 Kuonjezela apo anatelo kuti kudzela mwa mtengo wozunzikilapo, ayanjanitse magulu awili a anthuwo kwa Mulungu, kutinso anthuwo akhale thupi limodzi cifukwa anali ataphelatu cidanico kudzela mwa iye mwini. 17 Cotelo iye anabwela kudzalengeza uthenga wabwino wa mtendele kwa inu amene munali kutali. Analengezanso za mtendele kwa amene anali pafupi. 18 Anatelo cifukwa kudzela mwa iye, ife, magulu onse awili, tingathe kufika kwa Atate mosabvuta kudzela mwa mzimu umodzi.
19 Conco simulinso anthu osadziwika kapena alendo, koma mofanana ndi oyelawo inunso ndinu nzika, ndipo ndinu a m’banja la Mulungu. 20 Mwamangidwa pamaziko a atumwi ndi aneneli, ndipo Khristu Yesu ndiye mwala wapakona wa mazikowo. 21 Mwa iye, nyumba yonse popeza ndi yolumikizika bwino, ikukula n’kukhala kacisi woyela wa Yehova. 22 Inunso mukumangidwa pamodzi mu mgwilizano ndi iye kuti mukhale malo oti Mulungu akhalemo mwa mzimu.