Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Yohane
6 Pambuyo pa izi, Yesu anawoloka nyanja ya Galileya, kapena kuti nyanja ya Tiberiyo. 2 Ndipo khamu la anthu linali kumutsatila cifukwa linali kuona zozizwitsa* zimene anali kucita pocilitsa anthu. 3 Conco Yesu anakwela m’phili, ndipo anakhala pansi mmenemo pamodzi ndi ophunzila ake. 4 Tsopano cikondwelelo ca Ayuda ca Pasika cinali citayandikila. 5 Yesu atakweza maso ake, n’kuona khamu lalikulu la anthu likubwela kwa iye, anafunsa Filipo kuti: “N’kuti kumene tingakagule mkate kuti anthuwa adye?” 6 Koma iye ananena izi pofuna kumuyesa, cifukwa Yesu anali kudziwa zimene anafuna kucita. 7 Filipo anamuyankha kuti: “Ndalama zokwana madinari 200 sizingakwanile kugula mkate woti aliyense adyeko ngakhale pang’ono.” 8 Mmodzi wa ophunzila ake Andireya, m’bale wake wa Simoni Petulo, anamuuza kuti: 9 “Pano pali kamnyamata komwe kali ndi mitanda isanu ya mkate wabalele ndi tinsomba tiwili. Koma kodi zimenezi zingakwanile khamu lonseli?”
10 Yesu anakamba kuti: “Auzeni anthuwo akhale pansi.” Pamalopo panali udzu wambili. Conco amuna pafupifupi 5,000 anakhala pansi. 11 Yesu anatenga mkatewo n’kuyamika, kenako anaupeleka kwa anthu amene anakhala pansi aja. Iye anacitanso cimodzimodzi ndi tunsomba tuja moti anthuwo anadya mmene anafunila. 12 Anthuwo atadya n’kukhuta, iye anauza ophunzila ake kuti: “Sonkhanitsani zonse zotsala kuti pasawonongeke ciliconse.” 13 Conco iwo anazisonkhanitsa pamodzi ndipo zinadzala matadza 12. Izi ndi zimene zinatsalako pambuyo pakuti anthu aja adya mkate kucokela ku mitanda isanu ya balele n’kulephela kuitsiliza.
14 Anthuwo ataona cozizwitsa* cimene anacitaci anayamba kunena kuti: “Zoonadi uyu ndiye mneneli uja amene anati adzabwela padziko.” 15 Ndiyeno Yesu atadziwa kuti anthuwo akufuna kudzamugwila kuti amulonge ufumu, anacoka n’kupitanso ku phili kwayekha.
16 Ndiyeno kutayamba kuda, ophunzila ake anapita ku nyanja. 17 Iwo anakwela bwato n’kuwoloka nyanjayo kupita ku Kaperenao. Apa n’kuti kwadelatu, ndipo Yesu anali asanabwelebe kwa iwo. 18 Komanso nyanjayo inayamba kuwinduka cifukwa cimphepo camphamvu cinali kuwomba. 19 Iwo atapalasa makilomita asanu kapena 6,* anaona Yesu akuyenda pa nyanja akuyandikila bwatolo, ndipo iwo anacita mantha. 20 Koma iye anawauza kuti: “Ndine, musacite mantha!” 21 Ndiyeno iwo anamulola kukwela m’bwatolo, ndipo posapita nthawi bwatolo linafika kumtunda kumene anali kupita.
22 Tsiku lotsatila, khamu limene linali kutsidya lina la nyanja linazindikila kuti bwato lokhalo laling’ono limene linali m’mbali mwa nyanja palibenso. Ophunzila a Yesu anakwela bwatolo n’kupita popanda Yesu. 23 Koma mabwato amene anacokela ku Tiberiyo anafika pafupi ndi malo amene anthuwo anadyela mkate uja Ambuye atayamika. 24 Conco khamu la anthulo litaona kuti Yesu ndi ophunzila ake kulibe kumeneko, linakwela mabwato awo n’kupita ku Kaperenao kukafunafuna Yesu.
25 Atamupeza kutsidya lina la nyanja anamufunsa kuti: “Mphunzitsi,* mwafika nthawi yanji kuno?” 26 Yesu anawayankha kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mukundifunafuna osati cifukwa ca zozizwitsa* zimene munaona, koma cifukwa ca mkate umene munadya ndi kukhuta. 27 Musamagwile nchito kuti mungopeza cakudya cimene cimawonongeka, koma kuti mupeze cakudya cokhalitsa, comwe cimabweletsa moyo wosatha, cimene Mwana wa munthu adzakupatsani. Pakuti Atate Mulungu mwiniyo waika cidindo pa Mwanayo comuvomeleza.”
28 Conco anthuwo anamufunsa kuti: “Kodi tiyenela kutani kuti tizicita zimene Mulungu amafuna?” 29 Yesu anawayankha kuti: “Mulungu amafuna kuti muzionetsa cikhulupililo mwa iye amene anamutuma.” 30 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Kodi mucita cozizwitsa* cotani kuti ticione ndi kukukhulupililani? Mucita nchito yotani? 31 Makolo athu akale, anadya mana m‘cipululu monga mmene Malemba amanenela kuti: ‘Iye anawapatsa cakudya cocokela kumwamba kuti adye.’” 32 Kenako Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mose sanakupatseni cakudya cocokela kumwamba, koma Atate wanga amakupatsani cakudya ceniceni cocokela kumwamba. 33 Cifukwa cakudya cimene Mulungu wapeleka, ndi iye amene watsika kucokela kumwamba n’kupeleka moyo ku dzikoli.” 34 Conco iwo anamuuza kuti: “Ambuye muzitipatsa cakudya cimeneci nthawi zonse.”
35 Yesu anawauza kuti: “Ine ndine cakudya copatsa moyo. Aliyense wobwela kwa ine sadzamva njala ngakhale pang’ono, ndipo aliyense wokhulupilila mwa ine sadzamva ludzu ayi. 36 Koma monga ndinakuuzilani, inu simukhulupililabe ngakhale kuti mwandiona. 37 Onse amene Atate andipatsa adzabwela kwa ine, ndipo amene wabwela kwa ine sindidzamupitikitsa. 38 Pakuti ndinabwela kucokela kumwamba kudzacita cifunilo ca iye amene anandituma, osati canga ayi. 39 Cifunilo ca amene anandituma n’cakuti, ndisataye ngakhale mmodzi mwa onse amene iye anandipatsa, koma kuti ndikawaukitse pa tsiku lothela. 40 Pakuti cifunilo ca Atate wanga n’cakuti aliyense wovomeleza Mwanayo ndi kukhulupilila mwa iye akapeze moyo wosatha, ndipo ine ndidzamuukitsa pa tsiku lothela.”
41 Ndiyeno Ayudawo anayamba kung’ung’udza za iye cifukwa anakamba kuti: “Ine ndine cakudya cocokela kumwamba.” 42 Iwo anayamba kunena kuti: “Kodi uyu si Yesu mwana wa Yosefe, amene atate ake ndi amayi ake timawadziwa? Nanga bwanji tsopano akunena kuti, ‘Ndinacokela kumwamba’?” 43 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Lekani kung’ung’udza pakati panu. 44 Palibe amene angabwele kwa ine ngati Atate amene anandituma sanamukopele* kwa ine, ndipo ine ndidzamuukitsa pa tsiku lothela. 45 Aneneli analemba kuti: ‘Onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.’ Aliyense amene wamvetsela kwa Atate ndipo waphunzila, amabwela kwa ine. 46 Palibe munthu amene anaonapo Atate, kupatulapo iye amene anacokela kwa Mulungu, ameneyu ndiye anaonapo Atate. 47 Ndithudi ndikukuuzani, aliyense wokhulupilila adzapeza moyo wosatha.
48 “Ine ndine cakudya copatsa moyo. 49 Makolo anu akale anadya mana m’cipululu koma anafabe. 50 Ici ndi cakudya cocokela kumwamba, coti aliyense adyeko ndipo asafe. 51 Ine ndine cakudya copatsa moyo cocokela kumwamba. Ngati wina angadye cakudyaci adzakhala ndi moyo kwamuyaya. Ndipo cakudya cimene ndidzapeleka, ndi mnofu wanga kuti anthu* akapeze moyo.”
52 Kenako Ayudawo anayamba kukangana akumati: “Kodi zingatheke bwanji munthu uyu kutipatsa mnofu wake kuti tidye?” 53 Conco Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, ngati simungadye mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, simudzapeza moyo.* 54 Aliyense amene amadya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga adzapeza moyo wosatha, ndipo ndidzamuukitsa pa tsiku lothela. 55 Cifukwa mnofu wanga ndi cakudya ceniceni, ndipo magazi anga ndi cakumwa ceniceni. 56 Aliyense amene amadya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga, amakhalabe wogwilizana ndi ine ndipo inenso ndimakhala wogwilizana naye. 57 Atate wamoyo anandituma ndipo ndili ndi moyo cifukwa ca Atatewo. Conco nayenso amene amadya mnofu wanga adzakhala ndi moyo cifukwa ca ine. 58 Ici ndi cakudya cocokela kumwamba. Sicili ngati cakudya cimene makolo anu akale anadya koma n’kufa ndithu. Aliyense wakudya cakudyaci adzakhala ndi moyo kwamuyaya.” 59 Iye anakamba zimenezi pamene anali kuphunzitsa m’sunagoge* ku Kaperenao.
60 Ambili mwa ophunzila ake atamva izi anati: “Mawu awa ndi okhumudwitsa. Ndani angafune kumvetsela zimenezi?” 61 Koma Yesu atadziwa kuti ophunzila ake anali kung’ung’udza cifukwa ca zimene iye anakamba, anawafunsa kuti: “Kodi izi zakupunthwitsani? 62 Nanga bwanji mukadzaona Mwana wa munthu akukwela kubwelela kumene anali poyamba? 63 Mzimu ndiwo umapatsa moyo koma mnofu ulibe nchito ngakhale pang’ono. Mawu amene ndakuuzani ndi mzimu ndiponso ndi moyo. 64 Koma pali ena a inu amene simukhulupilila.” Cifukwa Yesu anadziwa kucokela paciyambi amene sanamukhulupilile, komanso munthu amene adzamupeleka. 65 Iye anapitiliza kuti: “N’cifukwa cake ndinakuuzani kuti, palibe amene angabwele kwa ine ngati Atate sanamulole.”
66 Kaamba ka ici, ambili mwa ophunzila ake anabwelela ku zinthu zakumbuyo, ndipo analeka kuyenda naye. 67 Conco Yesu anafunsa atumwi ake 12 aja kuti: “Kodi inunso mufuna kupita?” 68 Simoni Petulo anamuyankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu a moyo wosatha. 69 Ife takhulupilila ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyela wa Mulungu.” 70 Yesu anawauza kuti: “Ndinakusankhani 12, si conco? Koma mmodzi wa inu ndi woneneza.”* 71 Apa iye anali kukamba za Yudasi mwana wa Simoni Isikariyoti, cifukwa ameneyu anali kudzamupeleka, ngakhale kuti anali mmodzi wa atumwi 12 amenewo.