Kwa Aefeso
1 Ine Paulo, amene ndinakhala mtumwi wa Khristu Yesu malinga ndi cifunilo ca Mulungu, ndikulembela oyela amene ali ku Efeso, amene ali mu mgwilizano ndi Khristu Yesu, amenenso ndi okhulupilika kuti:
2 Cisomo komanso mtendele wa Mulungu Atate wathu, ndi wa Ambuye Yesu Khristu zikhale nanu.
3 Atamandike Mulungu komanso Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, cifukwa watidalitsa ndi dalitso lililonse lauzimu m’malo akumwamba. Wacita zimenezi cifukwa cakuti tili mu mgwilizano ndi Khristu. 4 Iye anatisankha dziko lisanakhazikitsidwe* kuti tikhale mu mgwilizano ndi Khristu. Anatelo kuti tizionetsa cikondi, komanso kuti tikhale oyela ndiponso opanda cilema pamaso pake. 5 Popeza anatisankhilatu kuti adzatitenga n’kukhala ana ake kudzela mwa Yesu Khristu, mogwilizana ndi zimene zinamusangalatsa komanso zimene anafuna. 6 Anatelo kuti iye atamandike cifukwa ca cisomo caulemelelo cimene anaticitila kudzela mwa mwana wake wokondedwa. 7 Mwa Mwana wakeyo tinamasulidwa ndi dipo* la magazi ake. Inde, takhululukidwa macimo athu mwa cisomo cake.
8 Iye anaonetsetsa kuti cisomo cimeneci casefukila kwa ife potithandiza kuti tikhale anzelu komanso ozindikila, 9 potiululila cinsinsi cake copatulika cokhudza cifunilo cake. Cinsinsico n’cogwilizana ndi zimene zimamukondweletsa ndiponso cifunilo cake, 10 cakuti pakhale dongosolo pa nthawi imene anaikilatu. Dongosolo limenelo ndi kusonkhanitsa zinthu zonse pamodzi mwa Khristu, za kumwamba ndi za padziko lapansi. Inde, mwa iye 11 amene tili naye mu mgwilizano ndipo tidzalandila naye limodzi colowa. Pakuti tinasankhidwa pasadakhale mogwilizana ndi colinga ca iye amene amacita zinthu zonse malinga ndi cifunilo cake. 12 Anatelo kuti ife amene ndife oyamba kukhala ndi ciyembekezo mwa Khristu titamande Mulungu cifukwa iye ndi wamkulu. 13 Inunso munakhala ndi ciyembekezo mwa iye mutamva mau a coonadi, inde uthenga wabwino wa cipulumutso canu. Mutakhulupilila, Mulungu anagwilitsa nchito mzimu woyela umene analonjeza kuti akuikeni cidindo, ndipo anasewenzetsa Khristu pocita zimenezi. 14 Mzimu woyela umenewo ndi cikole cotitsimikizila kuti tidzalandila colowa cathu. Mulungu anatelo n’colinga cakuti anthu, amene ndi cuma cake, akamasulidwe kupyolela m’dipo. Izi zidzacititsa kuti citamando ndi ulemelelo wonse zipite kwa iye.
15 Pa cifukwa cimeneci, inenso kuyambila pamene ndinamva za cikhulupililo cimene muli naco mwa Ambuye Yesu, komanso cikondi cimene mumaonetsa oyela onse, 16 sindinaleke kuyamikila Mulungu cifukwa ca inu. Ndikupitiliza kukupemphelelani, 17 kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate waulemelelo, akupatseni mzimu wa nzelu ndi wa bvumbulutso kuti mukhale ndi cidziwitso colongosoka pa iye. 18 Mulungu waunikila mitima yanu kuti muone komanso kuti mudziwe ciyembekezo cimene anakuitanilani, inde cuma caulemelelo cimene amapeleka ngati colowa kwa oyela, 19 komanso kuti mudziwe kukula kwa mphamvu zake zopambana zimene amazionetsa kwa ife okhulupilila. Mphamvu zake zazikuluzo zikuonekela m’nchito zake. 20 Iye anazigwilitsa nchito poukitsa Khristu kwa akufa n’kumukhazika kudzanja lake lamanja m’malo akumwamba. 21 Anamukweza kuposa boma lililonse, ulamulilo uliwonse, amphamvu onse, ambuye onse, ndi aliyense amene ali ndi dzina laulemu, osati m’nthawi* ino yokha, koma ngakhale imene ikubwelayo. 22 Mulungu anaikanso zinthu zonse pansi pa mapazi ake, ndipo anamuika kuti akhale mutu wa zonse zokhudzana ndi mpingo. 23 Mpingowo ndi thupi la Khristu, ndipo ndi wodzazidwa ndi Khristuyo amene amadzaza zinthu zonse mokwanila.