Kwa Aroma
7 Kodi simukudziwa abale, (pakuti ndikulankhula ndi anthu odziwa cilamulo) kuti Cilamulo cimakhala ndi mphamvu pa munthu pamene ali ndi moyo? 2 Mwacitsanzo, mkazi wokwatiwa amakhala womangidwa kwa mwamuna wake mwalamulo pamene mwamunayo ali moyo. Koma mwamuna wakeyo akamwalila, mkaziyo amamasuka ku lamulo la mwamuna wake. 3 Conco, ngati mkaziyo angakwatiwe ndi mwamuna wina mwamuna wake ali moyo, ndiye kuti wacita cigololo. Koma ngati mwamuna wake wamwalila, mkaziyo amamasuka ku lamulo la mwamuna wake. Ndipo sanacite cigololo akakwatiwa ndi mwamuna wina.
4 Conco abale anga, thupi la Khristu linakumasulani* ku Cilamulo kuti mukhale a winawake amene anaukitsidwa ndi colinga cakuti tibale zipatso kwa Mulungu. 5 Pakuti pamene tinali kukhala mogwilizana ndi matupi athu ocimwawa, Cilamulo cinacititsa kuti zilakolako za ucimo zimene tinali nazo m’matupi* mwathu zionekele. Ndipo zilakolako zimenezi zinatibweletsela imfa. 6 Koma tsopano tamasulidwa ku Cilamulo, cifukwa tafa ku Cilamulo cimene cinali kutimanga kuti tikhale akapolo m’njila yatsopano motsogoleledwa ndi mzimu, osati m’njila yakale motsogoleledwa ndi malamulo olembedwa.
7 Ndiye tinene kuti ciyani? Kodi Cilamulo ndi ucimo? Ayi ndithu! Kukamba zoona, sindikanadziwa ucimo zikanakhala kuti panalibe Cilamulo. Mwacitsanzo, sindikanadziwa za kukhumbila kwansanje ngati Cilamulo sicinanene kuti: “Usasilile mwansanje.” 8 Koma cifukwa ca lamulo, ucimo unapeza njila yondipangitsa kukhala ndi kukhumbila kwansanje kwa mtundu ulionse. Pakuti popanda Cilamulo, ucimo unalibe mphamvu. 9 Cilamulo cisanapelekedwe ndinali wamoyo. Koma Cilamulo citafika, ucimo unakhalanso wamoyo, koma ine ndinafa. 10 Ndipo lamulo limene linali kufunika kunditsogolela ku moyo, linanditsogolela ku imfa. 11 Ucimo unagwilitsa nchito lamulo limeneli pondinyengelela ndipo unandipha. 12 Conco Cilamulo pacokha n’coyela, ndipo malamulo ndi oyela, olungama ndiponso abwino.
13 Kodi izi zitanthauza kuti cinthu cabwino cinacititsa kuti ine ndife? Ayi ndithu! Ucimo ndi umene unacititsa kuti ndife. Cilamulo n’cabwino, kungoti cinacititsa kuti zidziwike bwino kuti ucimo ukucititsa kuti ndife. Conco malamulo anatithandiza kudziwa kuti ucimo ndi woipa kwambili. 14 Pakuti tikudziwa kuti Cilamulo n’cocokela kwa Mulungu,* koma ine ndine wopanda ungwilo, ndipo ndinagulitsidwa ku ucimo. 15 Sindikumvetsa zimene zimandicitikila. Cifukwa sindicita zimene ndimafuna, koma ndimacita zimene ndimadana nazo. 16 Komabe ngati ndimacita zimene sindikufuna kucita, ndiye kuti ndikuvomeleza kuti Cilamulo n’cabwino. 17 Cifukwa sindine amene ndikucita zimenezo, koma ucimo umene uli mwa ine. 18 Pakuti ndikudziwa kuti mwa ine, kutanthauza m’thupi langali, mulibe cabwino ciliconse. Cifukwa ndimafuna kucita zabwino koma sindikwanitsa kuzicita. 19 Zinthu zabwino zimene ndimafuna kucita sindizicita, koma zoipa zimene sindifuna kucita n’zimene ndimacita. 20 Conco ngati ndimacita zimene sindifuna kucita, ndiye kuti amene akucita zimenezo sindine ayi, koma ndi ucimo umene uli mwa ine.
21 Zimene zimandicitikila n’zakuti,* pamene ndikufuna kucita zabwino, zoipa zimakhala kuti zili ndi ine. 22 Ndimasangalala kwambili ndi malamulo a Mulungu mu mtima mwanga, 23 koma ndimaona lamulo lina m’thupi* langa likumenyana ndi malamulo a m’maganizo mwanga n’kundicititsa kukhala kapolo wa lamulo la ucimo limene lili m’thupi* langa. 24 Munthu womvetsa cifundo ine! Ndani angandipulumutse ku thupi ili limene likundicititsa kuti ndife? 25 Ndiyamika Mulungu cifukwa adzandipulumutsa kudzela mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Conco m’maganizo mwanga ndine kapolo wa malamulo a Mulungu, koma m’thupi mwanga ndine kapolo wa lamulo la ucimo.