Wolembedwa na Mateyo
12 Pa nthawiyo Yesu anali kudutsa m’minda ya tiligu pa Sabata. Ophunzila ake anamva njala, ndipo anayamba kuthyola ngalangala za tiligu n’kumadya. 2 Afarisi ataona izi, anamuuza kuti: “Onani! Ophunzila anu akucita zosaloleka pa Sabata.” 3 Iye anawayankha kuti: “Kodi simunaŵelenge zimene Davide anacita pamene iye na amuna amene anali naye anamva njala? 4 Kodi si paja analoŵa m’nyumba ya Mulungu na kudya mitanda ya mkate wa cionetselo, imene sikunali kololeka iye kudya kapena anthu omwe anali naye, koma ansembe okha? 5 Kapena simunaŵelenge m’Cilamulo kuti pa Sabata, ansembe m’kacisi amaphwanya lamulo la Sabata koma amakhalabe osalakwa? 6 Koma nikukuuzani kuti winawake wamkulu kuposa kacisi ali pano. 7 Komabe, mukanamvetsetsa tanthauzo la mawu akuti, ‘Nifuna cifundo osati nsembe,’ simukanaweluza anthu osalakwa. 8 Pakuti Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa Sabata.”
9 Atacoka pa malowo anapita kukaloŵa mu sunagoge wawo, 10 ndipo mmenemo munali mwamuna wina wopuwala dzanja! Cotelo iwo anafunsa Yesu kuti, “Kodi n’kololeka kucilitsa munthu pa Sabata?” Colinga cawo cinali kumupeza cifukwa. 11 Iye anawayankha kuti: “Ngati muli na nkhosa imodzi ndipo nkhosayo n’kugwela m’dzenje pa Sabata, ndani wa inu amene sangaigwile n’kuitulutsa? 12 Koma munthu ni wofunika kwambili kuposa nkhosa! Conco n’kololeka kucita cabwino pa Sabata.” 13 Ndiyeno anauza munthu uja kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi dzanjalo, ndipo linakhala bwino mofanana na linalo. 14 Koma Afarisiwo anacoka n’kupita kukamukonzela ciwembu kuti amuphe. 15 Yesu atadziŵa zimenezi, anacoka kumeneko. Anthu ambili anamutsatila, ndipo iye anawacilitsa onsewo, 16 koma anawalamula mwamphamvu kuti asamuulule. 17 Izi zinakwanilitsa mawu amene anakambidwa kupitila mwa mneneli Yesaya akuti:
18 “Taonani! Mtumiki wanga amene n’namusankha, wokondedwa wanga, amene nimakondwela naye! Nidzaika mzimu wanga pa iye, ndipo adzathandiza anthu a mitundu ina kudziŵa cilungamo ceniceni. 19 Iye sadzakangana na anthu kapena kufuula, ndipo palibe amene adzamva mawu ake m’misewu. 20 Bango lililonse lophwanyika sadzalithyola-thyola, ndipo nyale iliyonse yofuka sadzaizimitsa, mpaka atakwanitsa kubweletsa cilungamo. 21 Ndithudi, m’dzina lake mitundu ya anthu idzakhala na ciyembekezo.”
22 Ndiyeno anamubweletsela munthu wogwidwa na ciŵanda, amene anali wakhungu komanso wosalankhula. Anamucilitsa moti munthuyo anayamba kulankhula na kuona. 23 Zitatelo, khamulo linadabwa kwambili, ndipo linayamba kunena kuti: “Kodi ameneyu sangakhale Mwana uja wa Davide?” 24 Atamva izi, Afarisi anati: “Munthu uyu satulutsa ziŵanda na mphamvu zake ayi, koma na mphamvu za Belezebule,* wolamulila ziŵanda.” 25 Atadziŵa maganizo awo, Yesu anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogaŵikana umatha, ndipo mzinda uliwonse kapena nyumba iliyonse yogaŵikana, silimba. 26 Mofanana na zimenezi, ngati Satana amatulutsa Satana, ndiye kuti wagaŵikana, nanga ufumu wake ungakhalepo bwanji? 27 Kuwonjezela apo, ngati ine nimatulutsa ziŵanda na mphamvu ya Belezebule, nanga ophunzila anu amazitulutsa na mphamvu ya ndani? Ndiye cifukwa cake iwo adzakuweluzani. 28 Koma ngati nimatulutsa ziŵanda na mphamvu ya mzimu wa Mulungu, ndiye kuti Ufumu wa Mulungu wakufikanidi modzidzimutsa. 29 Kapena munthu angathyole bwanji nyumba ya munthu wamphamvu na kumulanda katundu wake asanayambe wam’manga munthu wamphamvuyo? Akamumanga m’pamene angathe kutenga zinthu m’nyumbamo. 30 Aliyense amene sali kumbali yanga akutsutsana nane, ndipo aliyense amene sakunithandiza kusonkhanitsa anthu kwa ine akuwamwaza.
31 “Pa cifukwa cimeneci, nikukuuzani kuti anthu adzakhululukidwa chimo lililonse kapena mawu onyoza alionse amene angakambe, koma wonyoza mzimu sadzakhululukidwa. 32 Mwa citsanzo, aliyense wokamba mawu onyoza Mwana wa munthu adzakhululukidwa, koma aliyense wonyoza mzimu woyela sadzakhululukidwa, kaya m’nthawi ino* kapena imene ikubwelayo.
33 “Inu mumacititsa mtengo pamodzi na zipatso zake kukhala zabwino, kapena mumacititsa mtengo pamodzi na zipatso zake kukhala zoipa, cifukwa mtengo umadziŵika na zipatso zake. 34 Ana a njoka inu, mungalankhule bwanji zinthu zabwino pamene muli oipa? Pakuti pakamwa pamalankhula zosefukila mu mtima. 35 Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino m’cuma cake cabwino, koma munthu woipa amatulutsa zinthu zoipa m’cuma cake coipa. 36 Nikukuuzani kuti pa Tsiku la Ciweluzo anthu adzayankha mlandu pa mawu alionse acabe-cabe amene amakamba; 37 Pakuti mwa mawu ako udzaweluzidwa kuti ndiwe wolungama, ndiponso mwa mawu ako udzaweluzidwa kuti ndiwe wolakwa.”
38 Ndiyeno pomuyankha, alembi na Afarisi ena anati: “Mphunzitsi, tifuna mutionetse cizindikilo.” 39 Poyankha iye anawauza kuti: “M’badwo woipa komanso wacigololo* ukufunabe cizindikilo, koma sudzapatsidwa cizindikilo ciliconse kupatulapo cizindikilo ca mneneli Yona. 40 Pakuti monga mmene Yona anakhalila m’mimba mwa cinsomba masiku atatu usana na usiku, nayenso Mwana wa munthu adzakhala mu mtima wa dziko lapansi masiku atatu usana na usiku. 41 Anthu a ku Ninive adzauka pa Tsiku la Ciweluzo pamodzi na m’badwo uwu, ndipo adzautsutsa, cifukwa analapa atamva ulaliki wa Yona. Koma onani! Winawake woposa Yona ali pano. 42 Mfumukazi ya kum’mwela idzaukitsidwa pa Tsiku la Ciweluzo pamodzi na m’badwo uwu ndipo idzautsutsa, cifukwa inacokela ku malekezelo a dziko lapansi n’kubwela kuti idzamve nzelu za Solomo. Koma onani! Winawake woposa Solomo ali pano.
43 “Mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, umadutsa m’malo opanda madzi kufuna-funa popumulila, koma supeza malo alionse. 44 Kenako umati, ‘Nibwelela m’nyumba yanga imene n’natulukamo,’ ndipo ukafika umapeza kuti m’nyumbamo mulibe aliyense, koma ni mopsela bwino komanso ni mokongoletsedwa. 45 Kenako umapita n’kukatenga mizimu ina 7 yoipa kwambili kuposa umenewo, ndipo yonse imaloŵa m’nyumbamo n’kumakhala mmenemo. Pamapeto pake, munthuyo amakhala woipa kwambili kuposa poyamba. Ni mmenenso zidzakhalila na m’badwo woipawu.”
46 Ali mkati molankhula na khamu la anthulo, abale ake na amayi ake anabwela n’kuimilila panja. Iwo anali kufuna kukamba naye. 47 Conco munthu wina anamuuza kuti: “Mphunzitsi! Mayi anu na abale anu aimilila panja afuna kukamba nanu.” 48 Poyankha Yesu anauza munthuyo kuti: “Kodi mayi anga ndani, nanga abale anga ndani?” 49 Pamenepo anatambasula dzanja lake n’kulata ophunzila ake. Kenako anati: “Ona! Awa ndiwo mayi anga na abale anga! 50 Pakuti aliyense wocita cifunilo ca Atate wanga amene ali kumwamba, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga, komanso mayi anga.”