Kwa Aroma
3 Kodi kukhala Myuda kuli ndi ubwino wanji, kapena mdulidwe uli ndi phindu lanji? 2 Ubwino wake ndi wambili. Coyamba, mawu opatulika a Mulungu anaikidwa m’manja mwa Ayuda. 3 Nanga bwanji ngati ena anali osakhulupilika? Kodi kusowa cikhulupililo kwawoko kukutanthauza kuti Mulungunso ndi wosakhulupilika? 4 M’pang’ono pomwe! Kwake Mulungu n’kukamba zoona nthawi zonse, ngakhale zitapezeka kuti munthu aliyense ndi wabodza, monga mmene Malemba amanenela kuti: “Mukamalankhula, mumalankhula zacilungamo kuti muwine mlandu pamene mukuweluzidwa.” 5 Komabe ngati kusalungama kwathu kukuonetsa bwino kuti Mulungu ndi wolungama, ndiye tikambe kuti ciyani? Kodi tingakambe kuti Mulungu ndi wosalungama akaonetsa mkwiyo wake? (Ndikulankhula ngati mmene anthu ena onse amalankhulila.) 6 Ayi! Nanga Mulungu akapanda kutelo, kodi adzaliweluza bwanji dziko?
7 Koma ngati cifukwa ca bodza langa coonadi ca Mulungu caonekela kwambili ndipo zimenezo zamubweletsela ulemelelo, n’cifukwa ciyani ndikuweluzidwa monga wocimwa? 8 Ndilekelenji kukamba zimene ena amatinamizila kuti timati: “Tiyeni ticite zoipa kuti zabwino zibwele”? Anthu amenewa adzaweluzidwa mogwilizana ndi cilungamo.
9 Ndiye kodi Ayudafe tili pamalo abwino kuposa ena? Kutali-tali! Cifukwa monga takambila kale, Ayuda ndiponso Agiriki, onse amalamulilidwa ndi ucimo 10 monga mmene Malemba amanenela kuti: “Palibe munthu wolungama ngakhale mmodzi yemwe. 11 Palibe aliyense amene ndi wozindikila ngakhale pang’ono, komanso palibe aliyense amene akuyesetsa kufunafuna Mulungu. 12 Anthu onse apatuka, ndipo onsewo akhala anthu opanda pake. Palibe ngakhale mmodzi amene akuonetsa kukoma mtima.” 13 “Mmelo wawo ndi manda otseguka. Iwo amalankhula zosoceletsa ndi lilime lawo.” “M’milomo yawo muli poizoni wa njoka.” 14 “Ndipo m’kamwa mwawo ndi modzala ndi matembelelo komanso mawu opweteka.” 15 “Mapazi awo amathamangila kukakhetsa magazi.” 16 “Zocita zawo zonse zimakhala zowononga komanso zobweletsa mavuto, 17 ndipo njila ya mtendele saidziwa.” 18 “Iwo saopa Mulungu.”
19 Tsopano tadziwa kuti zinthu zonse zimene Cilamulo cimanena, zimagwila nchito kwa amene amatsatila Cilamuloco. Colinga cake n’kucititsa anthu onse kusowa conena, komanso kuonetsa kuti dziko lonse lili ndi mlandu kwa Mulungu, ndipo liyenela kulangidwa. 20 Conco palibe aliyense amene adzaonedwa wolungama ndi Mulungu mwa kucita nchito za Cilamulo, pakuti Cilamulo cimatithandiza kudziwa bwino ucimo.
21 Koma tsopano zadziwika kuti munthu angakhale wolungama kwa Mulungu popanda kutsatila Cilamulo. Izi zinacitilidwa umboni m’Cilamulo komanso m’zolemba za aneneli. 22 Onse amene amakhulupilila Yesu Khristu, angaonedwe kukhala olungama ndi Mulungu cifukwa palibe kusiyana. 23 Pakuti anthu onse ndi ocimwa ndipo ndi opelewela pa ulemelelo wa Mulungu. 24 Ndipo iwo amaonedwa kukhala olungama mwa cisomo cake cimene waonetsa powamasula kudzela m’dipo limene Khristu Yesu analipila, kumene kuli ngati mphatso yaulele. 25 Mulungu anamupeleka monga nsembe yothandiza anthu kuyanjananso ndi Mulunguyo mwa kukhulupilila magazi ake. Anacita izi pofuna kuonetsa cilungamo cake, cifukwa anaonetsa kuti ndi wosakwiya msanga mwa kukhululuka macimo amene anacitika kale. 26 Anacita izi kuti aonetse cilungamo cake pa nthawi ino, mwa kuona kuti munthu amene amakhulupilila Yesu ndi wolungama.
27 Ndiye kodi pali cifukwa canji codzitamandila? Palibiletu. Kodi tizidzitama cifukwa cotsatila Cilamulo citi? Lamulo la nchito? Ayi ndithu, koma cifukwa cotsatila lamulo la cikhulupililo. 28 Pakuti munthu amakhala wolungama mwa cikhulupililo osati mwa kutsatila Cilamulo. 29 Kodi iye ndi Mulungu wa Ayuda okha? Kodi si kutinso ndi Mulungu wa a mitundu ina? Inde, alinso Mulungu wa anthu a mitundu ina. 30 Pakuti Mulungu ndi mmodzi, iye adzaona kuti anthu odulidwa ndi olungama cifukwa ca cikhulupililo cawo, ndipo adzaonanso kuti anthu osadulidwa ndi olungama cifukwa ca cikhulupililo cawo. 31 Ndiye kodi pamenepa tikuthetsa Cilamulo mwa cikhulupililo cathu? Ayi ndithu! M’malomwake tikulimbikitsa Cilamulo.