Macitidwe a Atumwi
17 Kenako iwo anayenda kudutsa ku Amfipoli komanso Apoloniya ndipo anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge wa Ayuda. 2 Conco Paulo mwacizolowezi cake, analowa m’sunagogemo. Ndipo kwa milungu itatu anali kukambilana nawo kucokela m’Malemba. 3 Iye anafotokoza ndi kuonetsa umboni wolembedwa wowatsimikizila kuti kunali koyenela kuti Khristu avutike, kenako auke. Anali kunena kuti: “Yesu amene ndikumulalikila kwa inu ndiye Khristu.” 4 Zotulukapo zake zinali zakuti, ena mwa iwo anakhala okhulupilila ndipo anagwilizana ndi Paulo ndi Sila. Agiriki ambili opembedza Mulungu komanso azimayi ambili olemekezeka anacitanso cimodzimodzi.
5 Koma Ayuda anacita nsanje, moti anasonkhanitsa anthu ena oipa amene anali kungoyendayenda mu msika. Iwo anapanga gulu laciwawa n’kuyambitsa cipolowe mu mzindamo. Kenako anaphwanya citseko n’kukalowa m’nyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Sila kuti awatulutse panja n’kuwapeleka ku gulu la cipolowelo. 6 Atalephela kuwapeza, anatenga Yasoni komanso abale ena n’kuwaguzila kwa olamulila mu mzinda, akufuula kuti: “Anthu awa amene asokoneza* dziko lonse alinso kuno. 7 Ndipo Yasoni wawalandila ngati alendo ake. Anthu onsewa akucita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara. Iwo akunena kuti kulinso mfumu ina dzina lake Yesu.” 8 Iwo atamva izi, khamu lonse komanso olamulila a mu mzindawo anakwiya kwambili. 9 Olamulila a mzindawo analipilitsa Yasoni komanso enawo ndalama.* Kenako anawamasula.
10 Kutangokuda, abale anatulutsa Paulo ndi Sila n’kuwatumiza ku Bereya. Iwo atafika kumeneko analowa mu sunagoge wa Ayuda. 11 Anthu a ku Bereya anali a mtima wofuna kuphunzila kuposa anthu a ku Tesolonika aja. Iwo analandila mawu a Mulungu ndi cidwi cacikulu kwambili, ndipo tsiku lililonse anali kufufuza Malemba mosamala kuti atsimikizile ngati zimene anamva zinalidi zoona. 12 Conco ambili a iwo anakhala okhulupilila, cimodzimodzinso akazi ochuka ambili ndi amuna acigiriki. 13 Koma Ayuda a ku Tesalonika atadziwa kuti Paulo akulengezanso mawu a Mulungu ku Bereya, anapita kumeneko kukatuntha khamu la anthu kuti agwile atumwiwo. 14 Kenako nthawi yomweyo abale anatumiza Paulo ku nyanja. Koma Sila ndi Timoteyo anatsalila kumeneko. 15 Anthu amene anapelekeza Paulo anafika naye mpaka ku Atene. Koma anabwelela atauzidwa kuti Sila ndi Timoteyo abwele kwa Paulo mwamsanga.
16 Pamene Paulo anali kuwayembekezela ku Atene, cinamuwawa kwambili poona kuti mzindawo ndi wodzala ndi mafano. 17 Conco ali m’sunagoge anayamba kukambilana ndi Ayuda komanso anthu ena olambila Mulungu. Ndipo tsiku lililonse anali kukambilananso ndi anthu amene anali kuwapeza mu msika. 18 Koma ena anzelu za Epikureya ndi Asitoiki anayamba kutsutsana naye. Ena anali kunena kuti: “Kodi munthu wobwetukabwetuka uyu akufuna kutiuza ciyani?” Pamene ena anali kunena kuti: “Ayenela kuti ndi mlaliki wa milungu yacilendo.” Zinali conco cifukwa iye anali kulengeza uthenga wabwino wokamba za Yesu, komanso za kuuka kwa akufa. 19 Conco anamugwila n’kupita naye ku bwalo la Areopagi n’kumuuza kuti: “Kodi ungatifotokozeleko za ciphunzitso catsopano cimene ukuphunzitsaci? 20 Cifukwa ukufotokoza zinthu zimene ndi zacilendo m’makutu mwathu, ndipo tifuna kudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi.” 21 Anthu onse a ku Atene, komanso alendo okhala kumeneko* anali kuthela nthawi yawo yopumula, akufotokoza kapena kumvetsela nkhani zatsopano. 22 Tsopano Paulo anaimilila pakati pa bwalo la Areopagi n’kunena kuti:
“Inu anthu a ku Atene, ndaona kuti pa zinthu zonse mumaopa kwambili milungu* kuposa mmene anthu ena amacitila. 23 Mwacitsanzo, pamene ndinali kudutsa n’kuyang’anitsitsa zinthu zimene mumalambila, ndapezanso guwa la nsembe lolembedwa kuti ‘Kwa Mulungu Wosadziwika.’ Conco ine, ndikulalikila kwa inu za Mulungu wosadziwikayo amene mukumulambila. 24 Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zonse zokhala mmenemo, Mbuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala mu akacisi opangidwa ndi manja. 25 Komanso satumikilidwa ndi manja a anthu ngati kuti amasowa kanthu, cifukwa iye mwini amapeleka kwa anthu onse moyo, mpweya ndi zinthu zina zonse. 26 Ndipo kucokela mwa munthu mmodzi, anapanga mitundu yonse ya anthu kuti ikhale pa dziko lonse lapansi. Iye anaika nthawi yakuti zinthu zina zizicitika, komanso anaika malile a malo akuti anthu azikhalamo. 27 Anacita zimenezo kuti anthuwo afunefune Mulungu, amufufuze ndi kumupezadi, ngakhale kuti iye kwenikweni sali kutali ndi aliyense wa ife. 28 Pakuti cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda, ndipo tilipo ngati mmene andakatulo anu ena ananenela kuti, ‘Pakuti nafenso ndife ana ake.’
29 “Conco, popeza ndife ana a Mulungu, sitiyenela kuganiza kuti Mulunguyo ali ngati golide, siliva, mwala, kapena ciliconse cosemedwa ndi anthu aluso. 30 N’zoona kuti Mulungu ananyalanyaza nthawi imene anthu sanali kudziwa zinthu, koma tsopano akulengeza kwa anthu onse kwina kulikonse kuti alape. 31 Cifukwa wakhazikitsa tsiku limene adzaweluza mwacilungamo dziko lonse lapansi kudzela mwa munthu amene iye wamusankha. Ndipo watsimikizila anthu onse zimenezi mwa kumuukitsa kwa akufa.”
32 Ndiyeno anthuwo atamva za kuuka kwa akufa, ena a iwo anayamba kumunyodola, pamene ena anati: “Tidzakumvetselanso nthawi ina pa nkhaniyi.” 33 Conco Paulo anawasiya. 34 Koma anthu ena anakhala kumbali ya Paulo ndipo anakhala okhulupilila. Ena mwa iwo anali Diyonisiyo, amene anali woweluza m’khoti ya Areopagi, mayi wina dzina lake Damarisi komanso anthu ena.