Macitidwe a Atumwi
8 Saulo anavomeleza zakuti Sitefano aphedwe.
Pa tsiku limenelo, mpingo umene unali ku Yerusalemu unayamba kuzunzidwa koopsa. Ndipo ophunzila onse anamwazikana n’kupita ku zigawo za ku Yudeya ndi Samariya, kupatulapo atumwi. 2 Koma anthu oopa Mulungu ananyamula mtembo wa Sitefano n’kukauika m’manda, ndipo anamulila kwambili. 3 Saulo anayamba kuzunza mpingo mwankhanza. Iye anali kulowa m’nyumba ndi nyumba kumatulutsa panja amuna ndi akazi, kenako n’kukawaponya m’ndende.
4 Komabe, anthu aja amene anamwazikana anapitiliza kulalikila uthenga wabwino wa mawu a Mulungu kumene anapita. 5 Tsopano Filipo anapita ku mzinda* wa Samariya, ndipo anayamba kulalikila za Khristu kwa anthu a kumeneko. 6 Khamu la anthu linali kumvetsela zimene Filipo anali kukamba. Onse pamodzi anali kumvetsela ndi kuona zizindikilo zimene iye anali kucita. 7 Pakuti ambili a iwo anali ndi mizimu yonyansa, ndipo mizimuyo inali kufuula mwamphamvu n’kutuluka. Komanso anthu ambili ofa ziwalo ndi olemala anali kucilitsidwa. 8 Conco anthu a mumzindawo anakondwela kwambili.
9 Ndiyeno mumzindawo munali munthu wina dzina lake Simoni. Izi zisanacitike, iye anali kucita zamatsenga ndiponso zodabwitsa kwa anthu a ku Samariya. Iye anali kudzitama kuti ndi munthu wamphamvu. 10 Anthu onse, kuyambila wamng’ono mpaka wamkulu, anali kucita naye cidwi n’kumanena kuti: “Munthu uyu ali ndi mphamvu yaikulu yocokela kwa Mulungu.” 11 Conco iwo anali kucita naye cidwi cifukwa anawadabwitsa kwa nthawi yaitali ndi zamatsenga zake. 12 Koma pamene anthuwo anakhulupilila Filipo, yemwe anali kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndiponso wokamba za dzina la Yesu Khristu, amuna ndi akazi omwe anali kubatizika. 13 Nayenso Simoni anakhala wokhulupilila, ndipo atabatizika, anapitiliza kutsatila Filipo. Iye anali kudabwa poona zizindikilo* ndi nchito zazikulu zamphamvu zimene zinali kucitika.
14 Pamene atumwi ku Yerusalemu anamva kuti anthu a ku Samariya alandila mawu a Mulungu, anawatumizila Petulo ndi Yohane. 15 Iwo anapita kumeneko ndipo anawapemphelela kuti alandile mzimu woyela. 16 Cifukwa pa nthawiyi, mzimu woyela unali usanafike pa aliyense wa iwo, koma anali atangobatizidwa m’dzina la Ambuye Yesu. 17 Ndiyeno atumwiwo anaika manja awo pamitu ya anthuwo, ndipo iwo anayamba kulandila mzimu woyela.
18 Simoni ataona kuti anthu akulandila mzimu woyela atumwiwo akawaika manja pamutu, anafuna kuwapatsa ndalama. 19 Iye anati: “Inenso ndipatsenkoni mphamvu kuti ndikaika manja anga pamutu pa munthu azilandila mzimu woyela.” 20 Koma Petulo anamuuza kuti: “Siliva wako uwonongeke naye pamodzi, cifukwa ukuganiza kuti ungagule mphatso yaulele ya Mulungu ndi ndalama. 21 Nchitoyi sikukhudza, ndipo ulibepo mbali kapena gawo cifukwa mtima wako si wowongoka pamaso pa Mulungu. 22 Conco lapa coipa cimene wacitaci, ndipo umucondelele Yehova kuti ngati n’kotheka akukhululukile pa maganizo oipa amene ali mumtima mwako. 23 Cifukwa taona kuti ndiwe poizoni wowawa* ndipo ndiwe kapolo wa kupanda cilungamo.” 24 Simoni anawayankha kuti: “Ndipelekeleni pemphelo locondelela kwa Yehova kuti zinthu zimene mwakambazi zisandicitikile.”
25 Conco iwo atatsiliza kucitila umboni mokwanila ndi kulankhula mawu a Yehova, anayamba kubwelela ku Yerusalemu. Pobwelela anali kulengeza uthenga wabwino m’midzi yambili ya Asamariya.
26 Komabe mngelo wa Yehova analankhula ndi Filipo kuti: “Nyamuka upite kum’mwela kumsewu wocokela ku Yerusalemu kupita ku Gaza.” (Msewu umenewu unali wa m’cipululu.) 27 Iye atamva zimenezi, ananyamuka n’kupita, ndipo anakumana ndi nduna ya ku Itiyopiya, munthu wa ulamulilo pansi pa Kandake, mfumukazi ya Itiyopiya. Ndunayo ndiyo inali kuyang’anila cuma conse ca mfumukazi imeneyi, ndipo inapita ku Yerusalemu kukalambila Mulungu. 28 Iyo inali kubwelela kwawo ndipo inali khale m’galeta lake ikuwelenga mokweza ulosi wa mneneli Yesaya. 29 Conco mzimu unauza Filipo kuti: “Pita ufike pafupi ndi galetalo.” 30 Filipo anali kuthamanga m’mbali mwa galetalo, ndipo anamumva akuwelenga mokweza ulosi wa mneneli Yesaya. Ndiyeno Filipo anamufunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwelengazo?” 31 Iye anayankha kuti: “Ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulila?” Conco anapempha Filipo kuti akwele ndi kukhala naye m’galetamo. 32 Mawu a m’Malemba amene iye anali kuwelenga anali akuti: “Anapelekedwa kumalo okamuphela ngati nkhosa. Ndipo iye sanatsegule pakamwa pake ngati mwana wa nkhosa amene wangokhala cete pamaso pa womumeta ubweya. 33 Pamene anali kumucititsa manyazi, sanamucitile zinthu mwacilungamo. Kodi ndani amene angafotokoze mwatsatanetsatane m’badwo wa makolo ake? Cifukwa moyo wake wacotsedwa padziko lapansi.”
34 Ndiyeno ndunayo inauza Filipo kuti: “Conde ndiuze, kodi mneneliyu anali kukamba za ndani apa? Anali kukamba za iye mwini kapena za munthu wina?” 35 Filipo anayamba kulankhula. Iye anayambila palembali kumuuza uthenga wabwino wonena za Yesu. 36 Pamene iwo anali kuyenda mumsewumo, anafika pamene panali madzi ambili, ndipo nduna ija inauza Filipo kuti: “Taonani! Madzi si awa, cikundiletsa kubatizika n’ciyani?” 37* —— 38 Zitatelo, iye analamula kuti galetalo liime. Kenako Filipo ndi nduna ija anatsika n’kulowa m’madzimo, ndipo Filipo anaibatiza. 39 Iwo atatuluka m’madzimo, mwamsanga mzimu wa Yehova unatsogolela Filipo kuti acoke kumeneko moti nduna ija sinamuonenso, koma inapitiliza ulendo wake ikusangalala. 40 Koma Filipo anapezeka kuti ali ku Asidodi, ndipo anayamba kulengeza uthenga wabwino kumizinda yonseyo mpaka anafika ku Kaisareya.