Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Luka
14 Pa nthawi ina, Yesu anapita kukadya cakudya m’nyumba ya mmodzi wa atsogoleli a Afarisi pa Sabata, ndipo iwo anali kumuyang’anitsitsa. 2 Patsogolo pake panali mwamuna wodwala matenda otupikana.* 3 Ndiyeno Yesu anafunsa anthu odziwa bwino Cilamulo ndi Afarisi kuti: “Kodi n’kololeka kucilitsa munthu pa Sabata kapena ayi?” 4 Koma iwo anangokhala cete. Zitatelo, iye anagwila munthuyo n’kumucilitsa, ndipo anamuuza kuti azipita. 5 Kenako iye anawafunsa kuti: “Ndani wa inu amene mwana wake, kapena ng’ombe yake ikagwela m’citsime pa tsiku la Sabata sangaitulutse nthawi yomweyo?” 6 Iwo sanathe kumuyankha funso limeneli.
7 Ndiyeno anthu oitanidwawo anawauza fanizo ataona kuti akudzisankhila malo apamwamba kwambili. Iye anati: 8 “Munthu akakuitanila ku phwando la ukwati, usakhale pa malo apamwamba kwambili. Mwina anaitananso munthu wina wolemekezeka kuposa iwe. 9 Ndiyeno munthu amene anakuitanani nonse awilinu adzabwela kwa iwe n’kukuuza kuti, ‘Pepani, musiyile awa malowo.’ Zikatelo, udzanyamuka mwamanyazi n’kukakhala pa malo otsika kwambili. 10 Koma ukaitanidwa, pita ukakhale pa malo otsika kwambili kuti munthu amene anakuitanayo akabwela, adzakuuze kuti, ‘Mnzangawe, khala pa malo apamwambawa.’ Zikatelo, udzalemekezeka pamaso pa anzako onse oitanidwa. 11 Pakuti aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, ndipo aliyense wodzicepetsa adzakwezedwa.”
12 Ndiyeno anauzanso munthu amene anamuitanayo kuti: “Ukakonza cakudya camasana, kapena cakudya camadzulo, usaitane anzako, abale ako, acibale ako, kapena anthu olemela amene umakhala nawo pafupi, cifukwa nawonso angakakuitane ndipo zidzakhala ngati akukubwezela. 13 Koma iwe ukakonza phwando uziitana osauka, ogolontha, olemala, ndi akhungu, 14 ndipo udzakhala ndi cimwemwe cifukwa iwo alibe coti akubwezele. Pakuti Mulungu adzakubwezela pa kuuka kwa olungama.”
15 Mmodzi wa alendo anzake atamva zimenezi anamuuza kuti: “Wacimwemwe ndi munthu amene adzadya cakudya* mu Ufumu wa Mulungu.”
16 Yesu anamuuza kuti: “Munthu wina anakonza phwando lalikulu la cakudya camadzulo, ndipo anaitana anthu ambili. 17 Pa nthawi ya cakudya camadzuloco, iye anatuma kapolo wake kukauza oitanidwawo kuti, ‘Bwelani, cifukwa zonse zakonzedwa tsopano.’ 18 Koma onse anayamba kupeleka zifukwa zokanila. Woyamba anamuuza kuti, ‘Ine ndinagula munda ndipo ndifuna ndipite ndikauone. Pepani, sindibwela.’ 19 Ndipo wina ananena kuti, ‘Ine ndagula ng’ombe 10 za pajoko ndipo ndifuna ndikaziyese. Pepani, sindibwela.’ 20 Winanso ananena kuti, ‘Ndangokwatila kumene. Pa cifukwa cimeneci, sindibwela.’ 21 Conco kapoloyo anabwela n’kufotokozela mbuye wake zimenezi. Mbuyeyo atamva zimenezi anakwiya kwambili n’kuuza kapolo wake kuti, ‘Pita mwamsanga m’misewu ikuluikulu ndi m’njila za mumzinda, ndipo ukaitane osauka, ogolontha,* akhungu, komanso olemala.’ 22 Kapoloyo atabwelako anati, ‘Mbuyanga, ndacita zimene mwandiuza, koma malo akalimo.’ 23 Ndiyeno mbuye wa kapolo uja anati, ‘Pita m’misewu ya kunja kwa mzinda, ukalimbikitse anthu kubwela kuno kuti nyumba yanga idzale. 24 Ndithu ndikukuuzani, palibe ngakhale mmodzi mwa anthu aja omwe anaitanidwa poyamba, amene adzalawako cakudya canga camadzulo.’”
25 Tsopano khamu lalikulu la anthu linali kuyenda ndi Yesu. Ndiyeno iye anaceuka, n’kuwauza kuti: 26 “Ngati wina afuna kunditsatila, koma osadana* ndi atate ake, amayi ake, mkazi wake, ana ake, abale ake, ndi alongo ake, inde, ngakhale moyo wake, sangakhale wophunzila wanga. 27 Aliyense amene sananyamule mtengo wake wozunzikilapo* n’kunditsatila, sangakhale wophunzila wanga. 28 Mwacitsanzo, ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja, sayamba wakhala pansi n’kuwelengela mtengo wake, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanila zotsilizila nsanjayo? 29 Cifukwa ngati sangacite zimenezo, angayale maziko ake koma osakwanitsa kuitsiliza, ndipo onse oona angayambe kumuseka 30 n’kumanena kuti: ‘Munthu uyu anayamba bwinobwino kumanga, koma camukanga kuti atsilize.’ 31 Kapena ndi mfumu iti ingapite kukamenyana ndi mfumu ina ku nkhondo, siyamba yakhala pansi n’kuganizila mofatsa ngati asilikali ake 10,000 angalimbane ndi asilikali 20,000 a mfumu inayo, imene ikubwela kudzamenyana naye? 32 Ngati waona kuti sangakwanitse kulimbana nayo, mfumuyo ikali kutali, adzatumiza akazembe kukapempha mtendele. 33 Mofanana ndi zimenezi, dziwani kuti palibe aliyense wa inu amene angakhale wophunzila wanga ngati sangasiye* zinthu zake zonse.
34 “Kukamba zoona, mcele ndi wabwino. Koma ngati mcele watha mphamvu yake, kodi mphamvuyo angaibwezeletse ndi ciyani? 35 Mcelewo siwoyenela kuuthila m’nthaka kapena m’manyowa. Anthu amangoutaya. Amene ali ndi matu akumva, amve.”