Kalata Yoyamba kwa Akorinto
15 Tsopano abale, ndikukumbutsani za uthenga wabwino umene ndinaulengeza kwa inu, umenenso inu munaulandila komanso kuukhulupilila mwamphamvu. 2 Mukupulumutsidwa ngati mwagwila mwamphamvu uthenga wabwino umene ndinaulalikila kwa inu. Popanda kutelo ndiye kuti munakhala okhulupilila pacabe.
3 Pa zinthu zoyamba zimene ndinakuphunzitsani zimenenso ine ndinalandila, panali zakuti Khristu anafa kaamba ka macimo athu, mogwilizana ndi Malemba. 4 Komanso zakuti anaikidwa m’manda, ndiyeno anaukitsidwa pa tsiku lacitatu mogwilizana ndi Malemba. 5 Ndipo anaonekela kwa Kefa,* kenako kwa atumwi 12. 6 Pambuyo pake, anaonekela kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi, ndipo ambili a iwo tikali nao, koma ena anafa.* 7 Ndiyeno anakaonekela kwa Yakobo, kenako kwa atumwi onse. 8 Ndipo pothela pake anaonekela kwa ineyo, amene ndinali ngati khanda lobadwa masiku osakwana.
9 Ine ndine wamng’ono kwambili pa atumwi onse, ndipo sindine woyenela kuchedwa mtumwi, cifukwa ndinali kuzunza mpingo wa Mulungu. 10 Koma cifukwa ca cisomo ca Mulungu, ndili mmene ndililimu. Ndipo cisomo cimene anandicitila sicinapite pacabe, cifukwa ndinagwila nchito mwakhama kuposa atumwi onse. Komabe sindinacite zimenezi ndi mphamvu zanga zokha ai, koma cifukwa ca cisomo cimene Mulungu anandicitila. 11 Conco, kaya munaphunzitsidwa ndi ine, kapena iwo, uthenga umene tikulalikila ndi womwewo umene munaukhulupilila.
12 Tsopano ngati timalalikila kuti Khristu anaukitsidwa, n’cifukwa ciani ena a inu mumakamba kuti akufa sadzaukitsidwa? 13 Cifukwa ngati kuuka kwa akufa kulibe, ndiye kuti Khristu nayenso sanaukitsidwe. 14 Koma ngati Khristu sanaukitsidwe, kulalikila kwathu kulibe phindu, ndipo cikhulupililo canu cilibenso phindu. 15 Kuonjezela apo, ndiye kuti ndife mboni zabodza za Mulungu. Cifukwa ngati akufa sadzauka, ndiye kuti tapeleka umboni wonamizila Mulungu kuti anaukitsa Khristu pamene sanamuukitse. 16 Pakuti ngati akufa sadzaukitsidwa, ndiye kuti Khristu nayenso sanaukitsidwe. 17 Cina, ngati Khristu sanaukitsidwe, cikhulupililo canu cilibe nchito. Ndipo macimo anu sadzakhululukidwa. 18 Ndiye kuti naonso amene anafa mogwilizana ndi Khristu, zao zonse zinathela pomwepo. 19 Ngati tinali ndi ciyembekezo mwa Khristu pa moyo uno wokha, ndiye kuti ndife omvetsa cisoni kuposa munthu wina aliyense.
20 Koma tsopano Khristu anaukitsidwa kwa akufa monga cipatso coyambilila ca amene anagona mu imfa. 21 Pakuti imfa inabwela kudzela mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa nakonso kudzabwela kupitila mwa munthu mmodzi. 22 Monga mmene zilili kuti onse amafa cifukwa ca Adamu, onse adzakhalanso ndi moyo kudzela mwa Khristu. 23 Koma aliyense pa nthawi yake: Coyamba Khristu amene ndi cipatso coyambilila, ndiyeno onse amene ndi a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake. 24 Ndiyeno pamapeto pake, adzapeleka Ufumu m’manja mwa Mulungu wake ndi Atate wake, pamene adzathetsa maboma onse, maulamulilo onse, ndi mphamvu zonse. 25 Cifukwa ayenela kulamulila monga mfumu mpaka pamene Mulungu adzaike adani ake onse pansi pa mapazi ake. 26 Ndiponso imfa, mdani womaliza idzaonongedwa. 27 Mulungu “anaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.” Koma pamene anati ‘waika zinthu zonse pansi pa mapazi ake,’ n’zoonekelatu kuti sakuphatikizapo Mulunguyo, amene anaika zinthu zonse pansi pa iye. 28 Koma zinthu zonse zikadzakhala pansi pake, Mwana nayenso adzaonetsa kuti ali pansi pa ulamulilo wa Mulungu, amene anaika zinthu zonse pansi pake, kuti Mulunguyo akhale zinthu zonse kwa aliyense.
29 Tsopano, kodi amene akubatizidwa kuti akhale akufa adzacita ciani? Ngati akufa sadzaukitsidwa konse, n’cifukwa ciani anthuwo akubatizidwa kuti akhale akufa?* 30 N’cifukwa ciani ifenso timaika moyo wathu pa ciopsyezo nthawi zonse? 31 Tsiku lililonse ndimakhala pa ciopsyezo cakuti ndikhoza kufa. Izi n’zoona monga mmene zilili zoona kuti ndimakunyadilani cifukwa ca ubwenzi wanu ndi Khristu Yesu Ambuye wathu. 32 Ngati ndinamenyana ndi zilombo za kuchile ku Efeso, monga mmene ena anacitila,* kodi ndidzapindulapo ciani? Ngati akufa sadzaukitsidwa, “tiyeni tidye ndi kumwa, cifukwa mawa tidzafa.” 33 Musasoceletsedwe. Kugwilizana ndi anthu oipa kumaononga makhalidwe abwino. 34 Yambani kuganiza bwino ndipo muzicita zoyenela komanso musamacite chimo. Pakuti ena a inu simudziwa Mulungu. Ndikulankhula izi kuti ndikucititseni manyazi.
35 Koma wina angakambe kuti: “Kodi akufa adzaukitsidwa bwanji? Nanga adzaukitsidwa ndi thupi lotani?” 36 Iwe munthu wopanda nzelu! Cinthu cimene wabzala sicingakhale ndi moyo pokha-pokha citafa coyamba. 37 Ndipo pa zimene umabzala, umangobzala mbeu cabe, osati mmela umene udzakule, kaya mbeuyo ikhale ya tiligu kapena mbeu ina iliyonse. 38 Koma Mulungu amaipatsa thupi mwa kufuna kwake, ndipo thupi la mbeu ina iliyonse ikamakula imakhala yosiyana ndi inzake. 39 Sikuti matupi onse ndi ofanana. Pali matupi a anthu, matupi a ng’ombe, matupi a mbalame, komanso matupi a nsomba. 40 Ndipo palinso matupi akumwamba ndi matupi apadziko lapansi, koma ulemelelo wa matupi akumwamba ndi wina, komanso ulemelelo wa matupi apadziko lapansi ndi winanso. 41 Ulemelelo wa dzuwa ndi wina, ndipo ulemelelo wa mwezi ndi winanso. Naonso ulemelelo wa nyenyezi ndi wina, ndipo ulemelelo wa nyenyezi iliyonse umakhala wosiyana ndi ulemelelo wa nyenyezi ina.
42 Ndi mmenenso zilili ndi kuuka kwa akufa. Thupi limene lingathe kuola limafoceledwa. Koma thupi limene silingathe kuola limaukitsidwa. 43 Thupi pofoceledwa limakhala lonyozeka, koma limaukitsidwa lili lamphamvu. 44 Limafoceledwa lili la mnofu, koma limaukitsidwa lili lauzimu. Ngati pali thupi la mnofu, palinso thupi lauzimu. 45 Malemba amati: “Munthu woyambilila, Adamu, anakhala munthu wamoyo.” Koma Adamu wothela anakhala mzimu wopatsa moyo. 46 Komabe, thupi loyamba si lauzimu, koma la mnofu. Pambuyo pake panabwela thupi lauzimu. 47 Munthu woyamba anacokela padziko lapansi, ndipo anapangidwa ndi dothi. Munthu waciwili anacokela kumwamba. 48 Anthu a m’dzikoli ali ngati munthu amene Mulungu anapanga kucokela ku dothi. Koma akumwamba ali ngati uja amene anacokela kumwamba. 49 Monga mmene zilili kuti palipano tikufanana ndi amene anapangidwa ndi dothi uja, tidzafanananso ndi uja wakumwamba.
50 Koma ndikukuuzani izi abale, kuti mnofu ndi magazi sizingalowe mu Ufumu wa Mulungu. Ndipo cinthu cimene cingaole sicingalandile kusaola. 51 Taonani! Ndikukuuzani cinsinsi copatulika: Si tonse amene tidzagona mu imfa, koma tonse tidzasintha, 52 m’kanthawi kocepa, m’kuphetila kwa diso pa kulila kwa lipenga lothela. Pakuti lipenga lidzalila, ndiyeno akufa adzaukitsidwa ndi matupi amene sangaole ndipo tidzasintha. 53 Cifukwa matupi amene angaole adzasintha n’kukhala amene sangaole, ndipo ao amene angafe adzasintha n’kukhala amene sangafe. 54 Koma matupi ao amene angaole akadzasintha n’kukhala amene sangaole, komanso matupi ao amene angafe akadzasintha n’kukhala amene sangafe, pamenepo zimene Malemba amakamba zidzakwanilitsidwa zakuti: “Imfa idzamezedwa kwamuyaya.” 55 “Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, kodi kuluma* kwako kuli kuti?”* 56 Kuluma kumene kumabweletsa imfa,* ndi ucimo, koma Cilamulo n’cimene cimaonetsa mphamvu ya ucimo. 57 Koma tiyamika Mulungu cifukwa amatithandiza kupambana kudzela mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.
58 Conco okondedwa abale anga, khalani olimba, musasunthike. Ndipo nthawi zonse muzikhala ndi zocita zambili mu nchito ya Ambuye, podziwa kuti zimene mukucita mu nchito ya Ambuye sizidzapita pacabe.