Kalata Yoyamba kwa Akorinto
2 Conco abale, pamene ndinabwela kwa inu kudzalengeza za cinsinsi copatulika ca Mulungu, sindinalankhule mokokomeza kapena moonetsa kuti ndili ndi nzelu zodabwitsa. 2 Pakuti pamene ndinali pakati panu, ndinasankha kuti ndisadziwe ciliconse kupatulapo Yesu Khristu amene anaphedwa pamtengo.* 3 Pobwela kwa inu, ndinali wofooka ndipo ndinali kunthunthumila ndi mantha. 4 Ndipo polankhula komanso polalikila, mau anga sanali okopa kapena oonetsa nzelu, koma oonetsa mzimu ndi mphamvu, 5 kuti musamakhulupilile nzelu za anthu koma mphamvu ya Mulungu.
6 Tsopano tikulankhula zokhudza nzelu kwa anthu okhwima kuuzimu, koma osati nzelu za nthawi* ino kapena za olamulila a nthawi ino amene adzawonongedwa. 7 Koma tikulankhula zokhudza nzelu ya Mulungu yomwe ndi nzelu yobisika, imene inaonekela mu cinsinsi copatulika, cimene Mulungu anakonzelatu kale-kale nthawi ino isanafike, kuti tikhale ndi ulemelelo. 8 Palibe wolamulila aliyense wa nthawi* ino amene anali kudziwa nzelu imeneyi, cifukwa akanaidziwa sakanapha Ambuye waulemelelo. 9 Koma malinga ndi mmene Malemba amanenela kuti: “Palibe munthu amene anaonapo, kapena kumva, kapenanso kuganizila zimene Mulungu wakonzela anthu amene amamukonda.” 10 Pakuti Mulungu anatiululila zinthu zimenezi kupitila mwa mzimu wake, cifukwa mzimuwo umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.
11 Kodi ndani amene angadziwe maganizo a munthu wina kupatulapo mwiniwakeyo? Mofananamo, palibe amene akudziwa maganizo a Mulungu, kupatulapo mzimu wa Mulungu. 12 Ife sitinalandile mzimu wa dziko, koma mzimu wocokela kwa Mulungu, kuti tidziwe zinthu zimene Mulungu watipatsa mokoma mtima. 13 Timalankhulanso zinthu zimenezi, osati ndi mau ophunzitsidwa ndi nzelu za anthu, koma ndi mau amene mzimu watiphunzitsa, pamene tikufotokoza zinthu zauzimu ndi mau auzimu.
14 Koma munthu wokonda zinthu za m’dziko* sabvomeleza* zinthu za mzimu wa Mulungu, cifukwa amaziona kuti ndi zopusa ndipo sangathe kuzidziwa, cifukwa zimafuna kuzifufuza mwauzimu. 15 Komabe munthu wauzimu amafufuza zinthu zonse, koma iye safufuzidwa ndi munthu aliyense. 16 Nanga “ndani akudziwa maganizo a Yehova kuti amulangize?” Koma ife tili ndi maganizo a Khristu.