UTHENGA WABWINO WOLEMBEDWA NA MATEYO
1 Buku lofotokoza mbili ya* Yesu Khristu* mwana wa Davide, mwana wa Abulahamu:
2 Abulahamu anabeleka Isaki;
Isaki anabeleka Yakobo;
Yakobo anabeleka Yuda na abale ake;
3 Yuda anabeleka Perezi na Zera mwa Tamara;
Perezi anabeleka Hezironi;
Hezironi anabeleka Ramu;
4 Ramu anabeleka Aminadabu;
Aminadabu anabeleka Nasoni;
Nasoni anabeleka Salimoni;
5 Salimoni anabeleka Boazi mwa Rahabe;
Boazi anabeleka Obedi mwa Rute;
Obedi anabeleka Jese;
6 Jese anabeleka Davide mfumu.
Davide anabeleka Solomo mwa mkazi yemwe anali wa Uriya;
7 Solomo anabeleka Rehabiyamu;
Rehabiyamu anabeleka Abiya;
Abiya anabeleka Asa;
8 Asa anabeleka Yehosafati;
Yehosafati anabeleka Yehoramu;
Yehoramu anabeleka Uziya;
9 Uziya anabeleka Yotamu;
Yotamu anabeleka Ahazi;
Ahazi anabeleka Hezekiya;
10 Hezekiya anabeleka Manase;
Manase anabeleka Amoni;
Amoni anabeleka Yosiya;
11 Yosiya anabeleka Yekoniya na abale ake, Ayuda atatsala pang’ono kutengedwa ukapolo kupita ku Babulo.
12 Ku Babuloko, Yekoniya anabeleka Salatiyeli;
Salatiyeli anabeleka Zerubabele;
13 Zerubabele anabeleka Abiyudi;
Abiyudi anabeleka Eliyakimu;
Eliyakimu anabeleka Azoro;
14 Azoro anabeleka Zadoki;
Zadoki anabeleka Akimu;
Akimu anabeleka Eliyudi;
15 Eliyudi anabeleka Eliyezara;
Eliyezara anabeleka Matani;
Matani anabeleka Yakobo;
16 Yakobo anabeleka Yosefe mwamuna wa Mariya. Mariyayu ndiye anabeleka Yesu, wochedwa Khristu.
17 Conco mibadwo yonse, kucokela pa Abulahamu kukafika pa Davide inalipo 14; kucokela pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babulo, panali mibadwo 14; ndipo kucokela pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babulo, mpaka kukafika pa Khristu panali mibadwo 14.
18 Koma kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motele: Pa nthawi imene Mariya mayi ake anali wotomeledwa kwa Yosefe, Mariyayo anapezeka kuti ali na pathupi mwa mzimu woyela* asanatengane. 19 Komabe, cifukwa mwamuna* wake Yosefe anali wolungama, ndipo sanafune kumunyazitsa kwa anthu, anaganiza zomusudzula mwamseli. 20 Koma ataiganizila mofatsa nkhaniyi, mngelo wa Yehova* anaonekela kwa iye m’maloto, n’kumuuza kuti: “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kutengela mkazi wako Mariya ku nyumba, cifukwa pathupi pamene alinapo pakhala mwa mzimu woyela. 21 Iye adzabeleka mwana wamwamuna ndipo udzamuche Yesu,* cifukwa iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku macimo awo.” 22 Zonsezi zinacitikadi, ndipo zinakwanilitsa mawu amene Yehova anakamba kudzela mwa mneneli wake, akuti: 23 “Tamvelani! Namwali adzakhala na pathupi n’kubeleka mwana wamwamuna, ndipo adzamucha Emanuweli.” Dzinali polimasulila limatanthauza kuti “Mulungu Ali Nafe.”
24 Kenako Yosefe anauka n’kucita zimene mngelo wa Yehova anamulangiza. Anatengela mkazi wakeyo ku nyumba. 25 Koma sanagone naye mkaziyo kufikila atabeleka mwana wamwamuna, ndipo Yosefe anacha mwanayo dzina lakuti Yesu.
2 Yesu atabadwa ku Betelehemu wa ku Yudeya m’masiku a Herode mfumu, okhulupilila nyenyezi ocokela Kum’maŵa anabwela ku Yerusalemu. 2 Iwo anati: “Kodi mfumu ya Ayuda imene yabadwa ili kuti? Cifukwa tinaona nyenyezi yake pamene tinali Kum’maŵa, ndipo tabwela kuti tiiŵelamile.” 3 Mfumu Herode itamva zimenezi inavutika maganizo pamodzi na onse okhala mu Yerusalemu. 4 Kenako Herode anasonkhanitsa ansembe aakulu onse na alembi a anthu, n’kuwafunsa za kumene Khristu* adzabadwila. 5 Iwo anamuyankha kuti: “Ku Betelehemu wa Yudeya, pakuti izi n’zimene zinalembedwa kudzela mwa mneneli kuti: 6 ‘Ndipo iwe Betelehemu wa m’dziko la Yuda, sindiwe mzinda waung’ono kwambili pakati pa olamulila a Yuda, cifukwa mwa iwe mudzatuluka wolamulila amene adzaŵeta anthu anga Aisiraeli.’”
7 Ndiyeno Herode anaitanitsa okhulupilila nyenyezi aja mwamseli, na kuwafunsa mosamala kuti adziŵe nthawi yeniyeni imene nyenyeziyo inaonekela. 8 Powatumiza ku Betelehemu, iye anawauza kuti: “Pitani mukamufunefune mosamala mwanayo, ndipo mukakamupeza mudzabwelenso kudzaniuza, kuti inenso nikapite kukamuŵelamila.” 9 Atamva zimene mfumuyo inakamba, ananyamuka n’kumapita. Atanyamuka, nyenyezi ija imene anaiona ali Kum’maŵa inaonekelanso. Ndipo inayamba kuyenda kutsogolo kwawo mpaka inakaima pamwamba pa nyumba imene munali mwanayo. 10 Ataona kuti nyenyeziyo yaima anakondwela kwambili. 11 Pamene analoŵa m’nyumbamo, anamuona mwanayo ali na mayi ake Mariya, ndipo anagwada pansi na kumuŵelamila. Anamasulanso cuma cawo n’kumupatsa mphatso mwanayo. Anamupatsa golide, lubani na mule. 12 Koma popeza anacenjezedwa na Mulungu m’maloto kuti asabwelele kwa Herode, iwo anadzela njila ina pobwelela ku dziko lawo.
13 Iwo atacoka, mngelo wa Yehova anaonekela kwa Yosefe m’maloto n’kumuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu pamodzi na mayi ake uthaŵile ku Iguputo. Ukakhale kumeneko mpaka n’dzakuuze zocita, cifukwa Herode posacedwa adzayamba kufuna-funa mwanayu kuti amuphe.” 14 Conco Yosefe anauka usiku womwewo n’kutenga mwanayo na mayi ake kupita ku Iguputo. 15 Anakhalabe kumeneko mpaka pamene Herode anamwalila. Izi zinakwanilitsa mawu amene Yehova anakamba mwa mneneli wake, akuti: “N’naitana mwana wanga kuti atuluke mu Iguputo.”
16 Herode atazindikila kuti okhulupilila nyenyezi aja am’pusitsa, anakwiya koopsa. Conco anatumiza anthu kuti akaphe ana onse aamuna ku Betelehemu na m’madela onse ozungulila, kuyambila a zaka ziŵili kubwela pansi mogwilizana na nthawi imene okhulupilila nyenyezi aja anamuuza. 17 Izi zinakwanilitsa mawu amene ananenedwa kudzela mwa mneneli Yeremiya akuti: 18 “Mawu olila mokweza anamveka ku Rama. Anali Rakele kulila ana ake, ndipo sanafune kutonthozedwa cifukwa anawo kunalibenso.”
19 Herode atamwalila, mngelo wa Yehova anaonekela kwa Yosefe ku Iguputo 20 ndipo anati: “Nyamuka, tenga mwanayu pamodzi na mayi ake, ubwelele ku dziko la Isiraeli, cifukwa amene anali kufuna-funa moyo wa mwanayu anafa.” 21 Conco ananyamuka na kutenga mwanayo pamodzi na mayi ake, n’kupita ku dziko la Isiraeli. 22 Koma atamva kuti Arikelao ndiye akulamulila ku Yudeya, m’malo mwa Herode tate wake, anaopa kupita kumeneko. Kuwonjezela apo, atacenjezedwa na Mulungu kupitila m’maloto, anacoka n’kupita ku dela la Galileya. 23 Ndipo anapita kukakhala mu mzinda wa Nazareti. Izi zinakwanilitsa mawu amene ananenedwa kudzela mwa aneneli, akuti: “Iye adzachedwa Mnazareti.”*
3 M’masiku amenewo, Yohane M’batizi anapita ku cipululu ca Yudeya, na kuyamba kulalikila. 2 Anali kulalikila kuti: “Lapani, cifukwa Ufumu wa kumwamba wayandikila.” 3 Mneneli Yesaya anali kukamba za ameneyu pamene anati: “Winawake akufuula m’cipululu kuti: ‘Konzani njila ya Yehova! Wongolani misewu yake.’” 4 Yohane anali kuvala covala caubweya wa ngamila na lamba wacikumba m’ciuno mwake. Cakudya cake cinali dzombe na uci. 5 Pa nthawiyo, anthu a mu Yerusalemu na mu Yudeya yense, komanso a m’madela onse ozungulila Yorodani anali kupita kwa iye. 6 Iye anali kuwabatiza* mu mtsinje wa Yorodani, ndipo iwo anali kuulula macimo awo poyela.
7 Yohane ataona kuti Afarisi na Asaduki ambili akubwela ku ubatizowo, anawauza kuti: “Ana a njoka inu, ndani wakucenjezani kuti muthaŵe mkwiyo umene ukubwela? 8 Conco balani zipatso zoonetsa kulapa. 9 Musadzinamize n’kumati, ‘Tili na Abulahamu atate wathu.’ Pakuti nikukuuzani kuti Mulungu angathe kusandutsa miyala iyi kukhala ana a Abulahamu. 10 Nkhwangwa yaikidwa kale ku mizu ya mitengo. Cotelo mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa na kuponyedwa pa moto. 11 Ine nikukubatizani na madzi cifukwa mwalapa. Koma amene akubwela pambuyo panga ni wamphamvu kuposa ine, ndipo sindine woyenela kumuvula nsapato. Ameneyo adzakubatizani na mzimu woyela komanso moto. 12 Fosholo yake youluzila ili m’manja mwake. Iye adzayeletsa kothelatu malo ake opunthila mbewu. Ndipo tiligu adzamututila m’nkhokwe, koma mankhusu* adzawatentha pamoto wosazimitsika.”
13 Kenako Yesu anacoka ku Galileya n’kupita kwa Yohane ku Yorodani kuti akamubatize. 14 Koma Yohaneyo anayesa kumuletsa, amvekele: “Ndine amene niyenela kubatizidwa na inu, nanga bwanji inu mukubwela kwa ine?” 15 Yesu anamuyankha kuti: “Lola kuti zikhale telo pa nthawi ino, cifukwa kucita zimenezi n’koyenela kwa ife kuti tikwanilitse cilungamo conse.” Atatelo, analeka kumuletsa. 16 Yesu atabatizidwa, nthawi yomweyo anavuuka m’madzimo. Atavuuka, kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzatela pa iye. 17 Kumwamba kunamvekanso mawu akuti: “Uyu ndiye mwana wanga wokondeka, amene nimakondwela naye.”
4 Kenako mzimu unatsogolela Yesu ku cipululu kuti akayesedwe na Mdyelekezi. 2 Atasala kudya kwa masiku 40 usana na usiku, anamva njala. 3 Kenako Woyesayo anamuyandikila n’kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani miyala iyi isanduke mitanda ya mkate.” 4 Koma iye anamuyankha kuti: “Malemba amati: ‘Munthu sangakhale na moyo na cakudya cokha ayi, koma na mawu alionse ocokela m’kamwa mwa Yehova.’”
5 Kenako Mdyelekezi anamutengela ku mzinda woyela, ndipo anamukwezeka pamwamba penipeni pa* kacisi 6 na kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, dziponyeni pansi, cifukwa Malemba amati: ‘Iye adzalamula angelo ake za inu,’ ndipo ‘Iwo adzakunyamulani m’manja mwawo, kuti phazi lanu lisagunde mwala.’” 7 Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amatinso: ‘Usamuyese Yehova Mulungu wako.’”
8 Mdyelekezi anatengelanso Yesu ku phili lalitali kwambili n’kumuonetsa maufumu onse a padziko na ulemelelo wawo. 9 Kenako anamuuza kuti: “Zinthu zonsezi nikupatsani mukagwada pansi na kunilambilako kamodzi kokha.” 10 Apa lomba Yesu anamuuza kuti: “Coka Satana! Cifukwa Malemba amati: ‘Yehova Mulungu wako ni amene uyenela kum’lambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.’” 11 Pamenepo Mdyelekezi anamusiya, ndipo angelo anabwela na kuyamba kum’tumikila.
12 Lomba Yesu atamva kuti Yohane wamangidwa, anacoka n’kupita ku Galileya. 13 Ndiponso atacoka ku Nazareti anapita kukakhala ku Kaperenao kumbali kwa nyanja, m’madela a Zebuloni komanso Nafitali. 14 Izi zinakwanilitsa mawu amene anakambidwa kudzela mwa mneneli Yesaya akuti: 15 “Inu anthu okhala m’dziko la Zebuloni na dziko la Nafitali, m’mbali mwa msewu wopita ku nyanja, kutsidya lina la Yorodani, Galileya wa anthu a mitundu ina, 16 anthu okhala mu mdima anaona kuwala kwakukulu, ndipo anthu okhala mu mthunzi wa imfa, kuunika kunawawalila.” 17 Kucokela nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikila kuti: “Lapani, cifukwa Ufumu wa kumwamba wayandikila.”
18 Iye akuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya anaona amuna aŵili a pacibale, Simoni wochedwa Petulo, na Andireya m’bale wake, akuponya ukonde pa nyanja, popeza anali asodzi. 19 Ndiyeno anawauza kuti: “Nitsatileni, ndipo ine nidzakusandutsani asodzi a anthu.” 20 Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo n’kumutsatila. 21 Atacoka pamenepo, anaona amuna enanso aŵili a pacibale, Yakobo mwana wa Zebedayo na m’bale wake Yohane. Iwo anali m’bwato pamodzi na Zebedayo tate wawo akusoka maukonde awo ndipo anawaitana. 22 Nthawi yomweyo anasiya bwatolo na atate awo n’kumutsatila.
23 Kenako anazungulila m’cigawo conse ca Galileya. Iye anali kuphunzitsa m’masunagoge awo na kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu, komanso kucilitsa anthu matenda a mtundu uliwonse na zofooka zilizonse. 24 Mbili yonena za iye inamveka mu Siriya yense, moti anthu anamubweletsela odwala matenda osiyana-siyana na zopweteka zina. Anamubweletselanso ogwidwa na ziŵanda, akhunyu komanso ofa ziwalo, ndipo anawacilitsa. 25 Pa cifukwa ici, makamu a anthu ocokela ku Galileya, ku Dekapoli,* ku Yerusalemu, ku Yudeya, na kutsidya lina la Yorodani anamutsatila.
5 Ataona khamu la anthulo, anakwela m’phili. Ndipo atakhala pansi, ophunzila ake anabwela kwa iye. 2 Kenako anayamba kuwaphunzitsa kuti:
3 “Odala ni anthu ozindikila zosoŵa zawo zauzimu, cifukwa Ufumu wa kumwamba ni wawo.
4 “Odala ni anthu amene akumva cisoni, cifukwa adzatonthozedwa.
5 “Odala ni anthu ofatsa, cifukwa adzalandila dziko lapansi.
6 “Odala ni anthu amene ali na njala komanso ludzu lofuna cilungamo, cifukwa adzakhuta.
7 “Odala ni anthu acifundo, cifukwa adzacitilidwa cifundo.
8 “Odala ni anthu oyela mtima, cifukwa adzaona Mulungu.
9 “Odala ni anthu obweletsa mtendele, cifukwa adzachedwa ana a Mulungu.
10 “Odala ni anthu amene azunzidwa cifukwa ca cilungamo, pakuti Ufumu wa kumwamba ni wawo.
11 “Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, na kukunamizilani zoipa za mtundu uliwonse cifukwa ca ine. 12 Kondwelani na kusangalala kwambili, cifukwa mphoto yanu ni yaikulu kumwamba. Pakuti umu ni mmene anazunzila aneneli amene analipo inu musanakhaleko.
13 “Inu ndinu mcele wa dziko lapansi, koma ngati mcele watha mphamvu, kodi mphamvu yake ingabwezeletsedwe motani? Umakhala wopanda nchito iliyonse, ndipo umangotayidwa kunja kumene anthu amauponda-ponda.
14 “Inu ndinu kuwala kwa dziko. Mzinda wokhala pa phili sungabisike. 15 Anthu akayatsa nyale, saibwinikila na thadza, koma amaiika pa coikapo nyale, ndipo imaunikila onse m’nyumbamo. 16 Mofananamo, onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone nchito zanu zabwino na kulemekeza Atate wanu wa kumwamba.
17 “Musaganize kuti n’nabwela kudzawononga Cilamulo kapena zolemba za aneneli. Sin’nabwele kudzaziwononga ayi, koma kudzazikwanilitsa. 18 Ndithudi nikukuuzani kuti ngakhale kumwamba na dziko lapansi zitacoka, kacilembo kocepetsetsa kapena kambali kakang’ono ka cilembo ca m’Cilamulo sikadzacoka mpaka zonse zitakwanilitsidwa. 19 Cotelo aliyense wophwanya limodzi mwa malamulo aang’ono kwambili amenewa, na kuphunzitsa ena kucita zimenezo, adzakhala wosayenela kuloŵa mu Ufumu wa kumwamba. Koma aliyense wowatsatila na kuphunzitsa ena malamulowa, adzakhala woyenela kuloŵa mu Ufumu wa kumwamba. 20 Pakuti nikukuuzani kuti ngati cilungamo canu siciposa ca alembi na Afarisi, ndithu simudzaloŵa mu Ufumu wa kumwamba.
21 “Munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Usaphe munthu, aliyense wapha munthu wapalamula mlandu wa kukhoti.’ 22 Komabe ine nikukuuzani kuti aliyense wopitiliza kukwiyila m’bale wake, wapalamula mlandu wa ku khoti. Ndipo aliyense wonena m’bale wake na mawu acipongwe, wapalamula mlandu wa ku Khoti Yaikulu. Koma aliyense wonena mnzake kuti, ‘Ndiwe citsilu!’ adzapita ku Gehena* wa moto.
23 “Conco ngati wabweletsa mphatso yako ku guwa la nsembe, ndipo uli komweko wakumbukila kuti m’bale wako ali nawe cifukwa, 24 siya mphatso yako patsogolo pa guwa la nsembe pomwepo, ndipo pita ukayanjane naye m’bale wakoyo coyamba. Ndiyeno ubwelenso udzapeleke mphatso yako.
25 “Usacedwe kuthetsa nkhani na munthu wokuimba mlandu pamene uli naye pa ulendo wopita ku khoti, kuti mwina iye asakakupeleke kwa woweluza, komanso kuti woweluzayo asakakupeleke kwa msilikali wa pakhoti kuti akuponye m’ndende. 26 Ndithu nikukuuza kuti sudzatulukamo mpaka utalipila kakhobili kothela.
27 “Munamva kuti anati: ‘Usacite cigololo.’ 28 Koma ine nikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi mpaka kufika pomulakalaka, wacita naye kale cigololo mu mtima mwake. 29 Tsopano ngati diso lako lakumanja likukucimwitsa, ulikolowole na kulitaya. Pakuti ni bwino kuti ukhale wopanda ciwalo cimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.* 30 Komanso ngati dzanja lako lakumanja likukucimwitsa, ulidule na kulitaya. Pakuti ni bwino kuti ukhale wopanda ciwalo cimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse likaponyedwe ku Gehena.*
31 “Komanso paja anati: ‘Aliyense wosudzula mkazi wake ayenela kumupatsa cikalata ca cisudzulo.’ 32 Koma ine nikukuuzani kuti, aliyense wosudzula mkazi wake pa cifukwa cosakhala ciwelewele,* amapangitsa mkaziyo kukhala pa mayeselo ocita cigololo, ndipo aliyense wokwatila mkazi wotelo amacita cigololo.
33 “Munamvanso kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Usamalumbile koma osacita zimene walumbilazo. M’malo mwake, uzikwanilitsa malumbilo ako kwa Yehova.’ 34 Koma ine nikukuuzani kuti: Musamalumbile n’komwe, kaya mwa kuchula kumwamba cifukwa n’kumene kuli mpando wacifumu wa Mulungu, 35 kapena mwa kuchula dziko lapansi, cifukwa ni copondapo mapazi ake, kapenanso mwa kuchula Yerusalemu cifukwa ni mzinda wa Mfumu yaikulu. 36 Usamalumbile mwa kuchula mutu wako, cifukwa sungakwanitse kusandutsa ngakhale tsitsi limodzi kukhala loyela kapena lakuda. 37 Muzingotsimikiza kuti mukati ‘Inde,’ akhaledi inde, mukati ‘Ayi,’ akhaledi ayi, cifukwa mawu owonjezela pamenepa amacokela kwa woipayo.
38 “Munamva kuti anati: ‘Diso kulipila diso, dzino kulipila dzino.’ 39 Koma ine nikukuuzani kuti: Usalimbane naye munthu woipa. M’malo mwake, aliyense akakumenya mbama kutsaya lakumanja, mutembenuzilenso linalo. 40 Ndipo ngati munthu afuna kukupeleka ku khoti kuti atenge covala cako camkati, mulole kuti atengenso covala cako cakunja. 41 Ndipo ngati winawake waudindo wakulamula kuti umunyamulile katundu kwa mtunda wa kilomita imodzi, munyamulile kwa mtunda wa makilomita aŵili. 42 Munthu akakupempha cinthu mupatse, ndipo amene afuna kubweleka* cinacake kwa iwe usamumane.
43 “Munamva kuti anati: ‘Uzikonda mnzako na kudana naye mdani wako.’ 44 Koma ine nikukuuzani kuti: Pitilizani kukonda adani anu na kupemphelela amene amakuzunzani, 45 kuti muonetse kuti ndinudi ana a Atate wanu wa kumwamba, cifukwa iye amawalitsila dzuŵa lake pa anthu abwino na oipa omwe. Komanso amagwetsela mvula anthu olungama na osalungama omwe. 46 Nanga pali phindu lanji ngati mumakonda anthu okhawo amene amakukondani? Kodi si zimene okhometsa misonkho amacita? 47 Ndipo ngati mumapatsa moni abale anu okha, n’ciyani capadela cimene mukucita? Kodi si zimenenso anthu a mitundu ina amacita? 48 Conco inu muyenela kukhala angwilo,* mmene Atate wanu wa kumwamba alili wangwilo.
6 “Samalani kuti musamacite zabwino* pamaso pa anthu kuti akuoneni, cifukwa mukatelo simudzalandila mphoto kwa Atate wanu amene ali kumwamba. 2 Conco pamene mukupeleka mphatso za cifundo,* musamalize lipenga mmene amacitila anthu acinyengo m’masunagoge na m’misewu, kuti anthu awatamande. Ndithu nikukuuzani, iwo akulandililatu mphoto yawo yonse. 3 Koma inu mukamapeleka mphatso za cifundo, musalole kuti dzanja lanu lamanzele lidziŵe zimene dzanja lanu lamanja likucita, 4 kuti mphatso zanu za cifundo zikhale zamseli. Mukatelo, Atate wanu amene amaona ali kosaoneka adzakudalitsani.
5 “Komanso mukamapemphela, musamacite mmene anthu acinyengo amacitila, cifukwa iwo amakonda kupemphela ataimilila m’masunagoge na pa mphambano za misewu ikulu-ikulu kuti anthu awaone. Ndithu nikukuuzani, iwo akulandililatu mphoto yawo yonse. 6 Koma iwe ukafuna kupemphela, uziloŵa m’cipinda cako kwawekha ndipo uzipemphela kwa Atate wako amene ali kosaoneka. Ukatelo, Atate wako amene amaona ali kosaonekako adzakudalitsa. 7 Popemphela, usamanene mawu amodzi na amodzi, mmene amacitila anthu amitundu ina, cifukwa iwo amaganiza kuti Mulungu adzawamvela akaculukitsa mawu. 8 Conco musakhale ngati iwo cifukwa Atate wanu amadziŵa zimene mukufunikila ngakhale musanam’pemphe n’komwe.
9 “Koma inu muzipemphela motele:
“‘Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeletsedwe.* 10 Ufumu wanu ubwele. Cifunilo canu cicitike, monga kumwamba cimodzimodzinso pansi pano. 11 Mutipatse cakudya cathu ca lelo, 12 ndipo mutikhululukile macimo athu* mmenenso ife takhululukila amene anatilakwila.* 13 Ndiponso musatiloŵetse m’mayeselo, koma mutilanditse* kwa woipayo.’
14 “Pakuti mukamakhululukila anthu zolakwa zawo, nayenso Atate wanu wa kumwamba adzakukhululukilani. 15 Koma ngati simukhululukila anthu zolakwa zawo, nayenso Atate wanu sadzakukhululukilani zolakwa zanu.
16 “Mukamasala kudya, lekani kuonetsa nkhope zacisoni, monga mmene acinyengo aja amacitila. Pakuti iwo amaipitsa nkhope zawo* kuti aonekele kwa anthu kuti akusala kudya. Ndithu nikukuuzani, iwo akulandililatu mphoto yawo yonse. 17 Koma iwe ukamasala kudya, uzidzola mafuta kumutu na kusamba kumaso 18 kuti usaonekele kwa anthu kuti ukusala kudya, koma kwa Atate wako yekhayo amene ali kosaoneka. Ukatelo, Atate wako amene amaona ali kosaonekako adzakudalitsa.
19 “Lekani kudziunjikila cuma padziko lapansi pamene njenjete na nguwe zimawononga, komanso pomwe mbala zimathyola na kuba. 20 Koma mudziunjikile cuma kumwamba, kumene njenjete na nguwe siziwononga, komanso kumene mbala sizithyola na kuba. 21 Pakuti kumene kuli cuma cako, mtima wako umakhalanso komweko.
22 “Nyale ya thupi ni diso. Conco, ngati diso lako ni lolunjika pa cinthu cimodzi,* thupi lako lonse lidzawala. 23 Koma ngati diso lako ni la dyela,* thupi lako lonse lidzacita mdima. Ngati kuwala kuli mwa iwe ni mdima, ndiye kuti mdimawo ni mdima wandiweyani!
24 “Palibe angakhale kapolo wa ambuye aŵili, cifukwa adzadana na mmodzi n’kukonda winayo. Kapena adzakhulupilika kwa mmodzi n’kunyoza winayo. Simungakhale kapolo wa Mulungu komanso wa Cuma pa nthawi imodzi.
25 “Pa cifukwa cimeneci nikukuuzani kuti: Lekani kudela nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya ciyani kapena mudzamwa ciyani, kapenanso za matupi anu kuti mudzavala ciyani. Kodi moyo si wofunika kuposa cakudya, komanso thupi kuposa covala? 26 Yang’anitsitsani mbalame za mumlengalenga. Sizifesa mbewu ayi, kapena kukolola, kapenanso kututila m’nkhokwe. Koma Atate wanu wa kumwamba amazidyetsa. Kodi inu sindinu ofunika kwambili kuposa mbalame? 27 Ndani wa inu angatalikitse moyo wake ngakhale pang’ono pokha* mwa kuda nkhawa? 28 Komanso n’cifukwa ciyani mukudela nkhawa za zovala? Phunzilam’poni kanthu pa mmene maluŵa a kuchile amakulila. Sagwila nchito, kapena kupanga nsalu. 29 Koma nikukuuzani kuti ngakhale Solomo mu ulemelelo wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluŵa amenewa. 30 Lomba ngati umu ni mmene Mulungu amavekela zomela za kuchile, zimene zimangokhalapo lelo, maŵa n’kuziponya pamoto, kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo a cikhulupililo cocepa inu? 31 Conco musamade nkhawa kuti, ‘Tidzadya ciyani?’ kapena, ‘Tidzamwa ciyani?’ kapenanso kuti, ‘Tidzavala ciyani?’ 32 Pakuti anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wa kumwamba adziŵa kuti mukufunikila zinthu zonsezi.
33 “Cotelo pitilizani kufuna-funa Ufumu coyamba na cilungamo cake, ndipo zinthu zina zonsezi zidzawonjezedwa kwa inu. 34 Conco musamade nkhawa za tsiku lotsatila, cifukwa tsiku lotsatila lidzakhala na nkhawa zake. Zovuta za tsiku lililonse n’zokwanila pa tsikulo.
7 “Lekani kuweluza ena kuopela kuti inunso mungaweluzidwe; 2 cifukwa ciweluzo cimene mukuweluza naco ena, inunso mudzaweluzidwa naco, ndipo muyeso umene mukupimila ena, inunso adzakupimilani womwewo. 3 Nanga n’cifukwa ciyani ukuyang’ana kacitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaona mtanda wa mtenje wa nyumba umene uli m’diso lako? 4 Kapena ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘Leka nikucotse kacitsotso m’diso lako,’ pamene iwe m’diso lako muli mtanda wa mtenje wa nyumba? 5 Wonyenga iwe! Coyamba cotsa mtanda wa nyumba umene uli m’diso lakowo. Ukatelo, udzatha kuona bwino-bwino mmene ungacotsele kacitsotso m’diso la m’bale wako.
6 “Musamapatse agalu zinthu zopatulika kapena kuponyela nkhumba ngale zanu, kuopela kuti zingaponde-ponde ngalezo na kutembenuka n’kukukhadzulani.
7 “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; pitilizani kufuna-funa, ndipo mudzapeza; gogodanibe ndipo adzakutsegulilani; 8 pakuti aliyense wopempha amalandila, ndipo aliyense wofuna-funa amapeza, ndiponso aliyense wogogoda adzamutsegulila. 9 Ndani wa inu amene mwana wake akamupempha mkate, angamupatse mwala? 10 Kapena akamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? 11 Cotelo ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wanu wa kumwamba? Ndithudi, iye adzapeleka zinthu zabwino kwa amene amamupempha!
12 “Conco, zinthu zonse zimene mumafuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo. Ndipo izi n’zimene Cilamulo na zolemba za aneneli zimaphunzitsa.
13 “Loŵani pa geti yopanikiza, cifukwa msewu wotakasuka ukupita ku ciwonongeko, ndipo geti yake ni yaikulu, komanso anthu ambili akuyenda mmenemo; 14 koma geti yoloŵela ku moyo ni yopanikiza, ndiponso msewu wake ni wopanikiza, komanso amene akuyendamo ni ocepa.
15 “Samalani na aneneli onyenga amene amabwela kwa inu atavala ngati nkhosa, koma mkati mwawo ni mimbulu yolusa. 16 Mudzawazindikila na zipatso zawo. Anthu sathyola mphesa mu mtengo wa minga, kapena nkhuyu pa citsamba ca minga, amatelo kodi? 17 Mofananamo, mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse woipa umabala zipatso zoipa. 18 Mtengo wabwino sungabale zipatso zoipa, ndipo mtengo woipa sungabale zipatso zabwino. 19 Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino, amaudula n’kuuponya pa moto. 20 Cotelo, anthu amenewo mudzawazindikila mwa zipatso zawo.
21 “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzaloŵa mu Ufumu wa kumwamba ayi, koma yekhayo wocita cifunilo ca Atate wanga amene ali kumwamba. 22 Pa tsikulo, ambili adzati kwa ine: ‘Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenele m’dzina lanu, kutulutsa ziŵanda m’dzina lanu, na kucita nchito zambili zamphamvu m’dzina lanunso?’ 23 Koma ine nidzawauza kuti: ‘Sinikudziŵani m’pang’ono pomwe! Cokani pamaso panga, anthu osamvela malamulo inu!’
24 “Conco, aliyense womva mawu anga na kuwacita, adzakhala ngati munthu wanzelu amene anamanga nyumba yake pa thanthwe. 25 Ndiyeno kunagwa cimvula camphamvu ndipo madzi anasefukila. Kenako kunabwela cimphepo ndipo cinawomba nyumbayo mwamphamvu, koma sinagwe cifukwa maziko ake anali pa thanthwe. 26 Komanso, aliyense womva mawu angawa koma osawacita, adzakhala ngati munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pa mcenga. 27 Ndiyeno kunagwa cimvula camphamvu, ndipo madzi anasefukila. Kenako kunabwela cimphepo cimene cinawomba nyumbayo mwamphamvu, ndipo inagwa na kuwonongeka kothelatu.”
28 Yesu atatsiliza kukamba mawu amenewa, khamu la anthulo linadabwa kwambili na kaphunzitsidwe kake, 29 cifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu waulamulilo, osati monga alembi.
8 Atatsika m’philimo, cikhamu ca anthu cinamutsatila. 2 Ndiyeno kunabwela munthu wakhate, ndipo anamuŵelamila n’kunena kuti: “Ambuye, ngati mufuna munganiyeletse.” 3 Pamenepo Yesu anatambasula dzanja lake n’kumukhudza, ndipo anati: “Nifuna! Khala woyela.” Nthawi yomweyo khate lakelo linatha. 4 Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Samala kuti usauze aliyense zimenezi. Koma pita ukadzionetse kwa wansembe, ndipo ukapeleke mphatso imene Mose analamula, kuti ukhale umboni kwa iwo.”
5 Ataloŵa mu mzinda wa Kaperenao, kapitawo wa asilikali anabwela kwa iye, n’kuyamba kumucondelela 6 kuti: “Bambo, wanchito wanga ali gone m’nyumba, akudwala matenda ofa ziwalo, ndipo akuzunzika koopsa.” 7 Iye anamuuza kuti: “Nikafika kumeneko, nikam’cilitsa.” 8 Kapitawo uja anamuyankha kuti: “Bambo, ine sindine woyenela kuti inu mukaloŵe m’nyumba mwanga. Koma mungonena mawu, ndipo wanchito wanga acila. 9 Pakuti inenso nili na akulu-akulu amene amanilamulila, ndipo nili na asilikali amene nimawalamulila. Nikauza uyu kuti, ‘Pita!’ amapita, nikauza wina kuti, ‘Bwela!’ amabwela, ndipo nikauza kapolo wanga kuti, ‘Cita ici!’ amacita.” 10 Yesu atamva zimenezi anadabwa kwambili, ndipo anauza amene anali kumutsatila aja kuti: “Kukuuzani zoona, mu Isiraeli sin’napezemo munthu wa cikhulupililo cacikulu ngati ici. 11 Koma nikukuuzani kuti ambili ocokela kum’maŵa na kumadzulo, adzabwela kudzakhala pa thebulo pamodzi na Abulahamu, Isaki, komanso Yakobo mu Ufumu wa kumwamba. 12 Koma ana a Ufumuwo adzaponyedwa kunja ku mdima. Kumeneko azikalila na kukukuta mano.” 13 Kenako Yesu anauza kapitawo wa asilikaliyo kuti: “Pita. Popeza waonetsa cikhulupililo, zimene wapempha zicitike.” Ndipo mu ola limenelo wanchito uja anacila.
14 Tsopano Yesu ataloŵa m’nyumba ya Petulo, anaona apongozi aakazi a Petulo ali cigonele cifukwa codwala malungo.* 15 Iye anagwila dzanja lawo, ndipo anacila malungowo, moti anauka n’kuyamba kumukonzela cakudya. 16 Koma madzulo anthu anamubweletsela anthu ambili ogwidwa na ziŵanda, ndipo iye anatulutsa mizimuyo na mawu cabe, komanso anacilitsa onse amene anali kudwala, 17 kuti mawu amene ananenedwa kudzela mwa mneneli Yesaya akwanilitsidwe akuti: “Iyeyo anacotsa matenda athu na kunyamula zoŵaŵa zathu.”
18 Yesu ataona kuti khamu la anthu lamuzungulila, analamula ophunzila ake kuti anyamuke n’kupita naye ku tsidya lina. 19 Tsopano mlembi wina anabwela n’kumuuza kuti: “Mphunzitsi, nikutsatilani kulikonse kumene mungapite.” 20 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Nkhandwe zili na mapanga awo, ndipo mbalame za mumlengalenga zili na zisa, koma Mwana wa munthu alibe nyumba yake-yake.”* 21 Kenako wina mwa ophunzila ake anamuuza kuti: “Ambuye, niloleni coyamba nipite nikaike malilo a atate anga.” 22 Yesu anamuyankha kuti: “Pitiliza kunitsatila, aleke akufa aike akufa awo.”
23 Atakwela bwato, ophunzila ake anamutsatila. 24 Ndiyeno pa nyanjapo panauka namondwe woopsa! moti madzi anayamba kuloŵa m’bwatomo cifukwa ca kukula kwa mafunde; koma iye anali mtulo. 25 Kenako iwo anapita kukamuutsa n’kumuuza kuti: “Ambuye, tipulumutseni tikufa!” 26 Koma iye anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukucita mantha conci, a cikhulupililo cocepa inu?” Kenako iye anauka n’kudzudzula mphepo na nyanjayo, ndipo panakhala bata lalikulu. 27 Poona izi, ophunzilawo anadabwa ndipo anati: “Kodi munthu ameneyu ni wotani? Ngakhale mphepo na nyanja zikumumvela!”
28 Yesu atafika kutsidya lina la nyanja m’cigawo ca Agadara, anakumana na amuna aŵili ogwidwa na ziŵanda akucokela ku manda.* Iwo anali aukali kwambili, moti panalibe munthu anali kulimba mtima kupitila njila imeneyo. 29 Pamenepo iwo anayamba kufuula kuti: “Mufuna ciyani kwa ife inu Mwana wa Mulungu? Kodi mwabwela kudzatizunza nthawi yoikika isanakwane?” 30 Capatali ndithu kucokela pamenepo, panali gulu la nkhumba zambili zimene zinali kudya. 31 Cotelo ziŵandazo zinayamba kumucondelela kuti: “Ngati mutitulutse, mutitumize tikaloŵe m’nkhumba izo.” 32 Ndipo Yesu anaziuza kuti: “Pitani!” Pamenepo ziŵandazo zinatuluka n’kupita kukaloŵa m’nkhumbazo. Zitatelo, nkhumbazo zinathamangila ku phompho mpaka kukagwela m’nyanja, ndipo zinafela momwemo. 33 Koma oŵetela nkhumbazo anathaŵa. Ataloŵa mu mzinda, anafotokozela anthu zonse zimene zinacitika, kuphatikizapo za amuna ogwidwa na ziŵanda aja. 34 Pamenepo anthu onse a mu mzindawo anapita kukakumana na Yesu, ndipo atamuona anamupempha kuti acoke m’dela lawo.
9 Conco Yesu anakwela bwato n’kuwolokela ku tsidya lina, ndipo analoŵa mu mzinda wakwawo. 2 Kumeneko, anthu anamubweletsela munthu wofa ziwalo ali gone pa macila. Ataona cikhulupililo cawo, Yesu anauza wofa ziwaloyo kuti: “Limba mtima mwanawe, macimo ako akhululukidwa.” 3 Tsopano alembi ena mumtima anati: “Munthu uyu akunyoza Mulungu.” 4 Podziŵa maganizo awo, Yesu anati, “N’cifukwa ciyani mukuganiza zinthu zoipa m’mitima mwanu? 5 Mwa citsanzo, cosavuta n’citi, kukamba kuti, ‘Macimo ako akhululukidwa,’ kapena kukamba kuti, ‘Nyamuka uyambe kuyenda’? 6 Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa munthu ali na mphamvu zokhululukila macimo pa dziko lapansi . . .” kenako anauza wofa ziwaloyo kuti, “Nyamuka, nyamula macila akowa, pita ku nyumba kwanu.” 7 Iye ananyamuka n’kumapita kwawo. 8 Khamu la anthulo litaona zimenezi linagwidwa na mantha, ndipo linatamanda Mulungu amene anapeleka mphamvu zotelo kwa anthu.
9 Atacoka pamenepo, Yesu anaona munthu wina dzina lake Mateyo, atakhala pansi mu ofesi yokhometsela misonkho, ndipo anamuuza kuti: “Khala wotsatila wanga.” Nthawi yomweyo iye ananyamuka na kumutsatila. 10 Patapita nthawi, Yesu anali kudya m’nyumba, ndipo okhometsa misonkho ambili komanso ocimwa, anabwela n’kuyamba kudya naye pamodzi na ophunzila ake. 11 Koma Afarisi ataona zimenezi anafunsa ophunzila ake kuti: “N’cifukwa ciyani mphunzitsi wanu amadya na okhometsa misonkho komanso ocimwa?” 12 Yesu atamva zimenezi anati: “Anthu athanzi safunikila dokotala, koma odwala ndiwo amamufuna. 13 Cotelo, pitani mukamvetsetse tanthauzo la mawu akuti: ‘Nifuna cifundo osati nsembe.’ Pakuti n’nabwela kudzaitana anthu ocimwa osati olungama.”
14 Kenako ophunzila a Yohane anabwela kwa iye n’kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani ife na Afarisi timasala kudya, koma ophunzila anu sasala kudya?” 15 Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati sakhala acisoni ngati mkwatiyo ali nawo limodzi, amatelo kodi? Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzacotsedwa pakati pawo, ndipo panthawiyo adzasala kudya. 16 Palibe munthu amene amasokelela cigamba ca nsalu yatsopano pa covala cakunja cakale, cifukwa akatelo cigamba catsopanoco cimaguza covalaco, ndipo pong’ambikapo pamakula kwambili. 17 Ndiponso anthu sathila vinyo watsopano m’matumba acikumba akale. Akatelo, matumba a vinyowo amaphulika, ndipo vinyoyo amatayika matumbawo n’kuwonongeka. Koma anthu amathila vinyo watsopano m’matumba acikumba atsopano, ndipo zonse ziŵili zimasungika bwino.”
18 Pamene iye anali kuwauza zimenezi, kunafika wolamulila wina amene anamugwadila na kumuuza kuti: “Pano nikukamba, mwana wanga wamkazi ayenela kuti wamwalila. Koma tiyeni mukaike dzanja lanu pa iye, ndipo akhalanso na moyo.”
19 Pamenepo Yesu ananyamuka pamodzi na ophunzila ake n’kumutsatila. 20 Tsopano mayi wina wodwala matenda otaya magazi kwa zaka 12, anamuyandikila kumbuyo kwake n’kugwila ulusi wopota wa covala cake cakunja, 21 cifukwa mumtima mwake anali kunena kuti: “Nikangogwila covala cake cakunja, nicila ndithu.” 22 Pamenepo Yesu anatembenuka, ndipo atamuona anati: “Limba mtima mwanawe! Cikhulupililo cako cakucilitsa.” Kucokela ola limenelo, mayiyo anacila.
23 Ndiyeno Yesu ataloŵa m’nyumba ya wolamulila uja, anaona anthu oliza zitolilo, komanso anthu ambili akulila mokweza. 24 Ndiyeno Yesu anati: “Tulukani, cifukwa mtsikana wamng’onoyu sanamwalile koma wagona.” Anthuwo atamva zimenezi anayamba kumuseka monyodola. 25 Atangowatulutsa panja anthuwo, Yesu analoŵa n’kugwila dzanja la mtsikanayo, ndipo iye anauka. 26 Nkhani imeneyi inafala m’dela lonselo.
27 Yesu pocoka kumeneko, amuna aŵili akhungu anam’tsatila. Iwo anali kufuula, amvekele: “Ticitileni cifundo inu Mwana wa Davide.” 28 Ataloŵa m’nyumba, akhungu aja anafika kwa Yesu, ndipo iye anawafunsa kuti: “Kodi muli na cikhulupililo cakuti ningacite zimenezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde Ambuye.” 29 Kenako anawagwila m’maso na kuwauza kuti: “Zicitike mogwilizana na cikhulupililo canu.” 30 Pamenepo anayamba kuona. Ndiyeno Yesu anawacenjeza mwamphamvu kuti: “Samalani kuti aliyense asadziŵe zimenezi.” 31 Koma atatuluka panja, anafalitsa za iye m’dela lonselo.
32 Pamene iwo anali kucoka, anthu anamubweletsela munthu wosalankhula wogwidwa na ciŵanda. 33 Ciŵandaco atacitulutsa, munthu wosalankhulayo anayamba kulankhula. Khamu la anthulo litaona zimenezi, linadabwa kwambili ndipo linati: “Zotelezi sitinazionepo mu Isiraeli.” 34 Koma Afarisi anali kunena kuti: “Ameneyu amatulutsa ziŵanda na mphamvu za wolamulila ziŵanda.”
35 Ndiyeno Yesu anayamba ulendo woyendela mizinda na midzi yonse. Anali kuphunzitsa m’masunagoge awo, kulalikila uthenga wabwino, na kucilitsa matenda a mtundu uliwonse komanso zofooka zilizonse. 36 Ataona cikhamu ca anthuwo, anawamvela cisoni cifukwa anali omyuka-myuka komanso otayika ngati nkhosa zopanda m’busa. 37 Kenako iye anauza ophunzila ake kuti: “Zoonadi, zokolola n’zoculuka, koma anchito ni ocepa. 38 Conco pemphani mwini zokolola kuti atumize anchito okakolola.”
10 Conco, anaitana ophunzila ake 12 na kuwapatsa ulamulilo pa mizimu yonyansa, kuti aziitulutsa komanso kuti azicilitsa anthu matenda a mtundu uliwonse na zofooka zilizonse.
2 Maina a atumwi 12 amenewo ni awa: Simoni wochedwanso Petulo, na Andireya m’bale wake; Yakobo mwana wa Zebedayo na Yohane m’bale wake; 3 Filipo na Batulomeyo; Thomasi na Mateyo wokhometsa misonkho; Yakobo mwana wa Alifeyo; Tadeyo; 4 Simoni Kananiya;* na Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anapeleka Yesu.
5 Yesu anatumiza amuna 12 amenewa na kuwapatsa malangizo akuti: “Musapite mumsewu wa anthu a mitundu ina. Komanso musaloŵe mu mzinda uliwonse wa Asamariya. 6 M’malo mwake, nthawi zonse muzipita kwa nkhosa zosocela za nyumba ya Isiraeli. 7 Pamene mukupita, muzilalikila kuti: ‘Ufumu wa kumwamba wayandikila.’ 8 Cilitsani odwala, ukitsani akufa, yeletsani akhate, tulutsani ziŵanda. Munalandila kwaulele, pelekani kwaulele. 9 Musanyamule golide kapena siliva kapena kopa m’zikwama zanu za ndalama. 10 Musanyamulenso cola ca zakudya za paulendo kapena zovala ziŵili,* kapena nsapato, kapenanso ndodo, pakuti wanchito ayenela kulandila cakudya cake.
11 “Mukaloŵa mu mzinda kapena m’mudzi uliwonse, funa-funani mmenemo amene ali woyenelela, ndipo mukhalebe mmenemo mpaka nthawi yocoka. 12 Mukaloŵa m’nyumba, pelekani moni kwa a m’nyumbayo. 13 Ngati nyumbayo ni yoyenelela, mtendele umene mukuifunila ukhale pa iyo. Koma ngati si yoyenelela, mtendele wanu mubwelele nawo. 14 Kulikonse kumene munthu sakakulandilani kapena kumvetsela mawu anu, potuluka m’nyumba imeneyo kapena mu mzinda umenewo, kutumulani fumbi ku mapazi anu. 15 Ndithu nikukuuzani kuti pa Tsiku la Ciweluzo, cilango ca Sodomu na Gomora cidzakhala cocepelako poyelekezela na ca mzinda umenewo.
16 “Tamvelani! Nikukutumizani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Conco khalani ocenjela ngati njoka, koma oona mtima ngati nkhunda. 17 Samalani na anthu cifukwa adzakupelekani ku makhoti aang’ono, ndipo adzakukwapulani m’masunagoge awo. 18 Ndiponso adzakupelekani kwa abwanamkubwa na mafumu cifukwa ca ine, kuti ukhale umboni kwa iwo komanso kwa anthu a mitundu ina. 19 Komabe akakupelekani kumeneko, musade nkhawa za mmene mukakambile kapena zimene mukakambe, cifukwa zimene mukakambe mudzapatsidwa nthawi yomweyo. 20 Pakuti amene adzakamba si inuyo panokha ayi, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzela mwa inu. 21 Komanso m’bale adzapeleka m’bale wake kuti aphedwe, tate adzapeleka mwana wake, ndipo ana adzaukila makolo awo n’kuwapeleka kuti aphedwe. 22 Anthu onse adzakudani cifukwa ca dzina langa. Koma amene adzapilile* mpaka mapeto adzapulumuka. 23 Akakuzunzani mu mzinda wina, thaŵilani ku mzinda wina. Ndithu nikukuuzani kuti Mwana wa munthu adzafika musanatsilize kuzungulila mizinda yonse ya Isiraeli.
24 “Wophunzila saposa mphunzitsi wake, ndipo kapolo saposa mbuye wake. 25 N’zokwanila kwa wophunzila kukhala ngati mphunzitsi wake, komanso kwa kapolo kukhala ngati mbuye wake. Ngati anthu akucha mutu wa banja kuti Belezebule,* kuli bwanji a m’banja lake? Kodi sadzawacha maina oipa kuposa pamenepa? 26 Conco musawaope, pakuti palibe cobisika cimene sicidzaoneka. Ndipo palibe cinsinsi cimene sicidzadziŵika. 27 Zimene nakuuzilani mu mdima, zikambeni poyela. Ndipo mawu oŵeleŵesa amene mwamva, alalikileni pa mitenje ya nyumba. 28 Musamaope amene amapha thupi koma sangaphe moyo.* M’malo mwake, muziopa amene angathe kuwononga zonse ziŵili, moyo na thupi lomwe mu Gehena.* 29 Mpheta ziŵili amazigulitsa kakhobili kamodzi kocepa mphamvu, si conco kodi? Koma palibe ngakhale imodzi imene ingagwe pansi Atate wanu osadziŵa. 30 Ndipo ngakhale tsitsi la m’mutu mwanu amaliŵelenga lonse. 31 Conco musaope; ndinu ofunika kwambili kuposa mpheta zambili.
32 “Aliyense wonivomela pamaso pa anthu, inenso nidzamuvomela pamaso pa Atate wanga amene ali kumwamba. 33 Koma aliyense wonikana pamaso pa anthu, inenso nidzamukana pamaso pa Atate wanga amene ali kumwamba. 34 Musaganize kuti n’nabweletsa mtendele pa dziko lapansi. Sin’nabweletse mtendele koma lupanga. 35 Pakuti n’nabwela kudzacititsa magaŵano pakati pa mwana wamwamuna na atate ake, mwana wamkazi na amayi ake, komanso mkazi wokwatiwa na apongozi ake aakazi. 36 Kukamba zoona, adani a munthu adzakhala anthu a m’banja lake lomwe. 37 Munthu aliyense wokonda kwambili atate ake kapena amayi ake kuposa ine, si woyenela ine. Ndipo aliyense wokonda kwambili mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi kuposa ine, si woyenela ine. 38 Ndiponso aliyense wosalandila mtengo wake wozunzikilapo* na kunitsatila, si woyenela ine. 39 Aliyense woyesa kupulumutsa moyo wake adzautaya, ndipo aliyense wotaya moyo wake cifukwa ca ine adzaupeza.
40 “Munthu aliyense amene wakulandilani, walandilanso ine, ndipo aliyense amene walandila ine, walandilanso Iye amene ananituma. 41 Munthu aliyense wolandila mneneli poona kuti ni mneneli, adzalandila mphoto ya mneneli. Ndipo aliyense wolandila munthu wolungama poona kuti ni munthu wolungama, adzalandila mphoto ya munthu wolungama. 42 Aliyense wopatsa mmodzi wa ana aang’ono awa ngakhale kapu cabe ya madzi ozizila kuti amwe cifukwa ni wophunzila wanga, ndithu nikukuuzani kuti mphoto yake siidzatayika ngakhale pang’ono.”
11 Yesu atatsiliza kupeleka malangizo kwa ophunzila ake 12, anacoka kumeneko n’kupita kukaphunzitsa na kukalalikila ku mizinda ina.
2 Koma pamene Yohane anali m’ndende, anamva za nchito za Khristu, ndipo anatuma ophunzila ake 3 kukamufunsa kuti: “Kodi Mesiya uja amene tikuyembekezela ndinu, kapena tiyembekezelebe wina?” 4 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Pitani mukamuuze Yohane zimene mukumva na kuona: 5 Tsopano akhungu akuona, olemala akuyenda, akhate akuyeletsedwa, ogontha akumva, akufa akuukitsidwa, ndipo osauka akuuzidwa uthenga wabwino. 6 Wodala ni munthu amene sapeza copunthwitsa mwa ine.”
7 Pamene ophunzila a Yohane anali kubwelela, Yesu anayamba kulankhula na khamu la anthulo za Yohane kuti: “Kodi munapita ku cipululu kukaona ciyani? Kodi munapita kukaona bango logwedezeka na mphepo? 8 Nanga munapita kukaona ciyani? Munthu wovala zovala zapamwamba?* Iyai, anthu ovala zovala zapamwamba amapezeka m’nyumba za mafumu. 9 Ndiye n’cifukwa ciyani munapita kumeneko? Kukaona mneneli? Inde, nikukuuzani kuti iye amaposanso mneneli. 10 Uyu ni amene Malemba amati za iye: ‘Taona! Nikutumiza mthenga wanga patsogolo pako, amene adzakukonzela njila!’ 11 Ndithu nikukuuzani kuti pa anthu onse obadwa kwa akazi, sipanabadwepo aliyense wamkulu kuposa Yohane M’batizi. Koma wocepelapo mu Ufumu wa kumwamba ni wamkulu kuposa iye. 12 Kuyambila m’masiku a Yohane M’batizi mpaka pano, anthu akhala akulimbikila kuti apeze mwayi wokaloŵa mu Ufumu wa kumwamba. Ndipo amene akucita khama akuupeza. 13 Pakuti zonse, zolemba za aneneli komanso Cilamulo, zinalosela mpaka nthawi ya Yohane. 14 Kaya mukhulupilila kapena ayi, iye ndiye ‘Eliya amene aneneli anakamba kuti adzabwela.’ 15 Ali na matu amve.
16 “Kodi m’badwo uwu niuyelekezele na ndani? Uli ngati ana aang’ono opezeka m’misika amene akuitana anzawo oseŵela nawo 17 kuti: ‘Tinakuimbilani citolilo, koma inu simunavine. Tinalila mokweza, koma inu simunadzigugude pa cifuwa pomva cisoni.’ 18 Mofananamo, Yohane anabwela ndipo sanali kudya kapena kumwa, koma anthu anali kunena kuti, ‘Iye ali na ciŵanda.’ 19 Mwana wa munthu anabwela ndipo amadya na kumwa, koma anthu amati, ‘Taonani! Munthu wosusuka komanso wokonda kumwa vinyo, bwenzi la okhometsa misonkho na ocimwa.’ Mulimonsemo, nzelu imatsimikizilika kuti ni yolungama mwa nchito zake.”*
20 Kenako anayamba kudzudzula mizinda imene anacitamo nchito zamphamvu zambili cifukwa sinalape. 21 Anati: “Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwenso Betsaida! Cifukwa nchito zamphamvu zomwe zinacitika mwa inu zikanacitika ku Turo na ku Sidoni, anthu kumeneko akanalapa kale-kale, ndipo akanavala masaka aciguduli n’kukhala pa phulusa. 22 Koma ine nikukuuzani kuti, cilango ca Turo na Sidoni pa Tsiku la Ciweluzo, cidzakhala cocepelako poyelezekela na canu. 23 Ndipo iwe Kaperenao, kodi mwina udzakwezedwa kumwamba? Ayi udzatsikila ku Manda,* cifukwa nchito zamphamvu zimene zinacitika mwa iwe zikanacitikila ku Sodomu, mzindawo ukanakhalapobe mpaka lelo. 24 Koma nikukuuzani kuti cilango ca Sodomu pa Tsiku la Ciweluzo cidzakhala cocepelako poyelekezela na ca Kaperenao.”
25 Panthawiyo Yesu anati: “Nikukutamandani inu Atate, Ambuye wa kumwamba na dziko lapansi, cifukwa zinthu zimenezi mwazibisa kwa anthu anzelu komanso ophunzila kwambili, koma mwaziulula kwa ana aang’ono. 26 Inde Atate, cifukwa munaona kuti zimenezi ndiye zili bwino. 27 Atate wanga wapeleka zinthu zonse kwa ine, ndipo palibe amene akumudziŵa bwino Mwana kupatulapo Atate. Palibenso amene akuwadziŵa bwino Atate kupatulapo Mwana, komanso aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululila za Atatewo. 28 Bwelani kwa ine inu nonse ogwila nchito zolemetsa komanso inu olemedwa, ndipo ine nidzakutsitsimutsani. 29 Nyamulani joko yanga na kuphunzila kwa ine, cifukwa ndine wofatsa komanso wodzicepetsa, ndipo mudzatsitsimutsidwa. 30 Cifukwa joko yanga ni yosavuta kunyamula, ndipo katundu wanga ni wopepuka.”
12 Pa nthawiyo Yesu anali kudutsa m’minda ya tiligu pa Sabata. Ophunzila ake anamva njala, ndipo anayamba kuthyola ngalangala za tiligu n’kumadya. 2 Afarisi ataona izi, anamuuza kuti: “Onani! Ophunzila anu akucita zosaloleka pa Sabata.” 3 Iye anawayankha kuti: “Kodi simunaŵelenge zimene Davide anacita pamene iye na amuna amene anali naye anamva njala? 4 Kodi si paja analoŵa m’nyumba ya Mulungu na kudya mitanda ya mkate wa cionetselo, imene sikunali kololeka iye kudya kapena anthu omwe anali naye, koma ansembe okha? 5 Kapena simunaŵelenge m’Cilamulo kuti pa Sabata, ansembe m’kacisi amaphwanya lamulo la Sabata koma amakhalabe osalakwa? 6 Koma nikukuuzani kuti winawake wamkulu kuposa kacisi ali pano. 7 Komabe, mukanamvetsetsa tanthauzo la mawu akuti, ‘Nifuna cifundo osati nsembe,’ simukanaweluza anthu osalakwa. 8 Pakuti Mwana wa munthu ndiye Mbuye wa Sabata.”
9 Atacoka pa malowo anapita kukaloŵa mu sunagoge wawo, 10 ndipo mmenemo munali mwamuna wina wopuwala dzanja! Cotelo iwo anafunsa Yesu kuti, “Kodi n’kololeka kucilitsa munthu pa Sabata?” Colinga cawo cinali kumupeza cifukwa. 11 Iye anawayankha kuti: “Ngati muli na nkhosa imodzi ndipo nkhosayo n’kugwela m’dzenje pa Sabata, ndani wa inu amene sangaigwile n’kuitulutsa? 12 Koma munthu ni wofunika kwambili kuposa nkhosa! Conco n’kololeka kucita cabwino pa Sabata.” 13 Ndiyeno anauza munthu uja kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi dzanjalo, ndipo linakhala bwino mofanana na linalo. 14 Koma Afarisiwo anacoka n’kupita kukamukonzela ciwembu kuti amuphe. 15 Yesu atadziŵa zimenezi, anacoka kumeneko. Anthu ambili anamutsatila, ndipo iye anawacilitsa onsewo, 16 koma anawalamula mwamphamvu kuti asamuulule. 17 Izi zinakwanilitsa mawu amene anakambidwa kupitila mwa mneneli Yesaya akuti:
18 “Taonani! Mtumiki wanga amene n’namusankha, wokondedwa wanga, amene nimakondwela naye! Nidzaika mzimu wanga pa iye, ndipo adzathandiza anthu a mitundu ina kudziŵa cilungamo ceniceni. 19 Iye sadzakangana na anthu kapena kufuula, ndipo palibe amene adzamva mawu ake m’misewu. 20 Bango lililonse lophwanyika sadzalithyola-thyola, ndipo nyale iliyonse yofuka sadzaizimitsa, mpaka atakwanitsa kubweletsa cilungamo. 21 Ndithudi, m’dzina lake mitundu ya anthu idzakhala na ciyembekezo.”
22 Ndiyeno anamubweletsela munthu wogwidwa na ciŵanda, amene anali wakhungu komanso wosalankhula. Anamucilitsa moti munthuyo anayamba kulankhula na kuona. 23 Zitatelo, khamulo linadabwa kwambili, ndipo linayamba kunena kuti: “Kodi ameneyu sangakhale Mwana uja wa Davide?” 24 Atamva izi, Afarisi anati: “Munthu uyu satulutsa ziŵanda na mphamvu zake ayi, koma na mphamvu za Belezebule,* wolamulila ziŵanda.” 25 Atadziŵa maganizo awo, Yesu anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogaŵikana umatha, ndipo mzinda uliwonse kapena nyumba iliyonse yogaŵikana, silimba. 26 Mofanana na zimenezi, ngati Satana amatulutsa Satana, ndiye kuti wagaŵikana, nanga ufumu wake ungakhalepo bwanji? 27 Kuwonjezela apo, ngati ine nimatulutsa ziŵanda na mphamvu ya Belezebule, nanga ophunzila anu amazitulutsa na mphamvu ya ndani? Ndiye cifukwa cake iwo adzakuweluzani. 28 Koma ngati nimatulutsa ziŵanda na mphamvu ya mzimu wa Mulungu, ndiye kuti Ufumu wa Mulungu wakufikanidi modzidzimutsa. 29 Kapena munthu angathyole bwanji nyumba ya munthu wamphamvu na kumulanda katundu wake asanayambe wam’manga munthu wamphamvuyo? Akamumanga m’pamene angathe kutenga zinthu m’nyumbamo. 30 Aliyense amene sali kumbali yanga akutsutsana nane, ndipo aliyense amene sakunithandiza kusonkhanitsa anthu kwa ine akuwamwaza.
31 “Pa cifukwa cimeneci, nikukuuzani kuti anthu adzakhululukidwa chimo lililonse kapena mawu onyoza alionse amene angakambe, koma wonyoza mzimu sadzakhululukidwa. 32 Mwa citsanzo, aliyense wokamba mawu onyoza Mwana wa munthu adzakhululukidwa, koma aliyense wonyoza mzimu woyela sadzakhululukidwa, kaya m’nthawi ino* kapena imene ikubwelayo.
33 “Inu mumacititsa mtengo pamodzi na zipatso zake kukhala zabwino, kapena mumacititsa mtengo pamodzi na zipatso zake kukhala zoipa, cifukwa mtengo umadziŵika na zipatso zake. 34 Ana a njoka inu, mungalankhule bwanji zinthu zabwino pamene muli oipa? Pakuti pakamwa pamalankhula zosefukila mu mtima. 35 Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino m’cuma cake cabwino, koma munthu woipa amatulutsa zinthu zoipa m’cuma cake coipa. 36 Nikukuuzani kuti pa Tsiku la Ciweluzo anthu adzayankha mlandu pa mawu alionse acabe-cabe amene amakamba; 37 Pakuti mwa mawu ako udzaweluzidwa kuti ndiwe wolungama, ndiponso mwa mawu ako udzaweluzidwa kuti ndiwe wolakwa.”
38 Ndiyeno pomuyankha, alembi na Afarisi ena anati: “Mphunzitsi, tifuna mutionetse cizindikilo.” 39 Poyankha iye anawauza kuti: “M’badwo woipa komanso wacigololo* ukufunabe cizindikilo, koma sudzapatsidwa cizindikilo ciliconse kupatulapo cizindikilo ca mneneli Yona. 40 Pakuti monga mmene Yona anakhalila m’mimba mwa cinsomba masiku atatu usana na usiku, nayenso Mwana wa munthu adzakhala mu mtima wa dziko lapansi masiku atatu usana na usiku. 41 Anthu a ku Ninive adzauka pa Tsiku la Ciweluzo pamodzi na m’badwo uwu, ndipo adzautsutsa, cifukwa analapa atamva ulaliki wa Yona. Koma onani! Winawake woposa Yona ali pano. 42 Mfumukazi ya kum’mwela idzaukitsidwa pa Tsiku la Ciweluzo pamodzi na m’badwo uwu ndipo idzautsutsa, cifukwa inacokela ku malekezelo a dziko lapansi n’kubwela kuti idzamve nzelu za Solomo. Koma onani! Winawake woposa Solomo ali pano.
43 “Mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, umadutsa m’malo opanda madzi kufuna-funa popumulila, koma supeza malo alionse. 44 Kenako umati, ‘Nibwelela m’nyumba yanga imene n’natulukamo,’ ndipo ukafika umapeza kuti m’nyumbamo mulibe aliyense, koma ni mopsela bwino komanso ni mokongoletsedwa. 45 Kenako umapita n’kukatenga mizimu ina 7 yoipa kwambili kuposa umenewo, ndipo yonse imaloŵa m’nyumbamo n’kumakhala mmenemo. Pamapeto pake, munthuyo amakhala woipa kwambili kuposa poyamba. Ni mmenenso zidzakhalila na m’badwo woipawu.”
46 Ali mkati molankhula na khamu la anthulo, abale ake na amayi ake anabwela n’kuimilila panja. Iwo anali kufuna kukamba naye. 47 Conco munthu wina anamuuza kuti: “Mphunzitsi! Mayi anu na abale anu aimilila panja afuna kukamba nanu.” 48 Poyankha Yesu anauza munthuyo kuti: “Kodi mayi anga ndani, nanga abale anga ndani?” 49 Pamenepo anatambasula dzanja lake n’kulata ophunzila ake. Kenako anati: “Ona! Awa ndiwo mayi anga na abale anga! 50 Pakuti aliyense wocita cifunilo ca Atate wanga amene ali kumwamba, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga, komanso mayi anga.”
13 Tsiku limenelo Yesu anacoka pa nyumbayo n’kukakhala pansi m’mbali mwa nyanja. 2 Ndiyeno khamu lalikulu la anthu linasonkhana kwa iye moti anakwela m’bwato n’kukhala pansi, ndipo anthu onsewo anaimilila m’mbali mwa nyanjayo. 3 Kenako anayamba kuwauza zinthu zambili mwa mafanizo, kuti: “Tamvelani! Munthu wina anapita kukafesa mbewu. 4 Pamene anali kufesa mbewuzo, zina zinagwela m’mbali mwa msewu, ndipo mbalame zinabwela n’kuzidya. 5 Zina zinagwela pa miyala pamene panalibe dothi lokwanila, ndipo zinamela mwamsanga cifukwa nthaka inali yosazama. 6 Koma dzuŵa litatentha zinaŵauka, kenako zinauma cifukwa zinalibe mizu. 7 Mbewu zina zinagwela pa minga, ndipo mingazo zitakula, zinalepheletsa mbewuzo kukula. 8 Koma mbewu zina zinagwela pa nthaka yabwino, ndipo zinayamba kubala zipatso, mbewu iyi zipatso 100, ina 60, inanso 30. 9 Ali na matu amve.”
10 Conco ophunzila ake anabwela na kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mumalankhula nawo mwa mafanizo?” 11 Poyankha iye anati: “Inu mwapatsidwa mwayi womvetsa zinsinsi za Ufumu wa kumwamba, koma iwo sanapatsidwe mwayi umenewo. 12 Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zambili, ndipo adzakhala na zoculuka, koma aliyense amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene ali nazo. 13 Ndiye cifukwa cake nimalankhula nawo mwa mafanizo. Pakuti kuona amaona, koma kuona kwawo n’kopanda phindu, ndipo kumva amamva koma kumva kwawo n’kopanda phindu komanso samvetsa tanthauzo lake. 14 Ndipo ulosi wa Yesaya ukukwanilitsidwa pa iwo. Ulosiwo umati: ‘Kumva mudzamva ndithu, koma simudzamvetsa tanthauzo lake. Kuona mudzaona ndithu, koma simudzazindikila zimene mukuona. 15 Pakuti anthu awa aumitsa mitima yawo, ndipo amva na matu awo koma osacitapo kanthu, komanso atseka maso awo. Acita zimenezi kuti asaone na maso awo komanso kuti asamve na matu awo. Zotulukapo zake n’zakuti samvetsa tanthauzo lake m’mitima yawo n’kutembenuka kuti ine niwacilitse.’
16 “Koma inu ndinu odala cifukwa maso anu amaona, ndipo matu anu amamva. 17 Pakuti ndithu nikukuuzani, kuti aneneli ambili komanso anthu olungama, anali kulakalaka kuona zimene inu mukuona na kumva zimene inu mukumva.
18 “Tsopano mvetselani tanthauzo la fanizo la munthu wofesa mbewu uja. 19 Munthu aliyense akamva mawu a Ufumu koma osamvetsa tanthauzo lake, woipayo amabwela n’kucotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Izi ndizo mbewu zimene zinagwela m’mbali mwa msewu. 20 Mbewu zogwela pa miyala ni munthu amene amamva mawu, n’kuwalandila mwacimwemwe nthawi yomweyo. 21 Ngakhale n’conco, mawuwo sazika mizu mwa iye,* koma amapitiliza kwa kanthawi. Ndipo mazunzo kapena cisautso cikabwela cifukwa ca mawuwo, amapunthwa nthawi yomweyo. 22 Mbewu zogwela pa minga ni munthu amene amamva mawu, koma nkhawa za nthawi ino* komanso cinyengo camphamvu ca cuma, zimalepheletsa mbewuzo kukula, ndipo sizibala zipatso. 23 Koma mbewu zogwela pa nthaka yabwino ni munthu amene amamva mawu na kumvetsa tanthauzo lake, amene amabaladi zipatso, uyu zipatso 100, wina 60, komanso wina 30.”
24 Iye anawauzanso fanizo lina. Anati: “Ufumu wa kumwamba uli ngati munthu amene anafesa mbewu yabwino m’munda wake. 25 Anthu ali m’tulo, mdani wake anabwela n’kufesa namsongole m’munda wa tiliguwo, kenako anapita. 26 Mmelawo utakula na kutulutsa ngalangala, nayenso namsongole anaonekela. 27 Conco akapolo a mwinimunda uja anabwela n’kumufunsa kuti, ‘Ambuye, sipaja munafesa mbewu yabwino m’munda mwanu? Nanga namsongole wacokela kuti?’ 28 Poyankha iye anawauza kuti, ‘Munthu wina wodana nane ndiye anacita zimenezi.’ Akapolowo anamufunsa kuti, ‘Ndiye kodi tipite tikamuzule namsongoleyo?’ 29 Iye anawayankha kuti, ‘Ayi, kuopela kuti pozula namsongoleyo, mungazulile pamodzi na tiligu. 30 Zilekeni zikulile pamodzi mpaka nthawi yokolola, ndipo m’nyengo yokolola nidzauza okololawo kuti: Coyamba sonkhanitsani namsongole n’kumumanga mitolo-mitolo kuti akatenthedwe, kenako sonkhanitsani tiligu n’kumuika mu nkhokwe yanga.’”
31 Iye anawauzanso fanizo lina kuti: “Ufumu wa kumwamba uli ngati kanjele ka mpilu kamene munthu anatenga n’kukabyala m’munda wake. 32 Kanjele kameneka nikakang’ono kwambili pa mbewu zonse. Koma kamakula kuposa mbewu zonse za kudimba n’kukhala mtengo, moti mbalame za mumlengalenga zimapeza malo okhala m’nthambi zake.”
33 Anawauzanso fanizo lina kuti: “Ufumu wa kumwamba uli ngati zofufumitsa zimene mayi wina anatenga n’kuzisakaniza na ufa wokwana mbale zitatu zikulu-zikulu zopimila, ndipo mtanda wonsewo unafufuma.”
34 Yesu analankhula zinthu zonsezi na khamulo mwa mafanizo. Ndithudi sanalankhule nawo popanda fanizo, 35 kuti mawu amene ananenedwa kudzela mwa mneneli akwanilitsidwe, akuti: “Nidzatsegula pakamwa panga na kunena mafanizo. Nidzalengeza zinthu zimene zakhala zobisika kucokela pa ciyambi.”*
36 Ndiyeno atauza khamu la anthulo kuti lizipita analoŵa m’nyumba. Ophunzila ake anabwela kwa iye n’kunena kuti: “Tifotokozeleni tanthauzo la fanizo lija la namsongole m’munda.” 37 Iye anawayankha kuti: “Wofesa mbewu yabwino ni Mwana wa munthu; 38 ndipo mundawo ni dzikoli. Mbewu yabwino ni ana a Ufumu, koma namsongole ni ana a woipayo, 39 ndipo mdani amene anafesa namsongoleyo ni Mdyelekezi. Nthawi yokolola ndiyo cimalizilo ca nthawi ino,* ndipo okololawo ni angelo. 40 Conco monga mmene namsongole amamusonkhanitsila pamodzi na kumutentha pamoto, ni mmenenso zidzakhalila pa cimalizilo ca nthawi ino.* 41 Mwana wa munthu adzatumiza angelo ake amene adzacotsa mu Ufumu wake zinthu zonse zopunthwitsa kuphatikizapo anthu osamvela malamulo, 42 ndipo adzawaponya mu ng’anjo ya moto. Kumeneko azikalila na kukukuta mano. 43 Pa nthawiyo olungama adzawala kwambili ngati dzuŵa mu Ufumu wa Atate wawo. Ali na matu amve.
44 “Ufumu wa kumwamba uli ngati cuma cobisika m’munda, cimene munthu wina anapeza n’kucibisa. Ndipo cifukwa ca cimwemwe cimene anali naco, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.
45 “Komanso Ufumu wa kumwamba uli ngati wamalonda woyenda-yenda amene anali kufuna-funa ngale zabwino. 46 Atapeza ngale imodzi yamtengo wapatali anapita, ndipo mwamsanga anagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula ngaleyo.
47 “Ndiponso Ufumu wa kumwamba uli ngati khoka lalikulu limene linaponyedwa m’nyanja, ndipo linasonkhanitsa nsomba za mitundu-mitundu. 48 Litadzala analikokela ku mtunda, ndipo atakhala pansi anasonkhanitsa nsomba zabwino n’kuziika m’madengu, koma zoipa anazitaya. 49 Ni mmenenso zidzakhalila pa mapeto a nthawi ino.* Angelo adzapita n’kukacotsa oipa pakati pa olungama, 50 ndipo adzawaponya mu ng’anjo ya moto. Kumeneko azikalila na kukukuta mano.
51 “Kodi mwamvetsa tanthauzo la zinthu zonsezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde.” 52 Ndiyeno anawauza kuti: “Poti zili telo, mphunzitsi aliyense wa anthu amene waphunzitsidwa za Ufumu wa kumwamba, ali ngati mwininyumba, amene amatulutsa zinthu zatsopano komanso zakale mosungila cuma cake.”
53 Yesu atatsiliza kuwauza mafanizo amenewa anacoka kumeneko. 54 Atafika m’dela la kwawo anayamba kuphunzitsa anthu m’sunagoge wawo, moti anthuwo anadabwa kwambili ndipo anati: “Kodi munthu ameneyu anazitenga kuti nzelu na nchito zamphamvu zimenezi? 55 Kodi ameneyu si mwana wa kalipentala uja? Kodi mayi ake si Mariya, ndipo abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni na Yudasi? 56 Komanso alongo ake onse sitili nawo konkuno? Nanga zonsezi anazitenga kuti?” 57 Conco anayamba kupunthwa cifukwa ca iye. Koma Yesu anawauza kuti: “Mneneli salemekezedwa kwawo kapena panyumba pake, koma kwina.” 58 Cotelo sanacite nchito zambili zamphamvu kumeneko cifukwa ca kusoŵa cikhulupililo kwawo.
14 Pa nthawiyo, Herode wolamulila cigawo ca Galileya anamva za Yesu. 2 Ndipo anauza atumiki ake kuti: “Ameneyu ni Yohane M’batizi. Anaukitsidwa kwa akufa, ndiye cifukwa cake akucita nchito zamphamvu zimenezi.” 3 Herode* anali atagwila Yohane, anam’manga, na kukamuponya m’ndende cifukwa ca Herodiya mkazi wa Filipo m’bale wake. 4 Pakuti Yohane anali kumuuza kuti: “N’kosaloleka kuti inu mumukwatile mkaziyu.” 5 Koma ngakhale kuti Herode anali kufuna kupha Yohane, anali kuopa khamu la anthu cifukwa iwo anali kumuona kuti ni mneneli. 6 Koma pokondwelela tsiku la kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pa cikondweleloco. Ndipo Herode anakondwela ngako na kavinidwe kake, 7 moti anamulonjeza mocita kulumbila kuti adzamupatsa ciliconse cimene angamupemphe. 8 Kenako mtsikanayo, mayi ake atacita kumuuza zoti apemphe anati: “Nipatseni mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.” 9 Mfumuyo inamva cisoni cifukwa ca zimenezi. Koma cifukwa ca lumbilo lake komanso anthu amene anali kudya naye, analamula kuti mutuwo upelekedwe. 10 Conco anatuma munthu kukamudula mutu Yohane m’ndende. 11 Mutuwo anaubweletsa m’mbale n’kuupeleka kwa mtsikanayo, ndipo iye anaupeleka kwa amayi ake. 12 Pambuyo pake ophunzila ake anabwela n’kutenga mtembo wake kukauika m’manda. Kenako anapita kukauza Yesu. 13 Yesu atamva zimenezi anakwela bwato n’kucoka kupita ku malo opanda anthu kuti akakhale kwayekha. Koma khamu la anthu litamva zimenezo linam’tsatila wapansi kucokela m’mizinda yawo.
14 Atafika ku mtunda anaona khamu lalikulu la anthu, ndipo anawamvela cisoni na kucilitsa odwala awo. 15 Koma madzulo ophunzila ake anafika kwa iye n’kumuuza kuti: “Kuno tili n’kopanda anthu ndipo nthawi yatha kale. Auzeni anthuwa azipita, akaloŵe m’midzi kuti akadzigulile cakudya.” 16 Koma Yesu anawauza kuti: “Iwo safunika kucoka; inuyo muwapatse cakudya.” 17 Iwo anamuyankha kuti: “Tilibe ciliconse pano, kupatulapo mitanda isanu ya mkate na nsomba ziŵili.” 18 Iye anati: “Zibweletseni kuno.” 19 Ndiyeno anauza khamu la anthulo kuti likhale pansi paudzu. Kenako anatenga mitanda ya mkate isanu ija na nsomba ziŵili zija, ndipo atayang’ana kumwamba anapempha dalitso. Pambuyo pake ananyema-nyema mitandayo n’kuipeleka kwa ophunzila ake, ndipo iwo anagaŵila khamulo. 20 Cotelo onse anadya n’kukhuta. Zotsala anazitola-tola ndipo zinadzala matadza 12. 21 Amene anadya anali amuna pafupi-fupi 5,000, osaŵelengelako akazi komanso ana aang’ono. 22 Ndiyeno mwamsanga anauza ophunzila ake kuti akwele bwato na kupita ku tsidya lina la nyanja, pamene iye anali kuuza anthu kuti azipita.
23 Atauza khamulo kuti lizipita, Yesu anakwela m’phili yekha-yekha kukapemphela. Anakhalabe yekha kumeneko mpaka kunada. 24 Pa nthawiyi n’kuti bwatolo lapita kutali* pakati pa nyanja. Ophunzila ake anali kuvutika kuyendetsa bwatolo cifukwa linali kuwombedwa na mafunde, popeza kunali mphepo yamphamvu. 25 Koma pa nthawi ya ulonda wacinayi m’matandakuca,* iye anafika kwa iwo akuyenda pa madzi. 26 Ophunzilawo atamuona akuyenda pa nyanja, anacita mantha n’kunena kuti: “Ni cipuku!” Ndipo anafuula mwamantha. 27 Koma nthawi yomweyo Yesu anawauza kuti: “Limbani mtima! Ndine, musacite mantha.” 28 Poyankha Petulo anati: “Ambuye, ngati ndinudi, niuzeni niyende pamadzipa kubwela kwa inu.” 29 Iye anati: “Bwela!” Conco Petulo anatuluka m’bwatomo ndipo anayamba kuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu. 30 Koma atayang’ana cimphepo camphamvu anacita mantha. Ndipo atayamba kumila anakuwa, amvekele: “Ambuye, nipulumutseni!” 31 Mwamsanga Yesu anatambasula dzanja lake n’kumugwila, ndipo anamuuza kuti: “Wa cikhulupililo cocepa iwe, n’cifukwa ciyani wakayikila?” 32 Atakwela m’bwato cimphepoco cinaleka. 33 Ndiyeno amene anali m’bwatomo anamuŵelamila n’kunena kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.” 34 Ndipo anawolokela ku mtunda ku Genesareti.
35 Anthu a kumeneko atamuzindikila, anatumiza uthenga m’madela onse ozungulila, ndipo anthu anamubweletsela onse amene anali kudwala. 36 Iwo anamucondelela kuti angogwilako ulusi wopota wa m’mbali mwa covala cake cakunja, ndipo onse amene anagwila ulusiwo matenda awo anathelatu.
15 Ndiyeno Afarisi na alembi anabwela kwa Yesu kucokela ku Yerusalemu n’kumufunsa kuti: 2 “N’cifukwa ciyani ophunzila anu amanyozela miyambo ya makolo? Mwa citsanzo, iwo sasamba* m’manja akafuna kudya cakudya.”
3 Powayankha iye anati: “Nanga n’cifukwa ciyani inuyo mumaphwanya malamulo a Mulungu cifukwa ca miyambo yanu? 4 Mwa citsanzo Mulungu anati, ‘Uzilemekeza atate ako na amayi ako,’ komanso anati, ‘Aliyense wonyoza atate ake na amayi ake ayenela kuphedwa.’ 5 Koma inu mumati, ‘Aliyense wouza atate ake kapena amayi ake kuti: “Ciliconse cimene nili naco, cimene nikanakuthandizani naco ni mphatso yoyenela kupelekedwa kwa Mulungu,” 6 munthuyo asawalemekeze* n’komwe atate ake.’ Conco mwapangitsa mawu a Mulungu kukhala opanda phindu cifukwa ca miyambo yanu. 7 Onyenga inu, Yesaya analosela molondola za inu pamene anati: 8 ‘Anthu awa amanilemekeza na milomo yawo cabe, koma mitima yawo ili kutali na ine. 9 Iwo amanipembedza pacabe cifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu monga ziphunzitso za Mulungu.’” 10 Atakamba zimenezi, anaitana khamu la anthulo kuti libwele pafupi, ndipo anaŵauza kuti: “Mvetselani na kumvetsetsa tanthauzo lake: 11 Coloŵa m’kamwa mwa munthu si cimene cimamudetsa, koma cotuluka m’kamwa mwake n’cimene cimamudetsa.”
12 Ndiyeno ophunzilawo anabwela kwa iye n’kumuuza kuti: “Kodi mudziŵa kuti Afarisi akhumudwa na zimene mwakamba?” 13 Poyankha iye anati: “Mbewu iliyonse imene sinabyalidwe na Atate wanga wa kumwamba idzazulidwa. 14 Alekeni amenewo. Iwo ni atsogoleli akhungu. Cotelo ngati munthu wakhungu akutsogolela wakhungu mnzake, onse aŵili adzagwela m’dzenje.” 15 Petulo anati: “Timasulileni fanizo lija.” 16 Pamenepo Yesu anati: “Kodi inunso simukumvetsa mpaka pano? 17 Kodi simudziŵa kuti ciliconse coloŵa m’kamwa cimapita m’mimba, kenako cimakatayidwa ku cimbudzi? 18 Koma zilizonse zotuluka pakamwa zimacokela mu mtima, ndipo zimenezo n’zimene zimaipitsa munthu. 19 Mwa citsanzo, mumtima mumatuluka maganizo oipa monga: zakupha, zacigololo, zaciwelewele,* zakuba, maumboni onama komanso zonyoza Mulungu. 20 Izi n’zimene zimadetsa munthu. Koma kudya cakudya cosasamba* m’manja sikudetsa munthu.”
21 Atacoka kumeneko, Yesu anapita ku cigawo ca Turo na Sidoni. 22 Ndiyeno mayi wina wa ku Foinike, wocokela m’cigawo cimeneco, anabwela kwa iye n’kufuula kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, nicitileni cifundo. Mwana wanga wamkazi wagwidwa na ciŵanda ndipo akuzunzika koopsa.” 23 Koma Yesu sanamuyankhe ciliconse. Conco, ophunzila ake anapita kwa iye n’kumuuza kuti: “Muuzeni azipita, cifukwa akufuulabe n’kumatilondola.” 24 Poyankha iye anati: “Ine sin’natumidwe kwa wina aliyense koma kwa nkhosa zosocela za mtundu wa Isiraeli.” 25 Koma mayiyo anafika pafupi na Yesu, ndipo anamugwadila n’kunena kuti: “Ambuye, nithandizeni!” 26 Iye anamuyankha kuti: “N’kosayenela kutenga cakudya ca ana n’kuponyela tuagalu.” 27 Mayiyo anati: “N’zoona Ambuye, koma ngakhale tuana twa agalu tumadya nyenyeswa zakugwa pa thebulo la ambuye awo.” 28 Ndiyeno Yesu anamuyankha kuti: “Mayi iwe, cikhulupililo cako n’cacikulu. Zimene wapempha zicitike.” Nthawi yomweyo mwana wake anacila.
29 Yesu atacoka kumeneko, anapita kufupi na nyanja ya Galileya, ndipo anakwela m’phili n’kukhala pansi. 30 Tsopano kunafika khamu lalikulu la anthu limene linamubweletsela anthu olemala, othyoka ziwalo, akhungu, osalankhula, na ena ambili. Iwo anaika anthuwo pafupi na mapazi ake ndipo iye anawacilitsa. 31 Khamulo linadabwa kwambili poona kuti osalankhula akulankhula, othyoka ziwalo akukhala bwino, olemala akuyenda, komanso osaona akuona. Ndipo iwo anatamanda Mulungu wa Isiraeli.
32 Koma Yesu anaitana ophunzila ake n’kuwauza kuti: “Nikuwamvela cifundo anthuwa, cifukwa akhala nane masiku atatu osadya ciliconse. Sinifuna kuwauza kuti azipita na njala cifukwa angakomoke m’njila.” 33 Koma ophunzilawo anati: “Kodi tingapeze kuti cakudya cokwanila khamu lalikulu ngati ili kumalo opanda anthu kuno?” 34 Pamenepo Yesu anawafunsa kuti: “Muli na mitanda ingati ya mkate?” Iwo anati: “Tili nayo 7 na tunsomba toŵelengeka.” 35 Conco, anauza anthuwo kuti akhale pansi. 36 Ndiyeno anatenga mitanda 7 ija na tunsomba tuja n’kuyamika. Kenako ananyema-nyema mikateyo n’kuyamba kupatsa ophunzila ake pamodzi na tunsombato, ndipo iwo anagaŵila khamulo. 37 Onse anadya n’kukhuta, ndipo anatola-tola zotsala zokwana matadza 7 akulu-akulu. 38 Amene anadya anali amuna 4,000, osaŵelengelako akazi komanso ana. 39 Atauza anthuwo kuti azipita, anakwela bwato n’kupita ku cigawo ca Magadani.
16 Kenako Afarisi na Asaduki anafika kwa iye, ndipo pofuna kumuyesa anamupempha kuti awaonetse cizindikilo cocokela kumwamba. 2 Powayankha iye anati: “Pamene dzuŵa likuloŵa mumati, ‘Maŵa nyengo idzakhala bwino, cifukwa kumwamba kukuoneka psuu.’ 3 Ndipo m’maŵa mumakamba kuti, ‘Lelo kuzizila, ndipo kugwa mvula, cifukwa kumwamba kukuoneka psuu koma kuli mitambo.’ Mumadziŵa kumasulila maonekedwe a kumwamba koma simungathe kumasulila zizindikilo za nthawi ino. 4 M’badwo woipa komanso wacigololo* ukufunabe cizindikilo, koma sudzapatsidwa cizindikilo ciliconse kupatulapo cizindikilo ca Yona.” Atakamba zimenezi anacokapo n’kuwasiya.
5 Tsopano ophunzila ake anawolokela ku tsidya lina koma anaiŵala kunyamula mkate. 6 Yesu anawauza kuti: “Khalani maso ndipo samalani na zofufumitsa za Afarisi na Asaduki.” 7 Conco anayamba kukambilana kuti: “Sitinanyamule mitanda ya mkate pobwela kuno.” 8 Yesu anadziŵa zimene anali kukambilana, ndipo anawafunsa kuti: “A cikhulupililo cocepa inu, n’cifukwa ciyani mukukambilana zakuti mulibe mitanda ya mkate? 9 Kodi simukumvetsetsabe zimene nikutanthauza, kapena simukukumbukila mitanda isanu ya mkate imene anadya anthu 5,000, komanso kuculuka kwa matadza a zotsala zimene munasonkhanitsa? 10 Kapenanso simukukumbukila mitanda ya mkate 7 imene anadya anthu 4,000, komanso kuculuka kwa matadza akulu-akulu a zotsala zimene munasonkhanitsa? 11 Nanga n’cifukwa ciyani simukuzindikila kuti sinikunena za mkate? Koma samalani na zofufumitsa za Afarisi na Asaduki.” 12 Apa lomba ophunzilawo anamvetsa kuti anali kuwauza kuti asamale na ziphunzitso za Afarisi na Asaduki, osati na zofufumitsa za mkate.
13 Yesu atafika m’cigawo ca Kaisareya wa ku Filipi, anafunsa ophunzila ake kuti: “Kodi anthu amati Mwana wa munthu ndani?” 14 Iwo anayankha kuti: “Ena amati ni Yohane M’batizi, ena Eliya, komanso ena amati ni Yeremiya kapena mmodzi wa aneneli.” 15 Iye anawafunsanso kuti: “Nanga inu mumati ndine ndani?” 16 Simoni Petulo anayankha kuti: “Ndinu Khristu Mwana wa Mulungu wamoyo.” 17 Kenako Yesu anamuuza kuti: “Ndiwe wodala Simoni mwana wa Yona, cifukwa si munthu wakuululila zimenezi koma ni Atate wanga wa kumwamba. 18 Komanso nikukuuza kuti: Iwe ndiwe Petulo, ndipo pa thanthwe ili nidzamangapo mpingo wanga. Mageti a Manda* sizidzaugonjetsa. 19 Ine nidzakupatsa makiyi a Ufumu wa kumwamba. Ndipo ciliconse cimene udzamange pano pa dziko lapansi, cidzakhala citamangidwa kale kumwamba. Komanso ciliconse cimene udzamasule pa dziko lapansi, cidzakhala citamasulidwa kale kumwamba.” 20 Ndiyeno analamula ophunzila ake mwamphamvu kuti asauze aliyense kuti iye ni Khristu.
21 Kuyambila nthawi imeneyo, Yesu anayamba kuuza ophunzila ake kuti ayenela kupita ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa m’njila zosiyana-siyana na akulu, ansembe aakulu, komanso alembi. Kenako adzaphedwa, ndipo pa tsiku lacitatu adzaukitsidwa. 22 Petulo atamva izi anatengela Yesu pambali n’kuyamba kumudzudzula kuti: “Dzikomeleni mtima Ambuye. Ndipo izi sizidzakucitikilani ayi.” 23 Koma Yesu anatembenuka n’kuuza Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga Satana! Ndiwe copunthwitsa kwa ine, cifukwa zimene ukuganiza si maganizo a Mulungu koma maganizo a anthu.”
24 Kenako Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Ngati munthu afuna kunitsatila adzikane yekha, na kunyamula mtengo wake wozunzikilapo* n’kupitiliza kunitsatila. 25 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense wotaya moyo wake cifukwa ca ine adzaupeza. 26 Kunena zoona, kodi pali phindu lanji munthu atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma n’kutaya moyo wake? Kapena munthu angapeleke ciyani cosinthanitsa na moyo wake? 27 Pakuti Mwana wa munthu adzabwela mu ulemelelo wa Atate wake pamodzi na angelo ake, ndipo adzabwezela aliyense malinga na zocita zake. 28 Ndithu nikukuuzani kuti pali ena pano, amene sadzalaŵa imfa ngakhale pang’ono, mpaka coyamba ataona Mwana wa munthu akubwela mu Ufumu wake.”
17 Patapita masiku 6, Yesu anatenga Petulo, Yakobo na m’bale wake Yohane, n’kukwela nawo m’phili lalitali kwaokha-okha. 2 Kumeneko, iye anasandulika pamaso pawo. Nkhope yake inawala ngati dzuŵa, ndipo zovala zake zakunja zinawala kwambili.* 3 Kenako ophunzilawo anaona Mose na Eliya akulankhula na Yesu. 4 Tsopano Petulo anauza Yesu kuti: “Ambuye, zili bwino kuti ife tizikhala pom’pano. Ngati mufuna ningakhome matenti atatu pano. Ina yanu, ina ya Mose, komanso ina ya Eliya.” 5 Mawu ake akali m’kamwa, mtambo wowala unawaphimba. Kenako kunamveka mawu ocokela mu mtambomo akuti: “Uyu ni Mwana wanga wokondedwa amene nimakondwela naye. Muzimumvela.” 6 Ophunzilawo atamva mawu amenewa, anagwada n’kuŵelama mpaka nkhope zawo pansi, ndipo anacita mantha kwambili. 7 Kenako Yesu anawayandikila n’kuwagwila, ndipo anati: “Ŵelamukani. Musaope.” 8 Ataŵelamuka sanaone aliyense koma Yesu yekha. 9 Pamene anali kutsika m’philimo Yesu anawalamula kuti: “Musauzeko aliyense za masomphenyawa mpaka Mwana wa munthu ataukitsidwa kwa akufa.”
10 Koma ophunzilawo anamufunsa kuti: “Nanga n’cifukwa ciyani alembi amakamba kuti, Eliya ayenela kubwela coyamba?” 11 Poyankha Yesu anati: “Eliya akubweladi, ndipo adzabwezeletsa zinthu zonse. 12 Komabe, nikukuuzani kuti Eliya anabwela kale ndipo iwo sanamuzindikile, koma anamucita ciliconse cimene anali kufuna. Mofananamo, iwo adzazunza Mwana wa munthu.” 13 Pamenepo ophunzilawo anazindikila kuti anali kukamba nawo za Yohane M’batizi.
14 Iwo atafika kufupi na khamu la anthu, mwamuna wina anayandikila Yesu n’kumugwadila, ndipo anati: 15 “Ambuye, mucitileni cifundo mwana wanga wamwamuna, cifukwa ni wakhunyu ndipo akudwala kwambili. Nthawi zambili iye amagwela pa moto komanso pa madzi. 16 N’nabwela naye kwa ophunzila anu, koma alephela kumucilitsa.” 17 Yesu anayankha kuti: “Inu m’badwo wopanda cikhulupililo komanso wopotoka maganizo, kodi nikhalabe nanu mpaka liti? Kodi nikupilileni mpaka liti? Mubweletseni kuno.” 18 Ndiyeno Yesu anadzudzula ciŵandaco, ndipo cinatuluka mwa mnyamatayo moti anacila nthawi yomweyo. 19 Pambuyo pake ophunzilawo anapita kwa Yesu mwamseli n’kumufunsa kuti: “N’cifukwa ciyani ife tinalephela kutulutsa ciŵanda cija?” 20 Iye anati: “Cifukwa ca kucepa kwa cikhulupililo canu. Pakuti ndithu nikukuuzani kuti, mutakhala na cikhulupililo ngakhale cocepa ngati kanjele ka mpilu, mudzatha kuuza phili ili kuti, ‘coka pano upite apo,’ ndipo lidzacokadi. Palibe cimene cidzakhala cosatheka kwa inu.” 21 ——
22 Iwo atasonkhana ku Galileya Yesu anawauza kuti: “Mwana wa munthu adzapelekedwa m’manja mwa anthu. 23 Anthuwo adzamupha ndipo pa tsiku lacitatu adzaukitsidwa.” Ophunzila ake atamva zimenezi, anamva cisoni kwambili.
24 Atafika ku Kaperenao, anthu okhometsa msonkho wa madalakima aŵili anafika kwa Petulo n’kumufunsa kuti: “Kodi mphunzitsi wanu amakhoma msonkho wa madalakima aŵili?” 25 Iye anayankha kuti: “Inde.” Ndiyeno Petulo analoŵa m’nyumba, koma iye asanakambe ciliconse, Yesu anamufunsa kuti: “Simoni uganiza bwanji? Kodi mafumu a dziko amalandila misonkho kwa ndani? Kwa ana awo kapena kwa anthu ena?” 26 Atayankha kuti: “Kwa anthu ena,” Yesu anakamba kuti: “Ndiye kuti anawo sayenela kukhoma msonkho. 27 Koma kuti tisawakhumudwitse, pita ku nyanja ukaponye mbedza pamadzi. Nsomba yoyamba imene ukakole ukaitenge n’kuikanula kukamwa. Ndipo m’kamwamo ukapezamo ndalama ya siliva. Ukaitenge ukakhomele msonkho wanga na wako.”
18 Pa nthawi imeneyo ophunzila a Yesu anabwela kwa iye n’kumufunsa kuti: “Ndani maka-maka wamkulu kwambili mu Ufumu wa kumwamba?” 2 Pamenepo iye anaitana mwana wamng’ono n’kumuimika pakati pawo, 3 ndipo anati: “Ndithu nikukuuzani kuti simudzaloŵa mu Ufumu wa kumwamba ngati simutembenuka* n’kukhala ngati ana aang’ono. 4 Aliyense amene adzadzicepetsa ngati mwana wamng’ono uyu, ndiye wamkulu kwambili mu Ufumu wa kumwamba; 5 ndipo aliyense wolandila mwana wamng’ono ngati uyu cifukwa ca dzina langa, walandilanso ine. 6 Koma aliyense wopunthwitsa mmodzi wa ana aang’ono awa amene ali na cikhulupililo mwa ine, cingakhale bwino kwambili kum’mangilila cimwala ca mphelo m’khosi cimene bulu amaguza na kum’miza m’nyanja.
7 “Tsoka dzikoli cifukwa ca zopunthwitsa zake! N’zoona kuti zopunthwitsa zidzabwela ndithu, koma tsoka kwa munthu wobweletsa copunthwitsaco! 8 Cotelo, ngati dzanja lako kapena phazi lako limakupunthwitsa, ulidule n’kulitaya. Ni bwino kuti ukapeze moyo ulibe ciwalo cimodzi kapena uli wolemala, kusiyana n’kuti ukaponyedwe m’moto wosatha uli na manja onse aŵili, kapena mapazi onse aŵili. 9 Komanso ngati diso lako limakupunthwitsa, ulikolowole n’kulitaya. Ni bwino kuti ukapeze moyo uli na diso limodzi, kusiyana n’kuti ukaponyedwe ku Gehena* wa moto uli na maso onse aŵili. 10 Samalani kuti musanyoze mmodzi wa ana aang’ono awa, cifukwa nikukuuzani kuti angelo awo kumwamba, nthawi zonse amayang’ana nkhope ya Atate wanga amene ali kumwamba. 11 ——
12 “Muganiza bwanji? Ngati munthu ali na nkhosa 100, ndipo imodzi mwa nkhosazo yasocela, kodi sangasiye nkhosa 99 zija m’phili n’kupita kukafuna-funa nkhosa imodzi yosocelayo? 13 Ndithu nikukuuzani kuti akaipeza amakondwela nayo kwambili kuposa nkhosa 99 zija zimene sizinasocele. 14 Mofanana na zimenezi, Atate wanga* wa kumwamba safuna kuti ngakhale mmodzi wa ana aang’ono awa awonongeke.
15 “Komanso ngati m’bale wako wakucimwila, pita ukamufotokozele colakwa cake* panokha muli aŵili. Ngati wakumvela ndiye kuti wamubweza m’bale wakoyo. 16 Koma ngati sanakumvele upiteko na munthu mmodzi kapena aŵili kuti nkhani yonse ikatsimikizike pamaso pa* mboni ziŵili kapena zitatu. 17 Ngati iye sanawamvelenso uuze mpingo. Koma ngati mpingo nawonso sanaumvele, kwa iwe akhale ngati munthu wocokela ku mtundu wina komanso wokhometsa misonkho.
18 “Ndithu nikukuuzani kuti zilizonse zimene mudzamanga pano pa dziko lapansi, zidzakhala zitamangidwa kale kumwamba, komanso zilizonse zimene mudzamasula pano pa dziko lapansi, zidzakhala zitamasulidwa kale kumwamba. 19 Komanso ndithu nikukuuzani kuti, ngati aŵili a inu pano padziko lapansi mwagwilizana kuti mupemphe cinacake cofunika, Atate wanga wa kumwamba adzakupatsani cimeneco. 20 Pakuti pomwe aŵili kapena atatu asonkhana m’dzina langa, inenso nimakhala pakati pawo.”
21 Kenako Petulo anabwela kwa Yesu n’kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi m’bale wanga anganicimwile kangati ndipo ine n’kumukhululukila? Mpaka maulendo 7 kodi?” 22 Yesu anamuyankha kuti: “Nikukuuza kuti, osati maulendo 7 cabe ayi, koma mpaka maulendo 77.
23 “Ndiye cifukwa cake Ufumu wa kumwamba uli ngati mfumu imene inafuna kuti akapolo ake abweze nkhongole. 24 Atayamba kulandila nkhongolezo, atumiki ake anamubweletsela munthu wina amene anakongola matalente 10,000.* 25 Koma cifukwa cakuti sakanatha kubweza nkhongoleyo, mbuye wake analamula kuti munthuyo agulitsidwe pamodzi na mkazi wake, ana ake na zinthu zake zonse, kuti nkhongoleyo ibwezedwe. 26 Ndiyeno kapoloyo anagwada pansi ndipo anamuŵelamila n’kunena kuti, ‘Conde munilezeleko mtima, nidzakubwezelani zonse.’ 27 Mbuye wakeyo atamva zimenezi anamumvela cifundo, ndipo anamukhululukila nkhongole yake n’kumulola kuti apite. 28 Koma kapoloyo atatuluka, anakumana na kapolo mnzake amene anali na nkhongole yake yokwana madinari 100. Iye anamugwila na kuyamba kumukanyanga pakhosi, n’kumuuza kuti, ‘Nibwezele zonse zimene unakongola.’ 29 Pamenepo kapolo mnzakeyo anagwada pansi n’kuyamba kumucondelela kuti, ‘Conde munilezeleko mtima, nidzakubwezelani.’ 30 Koma sanalole zimenezo, ndipo anapita kukam’mangitsa kuti akakhale ku ndende mpaka atabweza nkhongole yonse. 31 Akapolo anzake ataona zimene zinacitikazo, anamva cisoni kwambili. Ndipo anapita kukafotokozela mbuye wawo zonse zimene zinacitika. 32 Ndiyeno mbuye wake uja anamuitana n’kumuuza kuti: ‘Kapolo woipa iwe! Ine n’nakukhululukila nkhongole yako yonse utanidandaulila. 33 Kodi iwenso sunayenele kumucitila cifundo kapolo mnzako, mmene ine n’nakucitila cifundo?’ 34 Pamenepo mbuye wakeyo anakwiya kwambili, moti anamupeleka kwa woyang’anila ndende kuti amuponye m’ndende mpaka atabweza nkhongole yonse. 35 Atate wanga wa kumwamba adzacitanso nanu cimodzimodzi, ngati aliyense wa inu sakhululukila m’bale wake na mtima wake wonse.”
19 Yesu atatsiliza kulankhula zimenezi, anacoka ku Galileya n’kupita ku madela a kumalile kwa Yudeya, ku tsidya la Yorodani. 2 Khamu lalikulu la anthu linamutsatila, ndipo iye anawacilitsa kumeneko.
3 Ndiyeno Afarisi anabwela kwa iye, ndipo pofuna kumuyesa anamufunsa kuti: “Kodi n’kololeka mwamuna kusudzula mkazi wake pa cifukwa ciliconse?” 4 Yesu anayankha kuti: “Kodi simunaŵelenge kuti amene analenga anthu paciyambi anawalenga mwamuna na mkazi, 5 n’kunena kuti: ‘Pa cifukwa cimeneci, mwamuna adzasiya atate ake na amayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo aŵiliwo adzakhala thupi limodzi? 6 Conco iwo salinso aŵili koma thupi limodzi. Cotelo cimene Mulungu wacimanga pamodzi munthu asacilekanitse.” 7 Iwo anamufunsa kuti: “Nanga n’cifukwa ciyani Mose analamula kuti mwamuna azipeleka cikalata ca cisudzulo kwa mkazi wake n’kumuleka?” 8 Iye anawauza kuti: “Mose anakulolani kusudzula akazi anu cifukwa ca unkhutukumve wanu. Koma sizinali conco kucokela pa ciyambi. 9 Ine nikukuuzani kuti aliyense wosudzula mkazi wake, osati pa cifukwa ca ciwelewele,* n’kukwatila mkazi wina, wacita cigololo.”
10 Ndiyeno ophunzila ake anati: “Ngati umu ni mmene zilili pakati pa mwamuna na mkazi wake, cili bwino kusakwatila.” 11 Iye anawauza kuti: “Si anthu onse amene angathe kucita zimenezi, koma okhawo amene ali na mphatsoyo. 12 Pakuti ena sakwatila cifukwa anabadwa telo, ndipo ena sakwatila cifukwa anacita kufulidwa. Koma ena anasankha kukhala osakwatila cifukwa ca Ufumu wa kumwamba. Amene angathe kutelo acite zimenezi.”
13 Kenako anthu anamubweletsela ana aang’ono kuti awaike manja na kuwapemphelela, koma ophunzila ake anawadzudzula. 14 Komabe Yesu anawauza kuti: “Alekeni anawo abwele kwa ine musawaletse, cifukwa Ufumu wa kumwamba ni wa anthu ngati amenewa.” 15 Ndipo ataika manja ake pa iwo anacoka kumeneko.
16 Tsopano munthu wina anapita kwa iye n’kumufunsa kuti: “Mphunzitsi, n’ciyani cabwino cimene niyenela kucita kuti nikapeze moyo wosatha?” 17 Yesu anamuyankha kuti: “N’cifukwa ciyani ukunifunsa za cimene cili cabwino? Pali mmodzi yekhayo wabwino. Koma ngati ufuna kukapeza moyo wosatha, uzitsatila malamulo a Mulungu nthawi zonse.” 18 Iye anamufunsa kuti: “Malamulo ati?” Yesu anati: “Usaphe munthu, usacite cigololo, usabe, usapeleke umboni wonama, 19 uzilemekeza atate ako na amayi ako, komanso uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” 20 Mnyamatayo anayankha kuti: “Nakhala nikutsatila malamulo onsewa, nanga n’ciyaninso cina cimene nikupeleŵela?” 21 Yesu anamuuza kuti: “Ngati ufuna kukhala wangwilo,* pita ukagulitse zinthu zako ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatelo udzakhala na cuma kumwamba. Kenako ubwele udzakhale wotsatila wanga.” 22 Mnyamatayo atamva zimenezi, anacoka ali wacisoni cifukwa anali na katundu wambili. 23 Pamenepo Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Ndithu nikukuuzani kuti cidzakhala covuta munthu wolemela kuloŵa mu Ufumu wa kumwamba. 24 Komanso nikukuuzani kuti n’cosavuta ngamila kuloŵa pa diso la singano, kusiyana n’kuti munthu wolemela akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”
25 Ophunzilawo atamva zimenezi anadabwa kwambili, ndipo anati: “Ndiye pali amene angapulumuke ngati?” 26 Yesu anawayang’anitsitsa n’kuwauza kuti: “Kwa anthu izi n’zosathekadi, koma kwa Mulungu zonse n’zotheka.”
27 Ndiyeno Petulo poyankha anati: “Taonani! Ife tasiya zinthu zathu zonse n’kukutsatilani, kodi tidzapeza ciyani?” 28 Yesu anawauza kuti: “Ndithu nikukuuzani kuti pa nthawi ya kulenganso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pa mpando wake wacifumu waulemelelo, inu amene mwanitsatila mudzakhala pa mipando 12 yacifumu, n’kumaweluza mafuko 12 a Isiraeli. 29 Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, abale, alongo, atate, amayi, ana, kapena minda cifukwa ca dzina langa, adzalandila zoculuka kuwilikiza maulendo 100, komanso adzapeza moyo wosatha.
30 “Koma ambili amene ni oyamba adzakhala othela, ndipo othela adzakhala oyamba.
20 “Ufumu wa kumwamba uli ngati mwinimunda wa mpesa amene analaŵilila m’mamaŵa kukafuna aganyu kuti akagwile nchito m’munda wake wa mpesa. 2 Atapangana nawo aganyuwo malipilo a dinari imodzi pa tsiku, anawatumiza ku munda wake wa mpesa. 3 Ca m’ma 9 koloko m’maŵa,* anapitanso kukafuna aganyu ena, ndipo anaona ena atangoimilila mu msika kusoŵa nchito. 4 Conco iye anawauza kuti, ‘Inunso pitani m’munda wanga wa mpesa ndipo nidzakupatsani malipilo oyenelela.’ 5 Iwo anapitadi. Ndiyeno ca m’ma 12 koloko masana* komanso ca m’ma 3 koloko masana,* mwinimunda uja anapitanso kukacita cimodzimodzi. 6 Pamapeto pake, ca m’ma 5 koloko madzulo,* anapitanso ku msika kuja, ndipo anapeza anthu enanso atangoimilila. Iye anawafunsa kuti, ‘N’cifukwa ciyani mwangoimilila pano tsiku lonse osagwila nchito?’ 7 Iwo anayankha kuti, ‘Cifukwa palibe amene watipatsa ganyu.’ Iye anawauza kuti, ‘Inunso pitani m’munda wanga wa mpesa.’
8 “Madzulo, mwinimunda uja anaitana kapitawo wa aganyu aja n’kumuuza kuti, ‘Itana aganyu aja uwapatse malipilo awo. Uyambe na othela utsilizile oyamba.’ 9 Anthu amene anayamba kugwila nchito pa ola la 11 aja atabwela, aliyense wa iwo analandila dinari imodzi. 10 Ndiye oyamba aja atabwela, anaganiza kuti alandila malipilo oculuka, koma nawonso analandila dinari imodzi-imodzi. 11 Aganyuwo atalandila malipilo awo, anayamba kudandaulila mwinimunda uja 12 kuti, ‘Othelawa angogwila nchito ola limodzi lokha, koma mwawapatsa malipilo ofanana na ife amene takhaula nayo nchito tsiku lonse pa dzuŵa la phwe!’ 13 Koma anauza mmodzi wa iwo kuti, ‘Bwanawe, sin’nakulakwile ciliconse. Tinagwilizana kuti malipilo ako ni dinari imodzi si conco? 14 Tenga malipilo ako uzipita. Nifuna kupatsa othelawa malipilo olingana na ako. 15 Kodi nilibe ufulu wocita zimene nifuna na zinthu zanga? Kapena diso lako lacita kaduka* cifukwa ndine wabwino?’* 16 Conco, othela adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala othela.”
17 Ali m’njila kupita ku Yerusalemu, Yesu anatengela ophunzila ake 12 aja pambali n’kuwauza kuti: 18 “Lomba tikupita ku Yerusalemu. Kumeneko Mwana wa munthu akapelekedwa kwa ansembe aakulu na alembi. Iwo adzamuweluza kuti aphedwe, 19 komanso adzamupeleka kwa anthu a mitundu ina kuti akamucite zacipongwe, akamukwapule na kumuphela pa mtengo. Ndipo pa tsiku lacitatu adzaukitsidwa.”
20 Kenako, mkazi wa Zebedayo anafika kwa iye na ana ake aamuna, ndipo anamuŵelamila pofuna kumupempha cinacake. 21 Yesu anamufunsa kuti: “Mufuna ciyani mayi?” Iye anayankha kuti: “Lonjezani kuti mu Ufumu wanu, ana anga aŵiliwa adzakhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja, wina ku dzanja lanu lamanzele.” 22 Yesu anayankha kuti: “Simudziŵa cimene mukupempha. Kodi mungamwe za m’kapu zimene ine natsala pang’ono kumwa?” Iwo anati: “Inde tingamwe.” 23 Iye anawauza kuti: “Za m’kapu yanga mudzamwadi, koma kusankha munthu wokakhala ku dzanja langa lamanja kapena lamanzele, si udindo wanga. Atate wanga ndiwo adzapeleka malo amenewo kwa anthu amene anawakonzela malowo.”
24 Ophunzila 10 enawo atamva zimenezi, anakwiya kwambili na amuna aŵili apacibalewo. 25 Koma Yesu anawaitana n’kuwauza kuti: “Inu mukudziŵa kuti olamulila a anthu a mitundu ina amapondeleza anthu awo, ndipo akulu-akulu amaonetsa mphamvu zawo pa iwo. 26 Siziyenela kukhala conco pakati panu. Koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu, akhale mtumiki wanu. 27 Ndipo aliyense wofuna kukhala woyamba pakati panu, akhale kapolo wanu. 28 Mofanana na zimenezi, Mwana wa munthu sanabwele kudzatumikilidwa koma kudzatumikila, komanso kudzapeleka moyo wake dipo kuti awombole anthu ambili.”
29 Pamene iwo anali kutuluka mu mzinda wa Yeriko, khamu lalikulu la anthu linamutsatila. 30 Ndiyeno amuna aŵili akhungu amene anali atakhala pansi m’mbali mwa msewu anamva kuti Yesu akudutsa, ndipo anafuula kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, ticitileni cifundo!” 31 Pamenepo khamu la anthulo linawadzudzula kuti akhale cete. Koma m’pamene iwo anafuula kwambili kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, ticitileni cifundo!” 32 Conco Yesu anaima n’kuwaitana, ndipo anati: “Mufuna nikucitileni ciyani?” 33 Iwo anati: “Ambuye, titseguleni maso.” 34 Atagwidwa na cifundo, Yesu anagwila m’maso mwawo. Nthawi yomweyo akhunguwo anayambanso kuona ndipo anam’tsatila.
21 Iwo atayandikila ku Yerusalemu, anafika ku Betefage pa Phili la Maolivi. Kenako Yesu anatuma ophunzila ake aŵili 2 n’kuwauza kuti: “Pitani m’mudzi uwo, ndipo mukakangoloŵamo, mukapeza bulu atam’mangilila pamodzi na mwana wake wamphongo. Mukawamasule, n’kuwabweletsa kwa ine. 3 Munthu aliyense akakakufunsani ciliconse, mukanene kuti, ‘Ambuye akuwafuna.’ Ndipo nthawi yomweyo akawatumiza.”
4 Zimenezi zinacitikadi kuti mawu amene ananenedwa kudzela mwa mneneli akwanilitsidwe, akuti: 5 “Uza mwana wamkazi wa Ziyoni kuti: ‘Taona! Mfumu yako ikubwela kwa iwe. Ni yofatsa, ndipo yakwela pa bulu, inde, mwana wamphongo wa bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.’”
6 Conco ophunzilawo anapita, ndipo anacita ndendende zimene Yesu anawauza. 7 Anabwela naye buluyo pamodzi na mwana wake. Kenako anayanzika zovala zawo pa abuluwo, ndipo Yesu anakwelapo. 8 Anthu ambili m’khamulo anayanzika zovala zawo zakunja mu msewu, ndipo ena anali kudula nthambi za mitengo n’kuziyala mu msewu. 9 Komanso khamu la anthu limene linali patsogolo na pambuyo pake linali kufuula kuti: “M’pulumutseni Mwana wa Davide! Wodalitsika ni iye wobwela m’dzina la Yehova! M’pulumutseni inu amene muli kumwambamwambako!”
10 Ndiyeno ataloŵa mu Yerusalemu, mumzinda wonsewo munakhala ciphokoso. Ena anali kufunsa kuti: “Ndani ameneyu?” 11 Khamulo linali kuyankha kuti: “Ameneyu ni mneneli Yesu, wocokela ku Nazareti, ku Galileya!”
12 Yesu analoŵa m’kacisi na kupitikitsila panja onse omwe anali kugulitsa na kugula zinthu m’kacisimo. Komanso anagudubula matebulo a osintha ndalama na mabenchi a ogulitsa nkhunda. 13 Ndipo anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzachedwa nyumba yopemphelelamo,’ koma inu mukuisandutsa phanga la acifwamba.” 14 Komanso anthu akhungu na olemala anabwela kwa iye m’kacisimo, ndipo anawacilitsa.
15 Ansembe aakulu na alembi ataona zinthu zodabwitsa zimene iye anacita, ndiponso ataona anyamata amene anali kufuula kuti, “M’pulumutseni Mwana wa Davide!” anakwiya kwambili, 16 ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ukumva zimene awa akukamba?” Yesu anawayankha kuti: “Inde. Kodi simunaŵelengepo mawu akuti, ‘Mwacititsa pakamwa pa ana na makanda kulankhula mawu acitamando?” 17 Ndiyeno anawasiya n’kutuluka mu mzindawo kupita ku Betaniya, ndipo anagona kumeneko.
18 Akubwelela ku mzinda wa Yerusalemu m’mamaŵa, anamva njala. 19 Ataona mtengo wa mkuyu m’mbali mwa msewu, anapita komweko, koma sanapezemo ciliconse. Anangopezamo masamba okha-okha. Conco anauza mtengowo kuti: “Kuyambila lelo sudzabalanso zipatso.” Ndipo mtengo wa mkuyuwo unafota nthawi yomweyo. 20 Ophunzilawo ataona zimenezi anadabwa kwambili, ndipo anati: “Zatheka bwanji kuti mtengo wa mkuyuwu ufote nthawi yomweyi?” 21 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Ndithu nikukuuzani kuti, ngati muli na cikhulupililo ndipo simukayika, mudzatha kucita zimene nacita ku mtengo wa mkuyuwu. Ndiponso kuposa pamenepa mudzatha kuuza phili ili kuti, ‘Nyamuka, ukadziponye m’nyanja,’ ndipo zidzacikadi. 22 Zilizonse zimene mudzapempha m’mapemphelo anu, mudzalandila ngati muli na cikhulupililo.”
23 Yesu ataloŵa m’kacisi, ansembe aakulu na akulu anabwela kwa iye pamene anali kuphunzitsa n’kumufunsa kuti: “Kodi ulamulilo wocita zimenezi munautenga kuti? Nanga ndani anakupatsani ulamulilo umenewu?” 24 Yesu anawayankha kuti: “Inenso nikufunsani cinthu cimodzi. Mukaniyankha, inenso nikuuzani kumene n’natenga ulamulilo wocita zimenezi: 25 Kodi ubatizo wa Yohane unacokela kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?” Koma iwo anayamba kukambilana, n’kumati: “Tikanena kuti, ‘Unacokela kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga n’cifukwa ciyani simunamukhulupilile?’ 26 Komanso sitingakambe kuti, ‘Unacokela kwa anthu,’ cifukwa tikuopa khamu la anthuli popeza onse amakhulupilila kuti Yohane anali mneneli.” 27 Conco pomuyankha Yesu, iwo anati: “Sitidziŵa.” Yesu anati: “Inenso sinikuuzani kumene n’natenga ulamulilo wocita zimenezi.
28 “Muganiza bwanji? Munthu wina anali na ana aŵili. Ndipo anapita kwa mwana woyamba n’kumuuza kuti, ‘Mwanawe, lelo upite kukagwila nchito m’munda wa mpesa.’ 29 Poyankha iye anati, ‘Sinipita,’ koma pambuyo pake anamva cisoni ndipo anapita. 30 Anapita kwa waciŵili n’kumuuzanso cimodzimodzi. Iye poyankha anati, ‘Nipita atate,’ koma sanapite. 31 Pa ana aŵiliwa, ndani anacita cifunilo ca atate ake?” Iwo anati: “Woyamba uja.” Ndiyeno Yesu anati: “Ndithu nikukuuzani kuti okhometsa misonkho na mahule akukusiyani m’mbuyo n’kukaloŵa mu Ufumu wa Mulungu. 32 Pakuti Yohane anabwela kwa inu n’kukuonetsani njila ya cilungamo, koma simunam’khulupilile. Komabe, okhometsa misonkho na mahule anam’khulupilila. Koma ngakhale kuti inu munaona zimenezi, simunamve cisoni pambuyo pake n’kusintha maganizo anu kuti mum’khulupilile.
33 “Mvelani fanizo lina: Panali munthu wina amene anali na munda. M’mundawo analimamo mphesa n’kumanga mpanda kuzungulila mundawo, komanso anakumbamo copondelamo mphesa na kumanga nsanja. Kenako anausiya m’manja mwa alimi n’kupita ku dziko lina. 34 Nyengo yokolola zipatso itafika, iye anatuma akapolo ake kwa alimi aja kuti akatengeko zipatso zake. 35 Koma alimiwo anagwila akapolo aja. Mmodzi anamumenya, wina anamupha, ndipo wina anamuponya miyala. 36 Anatumanso akapolo ena ambili kuposa gulu loyamba lija. Koma amenewanso anawacita cimodzimodzi. 37 Pamapeto pake anatuma mwana wake kwa iwo, n’kunena kuti, ‘Mwana wangayu akamulemekeza.’ 38 Alimiwo ataona mwanayo anayamba kukambilana kuti, ‘Eya! Uyu ndiye wolandila coloŵa. Bwelani, tiyeni timuphe na kutenga coloŵa cake!’ 39 Conco anamugwila na kumuponya kunja kwa munda wa mpesawo n’kumupha. 40 Ndiye kodi mwinimunda wa mpesa uja akadzabwela, adzacita nawo ciyani alimiwo?” 41 Iwo anayankha kuti: “Cifukwa cakuti ni oipa, adzawawononga koopsa ndipo adzapeleka munda wa mpesawo kwa alimi ena, amene angamupatse zipatso nthawi yokolola ikakwana.”
42 Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Kodi simunaŵelenge m’Malemba kuti, ‘Mwala umene omanga anaukana, wakhala mwala wapakona wofunika kwambili.* Umenewu wacokela kwa Yehova, ndipo ni wodabwitsa m’maso mwathu? 43 Ndiye cifukwa cake nikukuuzani kuti, Ufumu wa Mulungu udzacotsedwa kwa inu na kupelekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake. 44 Komanso munthu wogwela pa mwala umenewu adzaphwanyika. Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwele, udzamupelelatu.”
45 Ansembe aakulu na Afalisi atamva mafanizo akewa, anadziŵa kuti anali kukamba za iwo. 46 Ngakhale kuti iwo anali kufuna kumugwila* anaopa khamu la anthu, cifukwa anthuwo anali kumuona kuti ni mneneli.
22 Yesu anawauzanso mafanizo ena. Anati: 2 “Ufumu wa kumwamba uli ngati mfumu imene inakonza phwando la ukwati wa mwana wake wamwamuna. 3 Ndipo inatuma akapolo ake kuti akaitane anthu oitanidwa ku phwando la ukwatilo, koma iwo anakana. 4 Anatumanso akapolo ena n’kuwauza kuti, ‘Kauzeni oitanidwa aja kuti: “Taonani! Nakonza cakudya ca masana, napha ng’ombe zanga na nyama zanga zonenepa, ndipo zonse zakonzedwa kale. Bwelani ku phwando la ukwati.”’ 5 Koma oitanidwawo sanalabadile ndipo anacoka, wina anapita ku munda kwake, wina ku malonda ake. 6 Koma enawo anagwila akapolo aja, ndipo anawazunza n’kuwapha.
7 “Pamenepo mfumu ija inakwiya koopsa, ndipo inatuma asilikali ake kukapha anthu amene anapha akapolo ake aja n’kutentha mzinda wawo. 8 Kenako anauza akapolo ake kuti, ‘Phwando la ukwati lakonzedwa, koma amene anaitanidwa aja sanali oyenela. 9 Conco, pitani m’misewu yotulukila mu mzinda uno, mukaitane aliyense amene mum’peze kuti abwele ku phwando la ukwatili.’ 10 Conco akapolowo anapita m’misewu na kusonkhanitsa anthu onse amene anapeza, oipa na abwino omwe. Ndipo cipinda cocitilamo phwando la ukwatilo cinadzala na anthu olandila cakudya.
11 “Mfumu ija italoŵa m’cipindamo poyendela oitanidwawo, inaona munthu wina amene sanavale covala ca ukwati. 12 Mfumuyo inamufunsa kuti, ‘Bwanawe, waloŵa bwanji muno popanda covala ca ukwati?’ Iye anasoŵa cokamba. 13 Basi mfumuyo inauza atumiki ake kuti, ‘M’mangeni manja na miyendo na kum’ponya kunja ku mdima. Kumeneko azikalila na kukukuta mano.’
14 “Pakuti oitanidwa ni ambili koma osankhidwa ni oŵelengeka.”
15 Pambuyo pake Afarisi anapita kukapangana zakuti amutape m’kamwa Yesu. 16 Conco iwo anamutumizila ophunzila awo pamodzi na a cipani ca Herode. Iwo anati: “Mphunzitsi, tidziŵa kuti mumakamba zoona na kuphunzitsa njila ya Mulungu m’coonadi, komanso simukondela cifukwa simuyang’ana maonekedwe a anthu. 17 Ndiye tiuzeni, muganiza bwanji? Kodi n’kololeka* kupeleka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” 18 Koma Yesu podziŵa colinga cawo coipa anati: “Onyenga inu, n’cifukwa ciyani mukuniyesa? 19 Nionetseni khobili la msonkhowo.” Iwo anamubweletsela khobili la dinari. 20 Kenako iye anawafunsa kuti: “Kodi cithunzi ici na mawu awa n’zandani?” 21 Iwo anayankha kuti: “Ni za Kaisara.” Ndiyeno iye anawauza kuti: “Conco pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.” 22 Atamva zimenezi anadabwa kwambili ndipo anamusiya n’kucoka.
23 Pa tsiku limenelo, Asaduki amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwela n’kumufunsa kuti: 24 “Mphunzitsi, Mose anati: ‘Mwamuna akamwalila wopanda ana, m’bale wake ayenela kukwatila mkazi wamasiyeyo, n’kubelekela m’bale wake uja ana.’ 25 Lomba panali amuna 7 apacibale. Woyamba anakwatila kenako anamwalila. Koma popeza analibe ana, mkazi uja anakwatiwa na m’bale wa mwamuna wake. 26 Zinacitika cimodzimodzi kwa waciŵili na wacitatu mpaka kwa onse 7. 27 Pothela pake mkazi uja nayenso anamwalila. 28 Ndiye pamene akufa adzauka, kodi mkaziyo adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatilapo?”
29 Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa, cifukwa simudziŵa Malemba kapena mphamvu za Mulungu; 30 Pakuti pa kuuka kwa akufa amuna sadzakwatila, ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba. 31 Ponena za kuuka kwa akufa, kodi simunaŵelenge zimene Mulungu anakuuzani pamene anati: 32 ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki komanso Mulungu wa Yakobo? Iye si Mulungu wa akufa, koma wa anthu amoyo.” 33 Khamulo litamva zimenezi, linadabwa kwambili na kaphunzitsidwe kake.
34 Afarisi atamva kuti Yesu anawasoŵetsa conena Asaduki, anasonkhana pamodzi n’kubwela kwa iye. 35 Ndipo mmodzi wa iwo, wodziŵa Cilamulo, anamuyesa mwa kumufunsa kuti: 36 “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambili m’Cilamulo ni liti?” 37 Iye anamuyankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako na mtima wako wonse, moyo wako wonse, na maganizo ako onse.’ 38 Ili ndilo lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba. 39 Laciŵili lofanana nalo ni ili: ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’ 40 Cilamulo conse komanso zolemba za aneneli zagona pa malamulo aŵili amenewa.”
41 Ndiyeno Afarisi aja atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti: 42 “Muganiza bwanji za Khristu? Kodi ni mwana wa ndani?” Iwo anamuyankha kuti: “Wa Davide.” 43 Iye anawafunsanso kuti: “Nanga n’cifukwa ciyani Davide mouzilidwa anamuchula kuti Ambuye, pamene anati 44 ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala ku dzanja langa lamanja, kufikila nitaika adani ako kunsi kwa mapazi ako”’? 45 Ngati Davide anamuchula kuti Ambuye, ndiye akhala bwanji mwana wake?” 46 Koma palibe anatha kumuyankha, ndipo kucokela tsiku limenelo palibe analimba mtima kumufunsanso mafunso.
23 Tsopano Yesu analankhula na khamu la anthulo komanso ophunzila ake kuti: 2 “Alembi na Afarisi adzikhazika okha pa mpando wa Mose. 3 Conco, muzicita na kutsatila zonse zimene amakuuzani, koma musamatengele zimene iwo amacita, cifukwa amangonena koma sacita zimene amanenazo. 4 Iwo amamanga katundu wolema n’kumuika pa mapewa a anthu, koma iwowo safuna kumukankhako ngakhale na cala cawo. 5 Zonse zimene iwo amacita, amazicita kuti anthu awaone. Pakuti amakulitsa tumapukusi twa malemba tumene amavala monga zithumwa, ndiponso amatalikitsa ulusi wopota wa m’mbali mwa zovala zawo. 6 Iwo amakonda malo olemekezeka kwambili pa cakudya ca madzulo, komanso amakonda kukhala pa mipando ya kutsogolo* m’masunagoge. 7 Amakondanso kupatsidwa moni m’misika, komanso kuti anthu aziwachula kuti Mphunzitsi.* 8 Koma inu musamachedwe aphunzitsi, cifukwa Mphunzitsi wanu ni mmodzi, ndipo nonsenu ndinu abale. 9 Komanso musamachule aliyense kuti atate wanu pa dziko pano, cifukwa Atate wanu ni mmodzi, wa kumwamba Yekhayo. 10 Musamachedwenso atsogoleli, cifukwa Mtsogoleli wanu ni mmodzi, Khristu. 11 Koma wamkulu pakati panu akhale mtumiki wanu. 12 Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, ndipo aliyense wodzicepetsa adzakwezedwa.
13 “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa mumatsekela anthu khomo loloŵela mu Ufumu wa kumwamba. Pakuti inuyo simuloŵamo, ndiponso amene afuna kuloŵamo mumawaletsa. 14 ——
15 “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa mumayenda mitunda itali-itali pa nyanja komanso pa mtunda kuti mukatembenule munthu mmodzi. Ndipo munthuyo akatembenuka mumamupangitsa kukhala woyenelela kuponyedwa mu Gehena* kuwilikiza kaŵili kuposa inu.
16 “Tsoka inu atsogoleli akhungu amene mumati, ‘Ngati munthu walumbila kuti, “Pali kacisi,” zilibe kanthu. Koma ngati walumbila kuti, “Pali golide wa m’kacisi,” ayenela kukwanilitsa lumbilo lake.’ 17 Opusa komanso akhungu inu! Kodi cofunika kwambili n’ciyani, golide kapena kacisi amene wayeletsa golideyo? 18 Ndiponso mumati, ‘Ngati munthu walumbila kuti, “Pali guwa la nsembe,” zilibe kanthu. Koma ngati walumbila kuti, “Pali nsembe yomwe ili paguwapo,” ayenela kukwanilitsa lumbilo lake.’ 19 Akhungu inu! Kodi cofunika kwambili n’ciyani, nsembe kapena guwa la nsembe lomwe layeletsa nsembeyo? 20 Conco, aliyense wolumbila kuti, “Pali guwa la nsembe,” akulumbila pali guwalo komanso zonse zimene zili pomwepo. 21 Ndipo aliyense wolumbila kuti, “Pali kacisi,” akulumbila pali kacisiyo komanso pali Iye wokhala mmenemo. 22 Komanso aliyense wolumbila kuti, “Pali kumwamba,” akulumbila pali mpando wacifumu wa Mulungu ndiponso pali Iye wokhala pa mpandowo.
23 “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa mumapeleka cakhumi ca minti, dilili, na kumini,* koma mumanyalanyaza zinthu zofunika kwambili za m’Cilamulo, monga cilungamo, cifundo, na kukhulupilika. Kupeleka zinthu zimenezi n’kofunika, koma simuyenela kunyalanyaza zinthu zinazo. 24 Atsogoleli akhungu inu, amene mumasefa zakumwa zanu kuti mucotsemo kanyelele, koma mumameza ngamila!
25 “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa muli ngati kapu na mbale imene yayeletsedwa kunja, koma mkati mwake muli zonyansa. Mumtima mwanu ni modzala dyela* komanso kusadziletsa. 26 Mfarisi wakhungu iwe, coyamba yeletsa mkati mwa kapu na mbale kuti kunja kwakenso kukhale koyela.
27 “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa muli ngati manda opaka laimu, amene amaoneka okongola kunja koma mkati mwake ni modzala na mafupa a anthu akufa komanso zonyansa za mtundu uliwonse. 28 Ni mmenenso inu mulili. Pamaso pa anthu mumaoneka olungama, koma mumtima mwanu nimodzala cinyengo na kusamvela malamulo.
29 “Tsoka inu alembi na Afarisi, onyenga inu! Cifukwa mumamanga manda a aneneli na kukongoletsa manda* a anthu olungama. 30 Ndipo mumanena kuti, ‘Tikanakhalako m’masiku a makolo athu, sitikanatengako mbali pokhetsa magazi a aneneli.’ 31 Cotelo, mukudzicitila umboni wakuti ndinu ana a anthu amene anapha aneneliwo. 32 Conco, tsilizitsani nchito imene makolo anu anaiyamba.
33 “Njoka inu! ana a mphili, mudzathaŵa bwanji cilango ca Gehena?* 34 Pa cifukwa cimeneci, nikukutumizilani aneneli, anthu anzelu komanso aphunzitsi. Ena mudzawapha na kuwapacika pa mtengo. Ndipo ena mudzawakwapula m’masunagoge anu na kuwazunza mu mzinda na mzinda, 35 kuti magazi onse a anthu olungama amene anakhetsedwa pa dziko lapansi akhale pa inu. Kuyambila magazi a munthu wolungama Abele mpaka magazi a Zekariya mwana wa Barakiya, amene munamuphela pakati pa nyumba yopatulika na guwa la nsembe. 36 Ndithu nikukuuzani kuti zinthu zonsezi zidzaugwela m’badwo uwu.
37 “Yerusalemu, Yerusalemu, iwe wakupha aneneli komanso woponya miyala anthu otumidwa kwa iwe. Mobweleza-bweleza n’nafuna kusonkhanitsa pamodzi ana ako, monga mmene nkhuku imasonkhanitsila anapiye ake m’mapiko ake! Koma inu simunafune zimenezo. 38 Lomba mvelani! Mulungu wakusiyilani nyumba yanu.* 39 Pakuti nikukuuzani kuti kuyambila tsopano simudzanionanso, mpaka pamene mudzati, ‘Wodalitsika ni iye wobwela m’dzina la Yehova!’”
24 Tsopano pamene Yesu anali kucoka pa kacisi, ophunzila ake anafika kwa iye kuti amuonetse zimango za pa kacisipo. 2 Iye anawauza kuti: “Kodi mukuziona zinthu zonsezi? Ndithu nikukuuzani kuti, pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”
3 Iye atakhala pansi mu Phili la Maolivi, ophunzila ake anamufikila mwamseli n’kumufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzacitika liti, nanga cizindikilo ca kukhalapo* kwanu komanso ca cimalizilo ca nthawi ino* cidzakhala ciyani?”
4 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Samalani kuti munthu asakusoceletseni, 5 cifukwa ambili adzabwela m’dzina langa n’kumanena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasoceletsa anthu ambili. 6 Mudzamva phokoso la nkhondo komanso mbili za nkhondo. Zimenezi zisadzakucititseni mantha. Pakuti ziyenela kucitika koma mapeto adzakhala asanafikebe.
7 “Mtundu udzaukilana na mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana na ufumu wina, komanso kudzakhala njala na zivomezi m’malo osiyana-siyana. 8 Zinthu zonsezi ni ciyambi ca masautso.*
9 “Ndiyeno anthu adzakupelekani kuti mukazunzidwe ndipo adzakuphani. Ndiponso mitundu yonse idzakudani cifukwa ca dzina langa. 10 Cina, anthu ambili adzapunthwa ndipo adzapelekana na kudana. 11 Kudzabwela aneneli ambili onyenga ndipo adzasoceletsa anthu ambili. 12 Ndiponso cifukwa ca kuwonjezeka kwa kusamvela malamulo, cikondi ca anthu ambili cidzacepa. 13 Koma amene adzapilile* mpaka pa mapeto adzapulumuka. 14 Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti udzakhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.
15 “Cotelo, mukadzaona cinthu conyansa cobweletsa ciwonongeko, cimene mneneli Danieli ananena, citaimilila pa malo oyela (woŵelenga adzazindikile). 16 Amene ali mu Yudeya adzayambe kuthaŵila ku mapili. 17 Munthu amene adzakhale pa mtenje asadzatsike kuti akatenge katundu m’nyumba mwake. 18 Ndipo munthu amene adzakhale ku munda asadzabwelele kuti akatenge covala cake cakunja. 19 Tsoka kwa akazi apathupi komanso oyamwitsa m’masiku amenewo! 20 Pitilizani kupemphela kuti musadzathaŵe m’nyengo yozizila kapena pa tsiku la Sabata. 21 Cifukwa panthawiyo kudzakhala cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca dziko mpaka pano, ndipo sicidzacitikanso. 22 Kukamba zoona masikuwa akanapanda kucepetsedwa, palibe amene akanapulumuka. Koma cifukwa ca osankhidwawo masikuwo adzacepetsedwa.
23 “Cotelo munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’ kapena, ‘Ali uko!’ musakakhulupilile. 24 Pakuti kudzabwela anthu onamizila kukhala Khristu komanso aneneli onyenga. Ndipo adzacita zizindikilo zamphamvu na zodabwitsa kuti asoceletse anthu, ndipo ngati n’kotheka ngakhale osankhidwawo. 25 Onani! Ine nakucenjezelanitu. 26 Conco, anthu akadzakuuzani kuti, ‘Inu! Iye ali ku cipululu,’ musakapiteko. Akadzanena kuti ‘Ali m’zipinda zamkati,’ musadzakhulupilile. 27 Pakuti monga mmene mphenzi imang’animila kucokela kum’maŵa mpaka kumadzulo, ni mmenenso zidzakhalile na kukhalapo* kwa Mwana wa munthu. 28 Kulikonse kumene kuli thupi lakufa, ziwombankhanga zimasonkhana kumeneko.
29 “Cisautso ca m’masiku amenewo cikadzangotha, dzuŵa lidzacita mdima ndipo mwezi sudzawala. Nyenyezi zidzagwa kucokela kumwamba, ndipo mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. 30 Kenako cizindikilo ca Mwana wa munthu cidzaonekela kumwamba. Ndipo mafuko onse a padziko lapansi adzadziguguda pacifuwa cifukwa ca cisoni. Iwo adzaona Mwana wa munthu akubwela pa mitambo ya kumwamba ali na mphamvu komanso ulemelelo waukulu. 31 Iye adzatumiza angelo ake na kulila kwamphamvu kwa lipenga, ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kucokela ku mphepo zinayi. Kucokela kumalekezelo a mlengalenga mpaka kumalekezelo ake ena.
32 “Tsopano phunzilam’poni kanthu pa fanizo ili la mtengo wa mkuyu. Mukangoona kuti nthambi yake yanthete yayamba kuphuka na kutulutsa masamba, mumadziŵa kuti dzinja layandikila. 33 Mofananamo, inunso mukadzaona zinthu zonsezi mudzadziŵe kuti iye ali pafupi, pa khomo penipeni. 34 Ndithu nikukuuzani kuti m’badwo uwu sudzatha wonse, mpaka utaona zinthu zonsezi zitacitika. 35 Kumwamba na dziko lapansi zidzacoka, koma mawu anga sadzacoka ayi.
36 “Ponena za tsikulo na ola lake palibe amene adziŵa. Ngakhale angelo a kumwamba kapena Mwanayo, koma Atate yekha basi. 37 Pakuti monga zinalili m’masiku a Nowa, ni mmenenso zidzakhalile pa nthawi ya kukhalapo* kwa Mwana wa munthu. 38 M’masiku amenewo Cigumula cisanacitike anthu anali kudya na kumwa, amuna anali kukwatila ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikila tsiku limene Nowa analoŵa m’Cingalawa. 39 Anthuwa ananyalanyaza zimene zinali kucitika mpaka Cigumula cinafika n’kuwakokolola onsewo. Umu ni mmenenso zidzakhalile pa nthawi ya kukhalapo kwa Mwana wa munthu. 40 Pa nthawiyo amuna aŵili adzakhala m’munda, ndipo mmodzi adzatengedwa koma winayo adzasiyidwa. 41 Akazi aŵili adzakhala akupela pa mphelo. Mmodzi adzatengedwa koma winayo adzasiyidwa. 42 Conco khalani maso cifukwa simukudziŵa tsiku limene Mbuye wanu adzabwela.
43 “Koma dziŵani ici: Ngati mwininyumba angadziŵe nthawi imene mbala ikubwela usiku,* angakhalebe maso ndipo sangalole kuti mbalayo ithyole n’kuloŵa m’nyumba mwake. 44 Mwa ici, inunso khalani wokonzeka cifukwa Mwana wa munthu adzabwela pa ola limene inu simukuliganizila.
45 “Ndani maka-maka amene ali kapolo wokhulupilika ndiponso wanzelu, amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anila anchito ake a pakhomo, na kuwapatsa cakudya cawo pa nthawi yoyenela? 46 Kapoloyo adzakhala wodala ngati mbuye wake pobwela adzamupeza akucita zimenezo! 47 Ndithu nikukuuzani kuti adzamuika kuti aziyang’anila zinthu zake zonse.
48 “Koma ngati kapolo woipayo mumtima mwake anganene kuti, ‘Mbuye wanga akucedwa,’ 49 n’kuyamba kumenya akapolo anzake, ndiponso kudya na kumwa pamodzi na zidakwa zenizeni, 50 mbuye wa kapoloyo adzabwela pa tsiku limene iye sakuliyembekezela, komanso pa ola limene sakulidziŵa. 51 Pamenepo adzamupatsa cilango coŵaŵa kwambili, ndipo adzamuponya ku malo a anthu onyenga. Kumeneko azikalila na kukuta mano.
25 “Ufumu wa kumwamba uli ngati anamwali 10 amene anatenga nyale zawo n’kupita kukakumana na mkwati. 2 Anamwali asanu anali opusa, ndipo asanu enawo anali ocenjela.* 3 Opusawo anatenga nyale zawo, koma sanatenge mafuta owonjezela, 4 Koma ocenjelawo anatenga mafuta owonjezela m’mabotolo awo pamodzi na nyale zawo. 5 Popeza kuti mkwatiyo anacedwa, onse anayamba kukusila mpaka anagona. 6 Pakati pa usiku, kunamveka mawu ofuula akuti: ‘Mkwati uja wafika! Pitani mukamucingamile.’ 7 Nthawi yomweyo anamwali onsewo anauka n’kuyamba kukonza nyale zawo. 8 Anamwali opusa aja anapempha ocenjelawo kuti, ‘Tipatsen’koni mafuta anu, cifukwa nyale zathu zatsala pang’ono kuzima.’ 9 Koma ocenjelawo anayankha kuti: ‘Ayi, tikagaŵana mwina satikwanila tonse. Conco pitani kwa ogulitsa mukagule anu.’ 10 Pamene anali kupita kukagula mafutawo mkwati anafika. Ndipo anamwali amene anali okonzekawo analoŵa naye m’nyumba imene munali phwando la ukwati, ndipo citseko cinatsekedwa. 11 Pambuyo pake, anamwali ena aja nawonso anafika n’kunena kuti, ‘Ambuye, Ambuye, titsegulileni!’ 12 Poyankha iye anati, ‘Kukamba zoona, sinikudziŵani.’
13 “Conco, khalanibe maso, cifukwa simudziŵa tsiku kapena ola lake.
14 “Pakuti zili ngati munthu amene anatsala pang’ono kupita ku dziko lina. Iye anaitana akapolo ake n’kuwasungiza cuma cake. 15 Kapolo woyamba anamupatsa matalente asanu,* waciŵili matalente aŵili, wacitatu talente imodzi. Aliyense anamupatsa malinga na luso lake. Kenako munthuyo anapita ku dziko lina. 16 Nthawi yomweyo amene analandila matalente asanu uja anapita kukacita nawo malonda, ndipo anapindula matalente enanso asanu. 17 Nayenso uja amene analandila matalente aŵili, anapindula enanso aŵili. 18 Koma amene analandila talente imodzi uja anapita kukakumba pansi, n’kubisa ndalama* ya mbuye wakeyo.
19 “Patapita nthawi yaitali mbuye wa akapolowo anabwela kuti aone zimene anacita na ndalamazo. 20 Conco, amene analandila matalente asanu uja, anabwela na matalente enanso asanu, n’kunena kuti, ‘Ambuye, munanisungiza matalente asanu. Koma onani napindula enanso asanu.’ 21 Mbuye wakeyo anamuuza kuti: ‘Wacita bwino, ndiwe kapolo wabwino komanso wokhulupilika! Wakhulupilika pa zinthu zocepa. Nidzakuika kuti uziyang’anila zinthu zambili. Sangalala pamodzi nane mbuye wako.’ 22 Kenako amene analandila matalente aŵili uja anabwela n’kunena kuti, ‘Ambuye, munanisungiza matalente aŵili, koma onani, napindula enanso aŵili.’ 23 Mbuye wakeyo anamuuza kuti: ‘Wacita bwino, ndiwe kapolo wabwino komanso wokhulupilika! Wakhulupilika pa zinthu zocepa. Nidzakuika kuti uziyang’anila zinthu zambili. Sangalala pamodzi nane mbuye wako.’
24 “Pamapeto pake, kapolo amene analandila talente imodzi uja anabwela n’kunena kuti: ‘Ambuye, n’nali kudziŵa kuti ndinu munthu wovuta. Mumakolola kumene simunafese, na kututa tiligu kumene simunapepete. 25 Conco n’nacita mantha, ndipo n’napita kukabisa pansi talente ija. Aneni, tengani ndalama yanu.’ 26 Poyankha mbuye wakeyo anamuuza kuti: ‘Kapolo woipa komanso waulesi iwe, wati unali kudziŵa kuti nimakolola kumene sin’nafese, komanso nimatuta tiligu kumene sin’napepete? 27 Ndiye ukanacita bwino kusungiza ndalama yangayi kwa osunga ndalama.* Ndipo ine n’tafika, nikanailandila pamodzi na ciwongoladzanja cake.
28 “‘Cotelo mulandeni talenteyo, ndipo mupatse amene ali na matalente 10. 29 Pakuti aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zambili, ndipo adzakhala na zoculuka. Koma amene alibe adzalandidwa ngakhale zimene ali nazo. 30 M’ponyeni kunja ku mdima kapolo wacabe-cabe ameneyu. Kumeneko azikalila na kukukuta mano.’
31 “Mwana wa munthu akadzabwela mu ulemelelo wake, pamodzi na angelo onse, adzakhala pa mpando wake wacifumu waulemelelo. 32 Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa pamaso pake. Ndipo iye adzalekanitsa anthu mmene m’busa amalekanitsila nkhosa na mbuzi. 33 Ndipo adzaika nkhosa ku dzanja lake lamanja, koma mbuzi adzaziika kumanzele kwake.
34 “Ndiyeno Mfumu idzauza okhala ku dzanja lake lamanja kuti: ‘Bwelani inu amene mwadalitsidwa na Atate wanga. Loŵani mu Ufumu umene unakonzedwela inu kucokela pa kukhazikitsidwa kwa dziko. 35 Pakuti nitamva njala munanipatsa cakudya. Nitamva ludzu munanipatsa madzi. Ndipo pamene n’nali mlendo munanilandila bwino. 36 N’nali wamalisece* koma inu munaniveka. N’tadwala munanisamalila. N’nali m’ndende ndipo inu munabwela kudzaniona.’ 37 Ndiyeno olungamawo adzamuyankha kuti: ‘Ambuye, kodi ni liti pomwe tinakuonani muli na njala ife n’kukupatsani cakudya, kapena muli na ludzu ife n’kukupatsani madzi? 38 Ni liti pomwe tinakuonani muli mlendo, ife n’kukulandilani bwino, kapena muli wamalisece ife n’kukuvekani? 39 Ni liti pomwe munali kudwala kapena pomwe munali m’ndende, ife n’kubwela kudzakuonani?’ 40 Poyankha Mfumuyo idzawauza kuti, ‘Ndithu nikukuuzani kuti, ciliconse cimene munacitila mmodzi wa abale anga aang’ono awa, munacitila ine amene.’
41 “Ndiyeno adzauza aja okhala ku dzanja lake lamanzele kuti: ‘Cokani pamaso panga inu otembeleledwa. Pitani ku moto wosatha umene anausonkhela Mdyelekezi na ziŵanda zake. 42 Pakuti n’tamva njala simunanipatse cakudya, ndipo n’tamva ludzu simunanipatse madzi. 43 N’nali mlendo koma simunanilandile bwino. N’nali wamalisece koma simunaniveke. N’nali kudwala komanso n’nali m’ndende koma simunanisamalile.’ 44 Pamenepo iwonso adzayankha kuti: ‘Ambuye, ni liti pomwe tinakuonani muli anjala kapena aludzu, kapena muli mlendo kapena muli wamalisece, kapena mukudwala kapenanso muli m’ndende, koma ife osakutumikilani?’ 45 Poyankha Mfumuyo idzawauza kuti: ‘Ndithu nikukuuzani kuti, ciliconse cimene simunacitile mmodzi wa aang’ono awa, simunacitile ine amene.’ 46 Amenewa adzawonongedwa kothelatu,* koma olungama adzalandila moyo wosatha.”
26 Yesu atatsiliza kulankhula zinthu zonsezi, anauza ophunzila ake kuti: 2 “Inu mudziŵa kuti kwangotsala masiku aŵili kuti Pasika acitike, ndipo Mwana wa munthu adzam’peleka kuti amuphe pa mtengo.”
3 Pa nthawiyi, ansembe aakulu komanso akulu anasonkhana m’bwalo la mkati panyumba ya mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa. 4 Ndipo anapangana zakuti amugwile* Yesu mocenjela na kumupha. 5 Koma iwo anali kunena kuti: “Tisakamugwile pa cikondwelelo, kuopela kuti anthu angadzacite cipolowe.”*
6 Pamene Yesu anali ku Betaniya m’nyumba ya Simoni wakhate, 7 mayi wina anafika pafupi na Yesu atanyamula botolo la mwala wa alabasitala mmene munali mafuta odula onunkhila. Iye anayamba kuthila mafutawo pa mutu pa Yesu pamene anali kudya. 8 Ophunzila ake ataona zimenezi, anakwiya ndipo anati: “N’cifukwa ciyani akuwononga mafutawa? 9 Mafutawa akanagulitsidwa ndalama zambili, ndipo ndalamazo zikanapelekedwa kwa osauka.” 10 Yesu anadziŵa zimenezi ndipo anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani mukumuvutitsa mayiyu? Zimene iyeyu wanicitila n’zabwino. 11 Pakuti osaukawo muli nawo nthawi zonse, koma ine simudzakhala nane nthawi zonse. 12 Mayiyu wathila mafuta onunkhilawa pathupi langa pokonzekela kuikidwa m’manda kwanga. 13 Ndithu nikukuuzani kuti, kulikonse kumene uthenga wabwinowu udzalalikidwa pa dziko lonse, anthu azikafotokozanso zimene mayiyu wacita pomukumbukila.”
14 Pambuyo pake mmodzi wa atumwi 12 aja wochedwa Yudasi Isikariyoti, anapita kwa ansembe aakulu 15 n’kuwafunsa kuti: “Mudzanipatsa ciyani nikamupeleka kwa inu?” Iwo anamulonjeza ndalama 30 za siliva. 16 Conco kucokela nthawi imeneyo, iye anayamba kufuna-funa mpata wabwino woti amupeleke.
17 Pa tsiku loyamba la cikondwelelo ca Mikate Yopanda Zofufumitsa, ophunzila a Yesu anafika kwa iye n’kumufunsa kuti: “Mufuna tikakukonzeleni kuti malo odyelako Pasika?” 18 Iye anati: “Pitani mu mzinda kwa Uje mukamuuze kuti, ‘Mphunzitsi akuti, “Nthawi yanga yoikika ili pafupi. Nidzacitila kunyumba kwako cikondwelelo ca Pasika pamodzi na ophunzila anga.”’” 19 Conco ophunzilawo anacita zimene Yesu anawalangiza, ndipo anakonza zonse zofunikila pa Pasika.
20 Nthawi ya madzulo, Yesu na ophunzila ake 12 aja anali kudya pa thebulo. 21 Pamene anali kudya Yesu anati: “Ndithu nikukuuzani kuti mmodzi wa inu anipeleka.” 22 Pomva cisoni kwambili na zimenezi, aliyense wa iwo anayamba kumufunsa kuti: “Ambuye, ndine kapena?” 23 Iye anayankha kuti: “Amene akusunsa nane pamodzi m’mbalemu ndiye anipeleke. 24 Zoonadi, Mwana wa munthu akupita, monga mmene Malemba amakambila za iye. Koma tsoka kwa munthu amene apeleke Mwana wa munthu! Cikanakhala bwino munthu ameneyo akanapanda kubadwa.” 25 Yudasi amene anatsala pang’ono kumupeleka anayankha kuti: “Mphunzitsi,* ningakhale ine kapena?” Yesu anamuyankha kuti: “Wakamba wekha.”
26 Akupitiliza kudya, Yesu anatenga mtanda wa mkate, ndipo atayamika anaunyema-nyema n’kuupeleka kwa ophunzila ake. Iye anati: “Aneni idyani. Mkate uwu ukuimila thupi langa.” 27 Ndiyeno anatenga kapu n’kuyamika, ndipo anapatsa ophunzila ake n’kuwauza kuti: “Imwani za m’kapuyi nonsenu. 28 Pakuti vinyoyu akuimila ‘magazi anga a cipangano,’ amene adzakhetsedwa kuti anthu ambili akhululukidwe macimo. 29 Koma nikukuuzani kuti: Sinidzamwanso cakumwa ciliconse cocokela ku mphesa kufikila tsiku limene nidzamwa cakumwa catsopano pamodzi na inu mu Ufumu wa Atate wanga.” 30 Pa mapeto pake, iwo atatsiliza kuimba nyimbo za citamando,* anapita ku Phili la Maolivi.
31 Kenako Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthaŵa n’kunisiya nekha usiku uno, cifukwa Malemba amanena kuti: ‘Nidzapha m’busa ndipo nkhosa zake zidzamwazikana.’ 32 Koma nikadzaukitsidwa, nidzatsogola kupita ku Galileya inu musanafike kumeneko.” 33 Koma Petulo anamuyankha kuti: “Ngakhale ena onsewa atathaŵa n’kukusiyani, ine sinidzathaŵa!” 34 Yesu anamuuza kuti: “Ndithu nikukuuza kuti usiku wa lelo, iwe unikana katatu tambala asanalile.” 35 Petulo anayankha kuti: “Ngati n’kufa tifela pamodzi, ndipo siningakukaneni ngakhale pang’ono.” Ophunzila ena onsewo anakambanso cimodzi-modzi.
36 Kenako Yesu na ophunzila ake anafika pa malo ochedwa Getsemane, ndipo anawauza kuti: “Khalani pansi pompano, ine nipita uko kukapemphela.” 37 Popita kumeneko anatenga Petulo pamodzi na ana aŵili a Zebedayo. Ndipo anayamba kumva cisoni na kuvutika kwambili mumtima. 38 Kenako anawauza kuti: “Nili na cisoni cofa naco. Khalani pano ndipo mukhalebe maso pamodzi nane.” 39 Atapitako patsogolo pang’ono, anagwada mpaka nkhope yake pansi n’kuyamba kupemphela kuti: “Atate ngati n’kotheka, kapu iyi inipitilile. Osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”
40 Atabwelela kwa ophunzilawo anawapeza akugona, ndipo anafunsa Petulo kuti: “Kodi simungakhale maso pamodzi nane ngakhale kwa ola limodzi? 41 Khalanibe maso ndipo pitilizani kupemphela kuti musaloŵe m’mayeselo. Zoona mzimu ni wofunitsitsa,* koma thupi ni lofooka.” 42 Iye anapitanso kaciŵili kukapemphela ndipo anati: “Atate, ngati n’zosatheka kuti kapu iyi inipitilile mpaka n’tamwa ndithu, cifunilo canu cicitike.” 43 Atabwelelanso anawapeza akugona, cifukwa zikope zawo zinali zitalemela. 44 Conco anawasiya n’kupitanso kukapemphela kacitatu, akubweleza zinthu zimodzi-modzi. 45 Pambuyo pake anabwelelanso kwa ophunzilawo na kuwauza kuti: “Zoona pa nthawi ngati ino mukugona na kupumula! Onani! Ola lakuti Mwana wa munthu apelekedwe m’manja mwa ocimwa layandikila. 46 Nyamukani tiyeni tizipita. Onani! Wonipeleka uja ali pafupi.” 47 Ali mkati molankhula, Yudasi mmodzi wa Atumwi 12 aja anatulukila na khamu lalikulu la anthu, lotumidwa na ansembe aakulu komanso akulu. Anthuwo anali atanyamula malupanga na nkholi.
48 Pa nthawiyo, womupelekayo anali atawapatsa cizindikilo cakuti: “Amene nikam’psompsone ni ameneyo; mukamugwile.” 49 Atafika, Yudasi analunjika kwa Yesu n’kunena kuti: “Moni, Mphunzitsi!” Kenako anam’psompsona mwacikondi. 50 Koma Yesu anamufunsa kuti: “Bwanawe, wabwela kudzacita ciyani kuno?” Pamenepo anthuwo anafika pafupi n’kugwila Yesu na kumumanga. 51 Koma wina mwa amene anali na Yesu anasolola lupanga lake n’kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kumudula khutu. 52 Nthawi yomweyo Yesu anamuuza kuti: “Bwezela lupanga lako m’cimake, cifukwa onse onyamula lupanga adzafa na lupanga. 53 Kapena uganiza kuti siningapemphe Atate kuti anitumizile magulu oposa 12 a angelo nthawi yomwe ino? 54 Koma nikacita zimenezi, kodi Malemba amene anakambilatu kuti zotelezi ziyenela kucitika adzakwanilitsika bwanji?” 55 Pa nthawiyo Yesu anauza khamu la anthulo kuti: “N’cifukwa ciyani mwabwela kudzanigwila mutanyamula malupanga na nkholi, ngati kuti mukubwela kudzagwila wacifwamba? Tsiku lililonse n’nali kukhala m’kacisi kuphunzitsa koma simunanigwile. 56 Koma zonsezi zacitika kuti zolemba za aneneli zikwanilitsidwe.”* Kenako ophunzila ake onse anang’ondoka kuthaŵa n’kumusiya yekha.
57 Anthu amene anagwila Yesu aja anapita naye kwa Kayafa mkulu wa ansembe, kumene alembi na akulu anali atasonkhana. 58 Koma Petulo anamutsatilabe capatali ndithu, mpaka kukafika m’bwalo la kunyumba ya mkulu wa ansembe. Ataloŵa mkati anakhala pansi pamodzi na anchito a m’nyumbamo kuti aone zimene zicitike.
59 Pa nthawiyo, ansembe aakulu komanso onse mu Khoti Yaikulu ya Ayuda, anali kufuna-funa umboni wonama kuti amunamizile mlandu Yesu n’colinga cakuti amuphe. 60 Koma sanapeze umboni uliwonse ngakhale kuti kunabwela mboni zambili zonama. Pambuyo pake kunabwela mboni zina ziŵili. 61 Mbonizo zinati: “Munthu uyu anali kukamba kuti, ‘Ningathe kugwetsa kacisi wa Mulungu n’kumumanganso m’masiku atatu.’” 62 Mkulu wa ansembe atamva zimenezi anaimilila n’kumufunsa kuti: “Kodi suyankha ciliconse? Ukutipo ciyani pa zimene anthu awa akukuneneza?” 63 Koma Yesu anangokhala cete. Conco mkulu wa ansembeyo anamuuza kuti: “Nikukulumbilitsa pali Mulungu wamoyo, kuti utiuze ngati ndiwedi Khristu, Mwana wa Mulungu!” 64 Yesu anamuyankha kuti: “Inuyo mwanena nokha. Koma nikukuuzani kuti: Kuyambila tsopano, mudzaona Mwana wa munthu atakhala kudzanja lamanja lamphamvu, komanso akubwela pa mitambo ya kumwamba.” 65 Nthawi yomweyo mkulu wa ansembeyo anang’amba zovala zake zakunja, n’kunena kuti: “Wanyoza Mulungu! Kodi apa n’kufunanso umboni wina? Mwaona! Apa mwadzimvela nokha kuti akunyoza Mulungu. 66 Kodi inu mukutipo ciyani?” Iwo anayankha kuti: “Ameneyu ayenela kuphedwa ndithu.” 67 Kenako anamuthila mata kumaso na kum’menya makofi. Ena anamuwaza mbama kumaso, 68 n’kumanena kuti: “Iwe Khristu, lotela. Wakumenya ndani?”
69 Tsopano Petulo anakhala pansi panja m’bwalo lija, ndipo mtsikana wanchito anabwela kwa iye n’kunena kuti: “Inunso munali na Yesu wa ku Galileyayu!” 70 Koma iye anakana pamaso pa onse ndipo anati: “Sinizidziŵa zimene ukukamba.” 71 Atatuluka n’kupita ku kanyumba ka pageti, mtsikana winanso anamuzindikila n’kuuza amene anali pamenepo kuti: “Munthu uyu anali na Yesu Mnazareti.” 72 Apanso Petulo anakana mocita kulumbila, amvekele: “Ndithu munthu ameneyu sinimudziŵa!” 73 Patapita kanthawi pang’ono, amene anaimilila capafupi anabwela n’kuuza Petulo kuti: “Mosakayikila iwenso ndiwe mmodzi wa iwo, cifukwa kalankhulidwe kako kakuulula.” 74 Apa lomba iye anayamba kukana* na kulumbila kuti: “Nati munthu uyu ine sinimudziŵa iyayi!” Nthawi yomweyo tambala analila. 75 Ndipo Petulo anakumbukila mawu a Yesu aja akuti: “Iwe unikana katatu tambala asanalile.” Pamenepo anatuluka panja n’kuyamba kulila mwacisoni kwambili.
27 Kutaca m’maŵa, ansembe aakulu onse na akulu anakambilana na kugwilizana zakuti amuphe Yesu. 2 Atam’manga, anapita kukam’peleka kwa bwanamkubwa Pilato.
3 Ndiyeno Yudasi womupeleka uja ataona kuti Yesu waweluzidwa kuti aphedwe, anadzimvela cisoni kwambili, ndipo anapita kukabweza ndalama 30 zasiliva zija kwa ansembe aakulu komanso akulu. 4 Iye anati: “N’nacimwa cifukwa copeleka munthu wosalakwa.” Iwo anamuyankha kuti: “Izo n’zako!* Ife sizitikhudza!” 5 Conco iye anangoponya ndalama zasiliva zija m’kacisi n’kucoka. Kenako anapita kukadzimangilila. 6 Koma ansembe aakuluwo anatenga ndalama zasiliva zija n’kunena kuti: “Si kololeka kuika ndalamazi mosungila cuma copatulika, cifukwa ni malipilo a magazi.” 7 Pambuyo pokambilana, iwo anatenga ndalamazo na kukagulila munda wa woumba mbiya kuti ukhale manda a alendo. 8 Conco, munda umenewo wakhala ukuchedwa Munda wa Magazi mpaka lelo. 9 Izi zinakwanilitsa mawu amene ananenedwa kupitila mwa mneneli Yeremiya akuti: “Ndipo iwo anatenga ndalama 30 zasiliva, mtengo umene iwo anaika pa munthuyo, malipilo amene ena mwa ana a Isiraeli anagwilizana kugulila munthuyo. 10 Ndipo ndalamazo anagulila munda wa woumba mbiya, malinga na zimene Yehova ananilamula.”
11 Tsopano Yesu anaimilila pamaso pa bwanamkubwa, ndipo bwanamkubwayo anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti: “Mwanena nokha zimenezi.” 12 Koma pamene ansembe aakulu na akulu anali kumuneneza, iye sanayankhe ciliconse. 13 Ndiyeno Pilato anamufunsa kuti: “Kodi sukumva zonsezi zimene akukuneneza?” 14 Koma Yesu sanamuyankhe ciliconse. Anangokhala duu, moti bwanamkubwayo anadabwa kwambili.
15 Pa cikondwelelo ciliconse, bwanamkubwayo anali na cizoloŵezi comasulila anthu mkaidi mmodzi amene iwo afuna. 16 Pa nthawiyi anali kusunga mkaidi wina woopsa kwambili, dzina lake Baraba. 17 Cotelo iwo atasonkhana pamodzi, Pilato anawafunsa kuti: “Kodi mufuna nikumasulileni ndani, Baraba kapena Yesu, amene anthu amamucha Khristu?” 18 Pakuti Pilato anali kudziŵa kuti iwo anamupeleka cifukwa ca kaduka. 19 Komanso atakhala pa mpando woweluzila milandu, mkazi wake anamutumizila uthenga wakuti: “Nkhani ya munthu wolungamayu isakukhudzeni, cifukwa navutika kwambili m’maloto lelo kaamba ka munthu ameneyu.” 20 Koma ansembe aakulu komanso akulu analimbikitsa khamu la anthulo kupempha kuti Baraba amasulidwe ndipo Yesu aphedwe. 21 Conco, bwanamkubwa uja anawafunsa kuti: “Kodi mufuna nikumasulileni ndani pa aŵiliwa?” Iwo anayankha kuti: “Baraba!” 22 Pilato anawafunsanso kuti: “Nanga nicite naye ciyani Yesu, amene anthu amamucha kuti Khristu?” Anthu onsewo anayankha kuti: “Apacikidwe!”* 23 Iye anati: “Cifukwa ciyani? Walakwanji?” Koma m’pamene anthuwo anafuula mwamphamvu kuti: “Apacikidwe ndithu!”
24 Pilato ataona kuti sizikuthandiza, koma cipolowe cifuna kuyamba, anatenga madzi na kusamba m’manja khamulo likuona n’kunena kuti: “Nilibe mlandu wa magazi a munthu uyu. Zonse zili kwa inu.” 25 Pamenepo anthu onsewo anayankha kuti: “Magazi ake akhale pa ife komanso pa ana athu!” 26 Basi Pilato anawamasulila Baraba, koma analamula kuti Yesu akwapulidwe. Kenako anamupeleka kuti akaphedwe pa mtengo.
27 Ndiyeno asilikali a bwanamkubwa anatenga Yesu n’kupita naye ku nyumba kwa bwanamkubwayo, ndipo anasonkhanitsa asilikali onse n’kumuzungulila. 28 Ndiyeno anamuvula zovala n’kumuveka cinsalu cofiila kwambili. 29 Kenako analuka cisoti cacifumu caminga n’kumuveka kumutu, komanso anam’patsa bango m’dzanja lake lamanja. Ndipo anamugwadila n’kuyamba kukamba momunyodola kuti: “Moni,* inu Mfumu ya Ayuda!” 30 Iwo anamuthila mata. Kenako anatenga bangolo n’kuyamba kumumenya nalo pamutu. 31 Pambuyo, pomucita zacipongwezo, anamuvula cinsalu cija n’kumuveka zovala zake zakunja, ndipo anapita naye kukam’khomelela pa mtengo.
32 Pamene anali kupita, anakumana na munthu wina wa ku Kurene, dzina lake Simoni. Iwo analamula munthuyo kuti anyamule mtengo wozunzikilapo* wa Yesu. 33 Ndipo atafika pa malo ochedwa Gologota, kutanthauza Malo a Cigoba, 34 anamupatsa vinyo wosakaniza na ndulu* kuti amwe. Koma ataulaŵa, anakana kumwa. 35 Iwo atamukhomelela pa mtengo, anagaŵana zovala zake zakunja mwa kucita maele, 36 ndipo anakhala pansi pomwepo n’kumamulonda. 37 Komanso pamwamba pa mutu wake anakhomapo cikwangwani coonetsa mlandu umene anamuimba. Analembapo kuti: “Uyu ni Yesu Mfumu ya Ayuda.”
38 Ndiyeno acifwamba aŵili anapacikidwa pafupi naye, mmodzi ku dzanja lake lamanja, wina kumanzele kwake. 39 Ndipo anthu opita m’njila anali kumunena monyoza n’kumapukusa mitu yawo. 40 Iwo anali kunena kuti: “Iwe amene unali kunena kuti ukhoza kugwetsa kacisi n’kumumanga m’masiku atatu cabe, dzipulumutse! Ngati ndiwedi mwana wa Mulungu, tsika pa mtengo wozunzikilapowo!”* 41 Nawonso ansembe aakulu pamodzi na alembi komanso akulu anayamba kumunyodola n’kumanena kuti: 42 “Anali kupulumutsa ena, koma cam’kanga kuti adzipulumutse yekha. Ngati iye ni Mfumu ya Aisiraeli atsike pa mtengo wozunzikilapowo* tione, ndipo tidzam’khulupilila. 43 Iye amakhulupilila Mulungu. Amupulumutse tione ngati afuna kum’thandiza, cifukwa anali kunena kuti, ‘Ndine Mwana wa Mulungu.’” 44 Nawonso acifwamba amene anapacikidwa pa mitengo pafupi naye anali kumunyoza.
45 Kuyambila ca m’ma 12 koloko masana,* m’dziko lonselo munacita mdima mpaka ca m’ma 3 koloko masana.* 46 Ca m’ma 3 koloko momwemo, Yesu anafuula mokweza kuti: “Eli, Eli, lama sabakitani?” kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, n’cifukwa ciyani mwanilekelela?” 47 Atamva zimenezi, ena mwa amene anaimilila pamenepo anayamba kunena kuti: “Munthu uyu akuitana Eliya.” 48 Nthawi yomweyo mmodzi wa iwo anathamanga kukatenga cinkhupule n’kuciviika mu vinyo wowawasa. Kenako anaciika ku bango na kum’patsa kuti amwe. 49 Koma enawo ananena kuti: “Mulekeni! Tione ngati Eliyayo abwela kudzam’pulumutsa.” 50 Yesu anafuulanso mokweza, kenako anatsilizika.*
51 Nthawi yomweyo, cinsalu cochinga ca m’nyumba yopatulika cinang’ambika pakati, kucokela pamwamba mpaka pansi, ndipo dziko linagwedezeka komanso matanthwe anang’ambika. 52 Manda* anatseguka, moti mitembo yambili ya anthu oyela amene anaikidwa mmenemo, inaponyedwa kunja, 53 ndipo inaonekela kwa anthu ambili. (Yesu ataukitsidwa, anthu amene anali kubwela kucokela ku mandawo analoŵa mu mzinda woyela). 54 Koma kapitawo wa asilikali, na aja amene anali naye polonda Yesu, ataona civomezico na zimene zinali kucitika, anacita mantha kwambili ndipo anati: “Ameneyu analidi Mwana wa Mulungu.”
55 Komanso azimayi ambili anali kumeneko, ndipo anali kuona capatali. Iwo anali atatsatila Yesu pamene iye anali kucoka ku Galileya kuti azim’tumikila. 56 Ena mwa iwo anali Mariya Mmagadala, Mariya mayi wa Yakobo na Yose, komanso mayi wa Yakobo na Yohane.*
57 Ndiyeno madzulo, kunabwela munthu wina wacuma wa ku Arimateya, dzina lake Yosefe. Nayenso anali atakhala wophunzila wa Yesu. 58 Iye anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. Pilato analamula kuti amupatse mtembowo. 59 Yosefe anatenga mtembowo n’kuukulunga m’nsalu yoyela komanso yabwino kwambili, 60 ndipo anapita kukauika m’manda* ake atsopano, amene anali atagoba m’thanthwe. Kenako anatseka pa khomo la mandawo* mwa kugubuduzilapo cimwala cacikulu. Pambuyo pake anacoka. 61 Koma Mariya Mmagadala na Mariya wina uja anakhalabe komweko. Iwo anakhala pansi pafupi na mandawo.
62 Tsiku lotsatila, pambuyo pa tsiku la Cikonzekelo, ansembe aakulu komanso Afarisi anasonkhana pamodzi pamaso pa Pilato 63 na kunena kuti: “Bwana, tikumbukila kuti munthu wonyenga uja akali moyo ananena kuti, ‘Pambuyo pa masiku atatu, nidzauka.’ 64 Conco lamulani kuti pamandapo pakhale citetezo cokhwima kufikila tsiku lacitatu, kuti ophunzila ake asapite kukamuba n’kumauza anthu kuti, ‘Anauka kwa akufa!’ Ngati izi zingacitike, ndiye kuti cinyengo cothelaci cidzakhala coipa kwambili kuposa coyamba cija.” 65 Pilato anawauza kuti: “Tengani asilikali olonda. Pitani mukakhwimitse citetezo mmene mudziŵila.” 66 Conco iwo anapita kukakhwimitsa citetezo pamandapo mwa kumata pa khomo la mandawo, pomwe panali potseka na cimwala na kuikapo asilikali olonda.
28 Pambuyo pa tsiku la Sabata, m’matandakuca pa tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya Mmagadala na Mariya wina uja anapita kukaona mandawo.
2 Ndipo panali patacitika civomezi camphamvu, cifukwa mngelo wa Yehova anali atatsika kumwamba na kubwela kudzagubuduzila kumbali cimwalaco n’kukhalapo. 3 Maonekedwe ake anali owala ngati mphenzi, ndipo zovala zake zinali zoyela mbee! 4 Cifukwa coopa mngeloyo, alondawo ananjenjemela, ndipo anauma gwa ngati akufa!
5 Koma mngeloyo anauza azimayi aja kuti: “Musacite mantha cifukwa nidziŵa kuti mukufuna Yesu, amene anamuphela pa mtengo. 6 Iye sali kuno cifukwa wauka kwa akufa, monga ananenela. Bwelani muone pamene panali mtembo wake. 7 Ndiyeno pitani mwamsanga mukauze ophunzila ake kuti iye wauka kwa akufa, ndipo watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona kumeneko. Musaiŵale zimene nakuuzani.”
8 Nthawi yomweyo, azimayiwo anacoka pa mandapo ali na mantha komanso cisangalalo cosaneneka. Ndipo anathamanga kukauza ophunzila ake zimenezi. 9 Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo n’kunena kuti, “Moni azimayi!” Iwo anafika pafupi na iye. Ndiyeno anagwada na kugwila mapazi ake n’kumuŵelamila. 10 Kenako Yesu anawauza kuti: “Musacite mantha! Pitani mukauze abale anga kuti apite ku Galileya, ndipo akaniona kumeneko.”
11 Ali m’njila, ena mwa asilikali olonda aja anapita mu mzinda kukafotokozela ansembe aakulu zonse zimene zinacitika. 12 Ansembe aakuluwo anakumana pamodzi na akulu n’kukambilana nkhaniyo. Kenako anapeleka ndalama zambili zasiliva kwa asilikaliwo 13 n’kuwauza kuti: “Muzinena kuti, ‘Ophunzila ake anabwela usiku n’kuba mtembo wake ife tili mtulo.’ 14 Ndipo bwanamkubwa akamva za nkhaniyi, tikamba naye.* Inu musade nkhawa.” 15 Conco, anatenga ndalama zasilivazo n’kucita mmene anawalangizila, ndipo nkhaniyi yakhala yofala pakati pa Ayuda mpaka lelo.
16 Koma ophunzila 11 aja anapita ku Galileya, ku phili, kumene Yesu anawauza kuti akakumane. 17 Atamuona, anamugwadila, koma ena anakayikila ngati analidi Yesu. 18 Yesu anafika pafupi n’kuwauza kuti: “Ulamulilo wonse wapelekedwa kwa ine, kumwamba na padziko lapansi. 19 Conco pitani mukapange anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila. Muziwabatiza m’dzina la Atate, la Mwana, komanso la mzimu woyela, 20 na kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene n’nakulamulani. Ndipo dziŵani kuti ine nili nanu pamodzi masiku onse mpaka cimalizilo ca nthawi ino.”*
Kapena kuti, “mzele wa makolo a.”
Kapena kuti, “Mesiya; Wodzozedwa.”
Kapena kuti, “mphamvu ya Mulungu yogwila nchito.”
M’cikhalidwe ca Ayuda, anthu akatomelana anali kuwaona ngati ni okwatilana.
M’Baibo ino, awa ni malo oyamba pa malo 237 m’Malemba a Cigiriki a Cikhristu pamene pakupezeka dzina la Mulungu lakuti Yehova.
Dzinali, m’Ciheberi ni Yesuwa kapena kuti Yoswa, kutanthauza kuti “Yehova Ndiye Cipulumutso.”
Kapena kuti, “Mesiya; Wodzozedwa.”
Cioneka kuti dzinali linacokela ku liwu la Ciheberi lotanthauza kuti “mphukila.”
Kapena kuti, “kuwaviika; kuwamiza.”
“Mankhusu” ni makoko amene amacotsa ku mbewu monga mpunga akapuntha, ndipo amatha kuwauluza.
Kapena kuti, “pamwamba pa mpanda wa.”
Kapena kuti, “Cigawo ca Mizinda 10.”
Malo amene anali kutenthelako zinyalala kunja kwa Yerusalemu. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani “Matanthauzo a Mawu Ena.”
Onani “Matanthauzo a Mawu Ena.”
M’Cigiriki, por nei’a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kutanthauza kubweleka popanda ciwongoladzanja.
Kapena kuti, “kukhala okwanila.”
Mawu ake enieni, “cilungamo canu.”
Kapena kuti, “mphatso kwa osauka.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “lionedwe kuti ni lopatulika; lionedwe kuti ni loyela.”
Mawu ake enieni, “nkhongole zathu.”
Mawu ake enieni, “ali nafe nkhongole.”
Kapena kuti, “mutipulumutse.”
Kapena kuti, “amaleka kudzisamalila.”
Kapena kuti, “limaona bwino.”
Mawu ake enieni, “loipa.”
Mawu ake enieni, “na mkono umodzi.”
Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”
Mawu ake enieni, “alibe kulikonse kumene angasamile mutu wake.”
Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
Kapena kuti, “wokangalika.”
Kapena kuti, “covala cosinthila.”
Kapena kuti, “amene wapilila.”
Dzina la Satana, kalonga, kapena kuti wolamulila wa ziŵanda.
Kutanthauza ciyembekezo codzakhalanso na moyo m’tsogolo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “zovala zabwino kwambili.”
Kapena kuti, “zotulukapo zake.”
Kapena kuti, “Hade,” kutanthauza manda a anthu onse.
Dzina la Satana.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “wosakhulupilika.”
Kapena kuti, “mawuwo samufika pa mtima.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kamasulidwe kena, “kucokela pa kukhazikitsidwa kwa dziko.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ameneyu ni Herode Antipa.
Mawu ake enieni, “masitadiya ambili.” Sitadiya imodzi inali yaitali mamita 185.
Nthawiyi inali kuyamba ca m’ma 3 koloko usiku mpaka dzuŵa litatuluka ca m’ma 6 koloko.
Kutanthauza kusamba m’manja motsatila mwambo.
Kutanthauza kuti, “asawathandize.”
M’Cigiriki por nei’a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kutanthauza kusasamba m’manja motsatila mwambo.
Kapena kuti, “wosakhulupilika.”
Kapena kuti, “mphamvu za imfa.” Mawu ake enieni, “mageti a Hade.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “zinayela kwambili.”
Kapena kuti, “ngati simusintha.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kamasulidwe kena, “Atate wanu.”
Mawu ake enieni, “ukamudzudzule.”
Mawu ake enieni, “ikatsimikizike na pakamwa pa.”
Matalente 10,000 a siliva zinali ndalama zofanana na madinari 60,000,000.
M’Cigiriki por nei’a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “wokwanila.”
Mawu ake enieni, “pafupifupi ola lacitatu.”
Mawu ake enieni, “pafupifupi ola la 6.”
Mawu ake enieni, “pafupifupi ola la 9.”
Mawu ake enieni, “pafupifupi ola la 11.”
Mawu ake enieni, “ni loipa.”
Kapena kuti, “wowolowa manja.”
Mwala umenewu anali kuuika pa kona ya nyumba, pomwe zipupa ziŵili zimakumana.
Kapena kuti, “kumumanga.”
Kapena kuti, “kodi n’koyenela.”
Kapena kuti, “yabwino kwambili.”
Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ni dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Minti, dilili, na kumini ni tomela tokometsela cakudya tumene anthu amalima.
Kapena kuti, “khalidwe lolanda zinthu.”
Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kamasulidwe kena, “Nyumba yanu yasiidwa kwa inu ili bwinja.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “zoŵaŵa za pobeleka.”
Kapena kuti, “amene wapilila.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “akanadziŵa kuti mbala ibwela pa ulonda uti.”
Kapena kuti, “anzelu.”
Talente ya Agiriki inali yolemela makilogilamu 20.4.
Mawu ake enieni, “siliva.”
Mawu ake enieni, “siliva.”
Kapena kuti, “wosavala mokwanila.”
Mawu ake enieni, “adzadulidwa; adzasadzidwa.”
Kapena kuti, “amumange.”
Kapena kuti, “zaciwawa.”
Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ni dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.
Kapena kuti, “nyimbo zauzimu; masalimo.”
Kapena kuti, “mzimu ufuna.”
Kapena kuti, “malemba a aneneli akwanilitsidwe.”
Mawu ake enieni, “kudzitembelela.”
Kapena kuti, “Ilo ni vuto lako.”
Kapena kuti, “akaphedwe pa mtengo!”
Kapena kuti, “Mutamandike.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Apa, mawu akuti “ndulu” angatanthauze zinazake zamadzimadzi zoŵaŵa.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu ake enieni, “ola la 6.”
Mawu ake enieni, “ola la 9.”
Kapena kuti, “anapeleka mzimu wake.”
Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
Mawu ake enieni, “mayi wa ana a Zebedayo.”
Kapena kuti, “m’manda acikumbutso.”
Kapena kuti, “manda acikumbutsowo.”
Kapena kuti, “tidzamunyengelela.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.