LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • nwt Aefeso 1:1-6:24
  • Aefeso

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Aefeso
  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Aefeso

KALATA KWA AEFESO

1 Ine Paulo, amene ndinakhala mtumwi wa Khristu Yesu malinga ndi cifunilo ca Mulungu, ndikulembela oyela amene ali ku Efeso, amene ali mu mgwilizano ndi Khristu Yesu, amenenso ndi okhulupilika kuti:

2 Cisomo komanso mtendele wa Mulungu Atate wathu, ndi wa Ambuye Yesu Khristu zikhale nanu.

3 Atamandike Mulungu komanso Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, cifukwa watidalitsa ndi dalitso lililonse lauzimu m’malo akumwamba. Wacita zimenezi cifukwa cakuti tili mu mgwilizano ndi Khristu. 4 Iye anatisankha dziko lisanakhazikitsidwe* kuti tikhale mu mgwilizano ndi Khristu. Anatelo kuti tizionetsa cikondi, komanso kuti tikhale oyela ndiponso opanda cilema pamaso pake. 5 Popeza anatisankhilatu kuti adzatitenga n’kukhala ana ake kudzela mwa Yesu Khristu, mogwilizana ndi zimene zinamusangalatsa komanso zimene anafuna. 6 Anatelo kuti iye atamandike cifukwa ca cisomo caulemelelo cimene anaticitila kudzela mwa mwana wake wokondedwa. 7 Mwa Mwana wakeyo tinamasulidwa ndi dipo* la magazi ake. Inde, takhululukidwa macimo athu mwa cisomo cake.

8 Iye anaonetsetsa kuti cisomo cimeneci casefukila kwa ife potithandiza kuti tikhale anzelu komanso ozindikila, 9 potiululila cinsinsi cake copatulika cokhudza cifunilo cake. Cinsinsico n’cogwilizana ndi zimene zimamukondweletsa ndiponso cifunilo cake, 10 cakuti pakhale dongosolo pa nthawi imene anaikilatu. Dongosolo limenelo ndi kusonkhanitsa zinthu zonse pamodzi mwa Khristu, za kumwamba ndi za padziko lapansi. Inde, mwa iye 11 amene tili naye mu mgwilizano ndipo tidzalandila naye limodzi colowa. Pakuti tinasankhidwa pasadakhale mogwilizana ndi colinga ca iye amene amacita zinthu zonse malinga ndi cifunilo cake. 12 Anatelo kuti ife amene ndife oyamba kukhala ndi ciyembekezo mwa Khristu titamande Mulungu cifukwa iye ndi wamkulu. 13 Inunso munakhala ndi ciyembekezo mwa iye mutamva mau a coonadi, inde uthenga wabwino wa cipulumutso canu. Mutakhulupilila, Mulungu anagwilitsa nchito mzimu woyela umene analonjeza kuti akuikeni cidindo, ndipo anasewenzetsa Khristu pocita zimenezi. 14 Mzimu woyela umenewo ndi cikole cotitsimikizila kuti tidzalandila colowa cathu. Mulungu anatelo n’colinga cakuti anthu, amene ndi cuma cake, akamasulidwe kupyolela m’dipo. Izi zidzacititsa kuti citamando ndi ulemelelo wonse zipite kwa iye.

15 Pa cifukwa cimeneci, inenso kuyambila pamene ndinamva za cikhulupililo cimene muli naco mwa Ambuye Yesu, komanso cikondi cimene mumaonetsa oyela onse, 16 sindinaleke kuyamikila Mulungu cifukwa ca inu. Ndikupitiliza kukupemphelelani, 17 kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate waulemelelo, akupatseni mzimu wa nzelu ndi wa bvumbulutso kuti mukhale ndi cidziwitso colongosoka pa iye. 18 Mulungu waunikila mitima yanu kuti muone komanso kuti mudziwe ciyembekezo cimene anakuitanilani, inde cuma caulemelelo cimene amapeleka ngati colowa kwa oyela, 19 komanso kuti mudziwe kukula kwa mphamvu zake zopambana zimene amazionetsa kwa ife okhulupilila. Mphamvu zake zazikuluzo zikuonekela m’nchito zake. 20 Iye anazigwilitsa nchito poukitsa Khristu kwa akufa n’kumukhazika kudzanja lake lamanja m’malo akumwamba. 21 Anamukweza kuposa boma lililonse, ulamulilo uliwonse, amphamvu onse, ambuye onse, ndi aliyense amene ali ndi dzina laulemu, osati m’nthawi* ino yokha, koma ngakhale imene ikubwelayo. 22 Mulungu anaikanso zinthu zonse pansi pa mapazi ake, ndipo anamuika kuti akhale mutu wa zonse zokhudzana ndi mpingo. 23 Mpingowo ndi thupi la Khristu, ndipo ndi wodzazidwa ndi Khristuyo amene amadzaza zinthu zonse mokwanila.

2 Kuonjezela apo, Mulungu anapangitsa kuti mukhale amoyo ngakhale kuti munali akufa cifukwa ca zolakwa zanu komanso macimo anu. 2 Pa nthawi ina munali kuyenda m’zimenezo malinga ndi nthawi* ya m’dzikoli, pomvela wolamulila wa mpweya umene umalamulila zocita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe kameneka, tsopano kakugwila nchito mwa ana osamvela. 3 Inde pa nthawi ina pamene tinali kukhala pakati pao, tinali kucita zinthu motsatila zilakolako za thupi lathu. Tinali kucita zofuna za thupi ndi maganizo athu, ndipo mwacibadwa tinali ana oyenela kulandila mkwiyo wa Mulungu, mofanana ndi ena onse. 4 Koma popeza Mulungu ndi wacifundo cacikulu, komanso cifukwa ca cikondi cake cacikulu cimene anationetsa, 5 anapangitsa kuti tikhale amoyo limodzi ndi Khristu, ngakhale kuti tinali akufa cifukwa ca macimo athu. Ndipotu inu mwapulumutsidwa cifukwa ca cisomo cake. 6 Kuonjezela apo, Mulungu anatiukitsa limodzi, ndi kutikhazika limodzi m’malo akumwamba mu mgwilizano ndi Khristu Yesu. 7 Anatelo kuti mu nthawi zimene zikubwela, iye adzationetse cuma copambana ca cisomo cake m’cigwilizano ndi Khristu Yesu.

8 Mwa cisomo cimeneci, inu mwapulumutsidwa kudzela m’cikhulupililo. Sikuti zimenezi zatheka cifukwa ca khama lanu ayi, koma ndi mphatso ya Mulungu. 9 Zimenezi sizinatheke cifukwa ca nchito, kuti munthu asakhale ndi cifukwa codzitamandila. 10 Ife ndife nchito ya manja a Mulungu. Iye ndi amene anatilenga, ndipo tili mu mgwilizano ndi Khristu Yesu kuti ticite nchito zabwino, zimene Mulungu anakonzelatu kuti tiyendemo.

11 Conco, muzikumbukila kuti panthawi ina, inunso munali anthu a mitundu ina. Anthu “odulidwa” anali kukuchulani kuti anthu “osadulidwa.” Mdulidwe umenewu umacitika pa thupi ndi manja a anthu. 12 Panthawi imeneyo Khristu simunali kumudziwa. Munali otalikilana ndi mtundu wa Isiraeli, ndipo simunali nao m’zipangano za lonjezo. Munalibe ciyembekezo, ndipo Mulungu simunali kumudziwa m’dzikoli. 13 Koma tsopano popeza muli mu mgwilizano ndi Khristu Yesu, inu amene pa nthawi ina munali kutali, mwabwela pafupi cifukwa ca magazi ake. 14 Pakuti iye ndiye mtendele wathu, iye amene anaphatikiza magulu awili aja kukhala gulu limodzi, n’kugwetsa cipupa cowalekanitsa comwe cinali pakati pao. 15 Ndi thupi lake anacotsapo cinthu coyambitsa cidani comwe ndi Cilamulo, cokhala ndi malamulo komanso malangizo. Anacicotsapo kuti magulu awili omwe ali mu mgwilizano ndi iye akhale munthu mmodzi watsopano, ndi kuti akhazikitse mtendele. 16 Kuonjezela apo anatelo kuti kudzela mwa mtengo wozunzikilapo, ayanjanitse magulu awili a anthuwo kwa Mulungu, kutinso anthuwo akhale thupi limodzi cifukwa anali ataphelatu cidanico kudzela mwa iye mwini. 17 Cotelo iye anabwela kudzalengeza uthenga wabwino wa mtendele kwa inu amene munali kutali. Analengezanso za mtendele kwa amene anali pafupi. 18 Anatelo cifukwa kudzela mwa iye, ife, magulu onse awili, tingathe kufika kwa Atate mosabvuta kudzela mwa mzimu umodzi.

19 Conco simulinso anthu osadziwika kapena alendo, koma mofanana ndi oyelawo inunso ndinu nzika, ndipo ndinu a m’banja la Mulungu. 20 Mwamangidwa pamaziko a atumwi ndi aneneli, ndipo Khristu Yesu ndiye mwala wapakona wa mazikowo. 21 Mwa iye, nyumba yonse popeza ndi yolumikizika bwino, ikukula n’kukhala kacisi woyela wa Yehova. 22 Inunso mukumangidwa pamodzi mu mgwilizano ndi iye kuti mukhale malo oti Mulungu akhalemo mwa mzimu.

3 Cotelo, ine Paulo, ndili m’ndende cifukwa ndili kumbali ya Khristu Yesu komanso cifukwa cothandiza inu, anthu a mitundu ina—. 2 Ndithudi, munamva kuti ndinalandila udindo wokuthandizani kuti mupindule ndi cisomo ca Mulungu, 3 ndiponso kuti anandibvumbulila cinsinsi copatulika, malinga ndi zimene ndinalemba mwacidule m’mbuyomu. 4 Conco mukawelenga izi, mudzatha kuzindikila kuti ndimacimvetsa bwino cinsinsi copatulika conena za Khristu. 5 M’mibadwo ya m’mbuyo, cinsinsi cimeneci sicinabvumbulidwe kwa ana a anthu mmene Mulungu wacibvumbulila pano kwa atumwi ndi aneneli ake oyela kudzela mwa mzimu. 6 Cinsinsi cimeneci n’cakuti anthu a mitundu ina amene ali mu mgwilizano ndi Khristu Yesu, adzalandile colowa cimene Khristu adzalandile, ndipo adzakhala mbali ya thupi. Iwo adzalandilanso zinthu zimene Mulungu watilonjeza cifukwa ca uthenga wabwino. 7 Ndinakhala mtumiki wa zimenezi malinga ndi mphatso yaulele ya cisomo ca Mulungu, imene anandipatsa kudzela mu mphamvu yake.

8 Cisomo cimeneci cinaonetsedwa kwa ine munthu wamng’ono pondiyelekezela ndi wamng’ono kwambili pa oyela onse. Anandicitila cisomo cimeneci kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa anthu a mitundu ina wonena za cuma copanda polekezela ca Khristu, 9 ndiponso kuti ndithandize aliyense kuona mmene cinsinsi copatulikaco cikuyendetsedwela. Kwa zaka zambili Mulungu amene analenga zinthu zonse, wakhala akubisa cinsinsici. 10 Zinatelo kuti kupitila mumpingo, maboma ndi maulamulilo amene ali m’malo akumwamba, tsopano adziwe mbali zosiyana-siyana za nzelu za Mulungu. 11 Izi n’zogwilizana ndi colinga camuyaya cimene iye anakhala naco cokhudza Khristu, yemwe ndi Yesu Ambuye wathu. 12 Kudzela mwa iye, tili ndi ufulu wa kulankhula umenewu, ndiponso timatha kufika kwa Mulungu mosabvuta komanso mwa cidalilo, popeza timakhulupilila Yesu. 13 Cotelo ndikukupemphani kuti musabwelele m’mbuyo poona masautso amene ndikukumana nao cifukwa ca inu, pakuti masautsowa adzakubweletselani ulemelelo.

14 Pa cifukwa cimeneci ndikugwada kwa Atate, 15 amene amapangitsa banja lililonse kumwamba ndi padziko lapansi kuti likhale ndi dzina. 16 Ndikupempha kuti Mulungu amene ali ndi ulemelelo waukulu, akuloleni kuti munthu wanu wamkati akhale wamphamvu posewenzetsa mphamvu imene mzimu wake umapeleka. 17 Ndikupemphanso kuti mwa cikhulupililo canu, m’mitima yanu mukhale Khristu komanso cikondi. Muzike mizu ndiponso mukhale okhazikika pamaziko ake, 18 n’colinga coti inu limodzi ndi oyela onse muthe kumvetsa bwino mulifupi, mulitali, kukwela, ndi kuzama kwa coonadi, 19 komanso kuti mudziwe cikondi ca Khristu cimene cimaposa kudziwa zinthu, kuti mudzazidwe ndi makhalidwe onse amene Mulungu amapeleka.

20 Tsopano kwa iye amene angathe kucita zazikulu kwambili kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza, malinga ndi mphamvu yake imene ikugwila nchito mwa ife, 21 kwa iye kukhale ulemelelo kudzela ku mpingo komanso kupitila mwa Khristu Yesu, kumibadwo yonse mpaka muyaya. Ameni.

4 Cotelo, ine amene ndine mkaidi cifukwa ca Ambuye, ndikukucondelelani kuti muziyenda malinga ndi ciitano cimene munalandila. 2 Muziyenda modzicepetsa kwambili,* mofatsa, moleza mtima, ndiponso muzilolelana wina ndi mnzake mwacikondi. 3 Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi umene mzimu woyela umatithandiza kukhala nao kudzela mu mtendele, umene uli ngati comangila cotigwilizanitsa. 4 Pali thupi limodzi ndi mzimu umodzi, mogwilizana ndi ciyembekezo cimodzi cimene anakuitanilani. 5 Palinso Ambuye mmodzi, cikhulupililo cimodzi, ndi ubatizo umodzi. 6 Palinso Mulungu mmodzi, amenenso ndi Atate wa anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwila nchito kudzela mwa onse, ndipo ali mwa onse.

7 Tsopano aliyense wa ife anacitilidwa cisomo malinga ndi mmene Khristu anamupimila mphatso yauleleyi. 8 Paja Malemba amati: “Atakwela pamalo apamwamba anatenga anthu ogwidwa ukapolo, ndipo anapeleka mphatso za amuna.” 9 Ndiye kodi liu lakuti “atakwela” limatanthauza ciani? Limatanthauza kuti coyamba anatsika pansi, kutanthauza padziko lapansi. 10 Amene anatsikayo ndi amenenso anakwela kukakhala pamwamba kwambili kuposa kumwamba konse, kuti akwanilitse zinthu zonse.

11 Pa mphatso zimene anapelekazo, anapeleka ena kukhala atumwi, ena aneneli, ena alaliki,* ena abusa, ndipo ena aphunzitsi. 12 Anatelo pofuna kuthandiza* oyelawo kuti aziyenda m’njila yoyenela, kuti azigwila nchito yotumikila ena, komanso kuti amange mpingo umene ndi thupi la Khristu. 13 Colinga n’cakuti tonse tidzakhale ogwilizana pa zimene timakhulupilila, komanso podziwa molondola Mwana wa Mulungu. Zikadzatelo, tidzakhala acikulile, amene afika pamsinkhu wa munthu wamkulu, ngati umene Khristu anafikapo. 14 Conco tisakhalenso ana, otengeka-tengeka ngati kuti mafunde akutikankha, ndiponso otengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya ciphunzitso conyenga ca anthu, ya mabodza amene anthu amapeka mwamacenjela. 15 Koma tizilankhula zoona ndiponso kuonetsana cikondi. Tikatelo tidzakhala acikulile m’zinthu zonse, ndipo tidzatha kucita zinthu mogwilizana ndi Khristu, amene ndi mutu. 16 Tili ngati thupi, ndipo cifukwa ca iye, ziwalo zonse za thupi limeneli ndi zolumikizana bwino, ndipo zimathandizana kuti thupilo lizigwila bwino nchito. Ciwalo ciliconse ca thupili cikamagwila nchito yake thupili limakula bwino ndipo limamangika m’cikondi.

17 Conco ndikunena komanso kucitila umboni mwa Ambuye, kuti muleke kuyenda ngati mmene anthu a mitundu ina amayendela, potsatila maganizo ao opanda pake.* 18 Maganizo ao ali mumdima, ndipo iwo ndi otalikilana ndi moyo wocokela kwa Mulungu cifukwa ca umbuli wao, komanso cifukwa ca kuuma mtima kwao. 19 Popeza iwo sakukwanitsanso kuzindikila makhalidwe abwino, anadzipeleka okha ku khalidwe lotayilila,* kuti acite zonyansa za mtundu uliwonse mwadyela.

20 Koma inu simunaphunzile Khristu kukhala wotelo. 21 Zikanakhala conco ngati munamvadi zimene anali kuphunzitsa komanso ngati iye ndiye anakuphunzitsani, paja coonadi cili mwa Yesu. 22 Munaphunzitsidwa kuti mubvule umunthu wakale umene umagwilizana ndi makhalidwe anu akale umenenso ukuipitsidwa ndi zilakolako za umunthuwo. 23 Ndipo pitilizani kusintha kuti mukhale atsopano pa kaganizidwe kanu.* 24 Komanso mubvale umunthu watsopano umene unalengedwa malinga ndi cifunilo ca Mulungu m’cilungamo ceniceni ndi kukhulupilika.

25 Conco, popeza tsopano mwataya cinyengo, aliyense wa inu azilankhula zoona kwa mnzake, cifukwa ndife ziwalo zolumikizana. 26 Kwiyani, koma musacimwe. Dzuwa lisalowe muli cikwiile. 27 Musamupatse mpata* Mdyelekezi. 28 Munthu wakuba asiye kubako, koma azigwila nchito mwakhama. Azigwila nchito yabwino ndi manja ake kuti azikwanitsa kupeza zinthu zimene angagawane ndi munthu wosowa. 29 Pakamwa panu pasamatuluke mau owola, koma pazituluka mau abwino okha, kuti alimbikitse ena pakafunika kutelo, kutinso apindulile anthu amene akumvetsela. 30 Komanso musamamvetse cisoni mzimu woyela wa Mulungu, umene iye anausewenzetsa pokuikani cidindo kaamba ka tsiku limene mudzapulumutsidwe ndi dipo.

31 Cidani, kupsya mtima, mkwiyo, kulalata, mau acipongwe, komanso zinthu zonse zoipa zicotsedwe mwa inu. 32 Koma muzikomelana mtima, muzicitilana cifundo, komanso muzikhululukilana ndi mtima wonse, ngati mmene inunso Mulungu anakukhululukilani ndi mtima wonse kupitila mwa Khristu.

5 Conco muzitengela Mulungu monga ana ake okondedwa. 2 Ndipo pitilizani kukondana ngati mmene Khristu anatikondela,* n’kudzipeleka yekha cifukwa ca ife* ngati copeleka, ndiponso ngati nsembe ya pfungo lokoma kwa Mulungu.

3 Nkhani za ciwelewele* komanso conyansa ca mtundu uliwonse, kapena umbombo, zisachulidwe n’komwe pakati panu, cifukwa anthu oyela sayenela kucita zimenezi. 4 Musachulenso nkhani zokhudza khalidwe locititsa manyazi, nkhani zopusa, kapena nthabwala zotukwana, cifukwa ndi zinthu zosayenela. M’malomwake, muziyamika Mulungu. 5 Pakuti mfundoyi mukuidziwa ndi kuimvetsa bwino, kuti munthu waciwelewele,* wodetsedwa, kapena waumbombo, kumene ndi kulambila mafano, sadzalowa mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.

6 Munthu aliyense asakupusitseni ndi mau opanda pake, cifukwa ana osamvela amene akucita zinthu zimene ndachulazi, mkwiyo wa Mulungu udzawafikila. 7 Conco musamacite zimene iwo amacita.* 8 Cifukwa poyamba munali mdima, koma tsopano ndinu kuwala, popeza muli mu mgwilizano ndi Ambuye. Pitilizani kuyenda monga ana a kuwala. 9 Cifukwa zipatso za kuwala ndi ciliconse cabwino, colungama, ndi coona. 10 Nthawi zonse muzitsimikizila kuti cobvomelezeka kwa Ambuye n’citi. 11 Ndipo musiye kucita nao nchito zosapindulitsa za mumdima. M’malomwake, muzizibvumbulilatu kuti n’zoipa. 12 Cifukwa zimene iwo amacita mseli ndi zocititsa manyazi ngakhale kuzichula. 13 Tsopano zinthu zonse zimene zabvumbulidwa* zimaonekela poyela cifukwa ca kuwala, popeza ciliconse cimene caonekela cimakhala kuwala. 14 N’cifukwa cake pali mau akuti: “Uka, wogona iwe! Uka kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.”

15 Conco samalani kuti mmene mukuyendela, si monga anthu opanda nzelu, koma ngati anthu anzelu. 16 Muziigwilitsa nchito bwino nthawi yanu* cifukwa masikuwa ndi oipa. 17 Pa cifukwa cimeneci, lekani kucita zinthu ngati anthu opanda nzelu, koma pitilizani kuzindikila cifunilo ca Yehova. 18 Ndiponso musaledzele ndi vinyo, cifukwa m’kuledzela muli makhalidwe otayilila. Koma pitilizani kudzazidwa ndi mzimu. 19 Muziimbila limodzi masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu, ndiponso nyimbo zauzimu. Muziimba motsagana ndi malimba nyimbo zotamanda Yehova m’mitima yanu. 20 Nthawi zonse muziyamika Mulungu Atate wathu pa zinthu zonse m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.

21 Muzigonjelana poopa Khristu. 22 Akazi azigonjela amuna ao ngati kuti akugonjela Ambuye, 23 popeza mwamuna ndi mutu wa mkazi wake monga mmene Khristu alili mutu wa mpingo. Pajanso iye ndiye mpulumutsi wa thupi limeneli. 24 Ndipo monga mmene mpingo umagonjelela Khristu, naonso akazi azigonjela amuna ao pa ciliconse. 25 Inu amuna, pitilizani kukonda akazi anu ngati mmene Khristu anakondela mpingo mpaka kufika podzipeleka kaamba ka mpingowo, 26 kuti auyeletse pousambika m’madzi a mau a Mulungu. 27 Anatelo kuti iye alandile mpingowo uli wokongola ndiponso waulemelelo, wopanda banga, makwinya, kapenanso ciliconse cofanana ndi zimenezi, koma kuti ukhale woyela ndi wopanda ulemali.

28 Mofananamo, amuna azikonda akazi ao monga mmene amakondela matupi ao. Mwamuna amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, 29 cifukwa palibe munthu amene anadanapo ndi thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulicengeta, monga mmene Khristu amacitila ndi mpingo, 30 popeza ndife ziwalo za thupi lake. 31 “Pa cifukwa cimeneci, mwamuna adzasiya atate ake ndi amai ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiliwo adzakhala thupi limodzi.” 32 Cinsinsi copatulikaci n’cacikulu. Apa ndikunena za Khristu ndi mpingo. 33 Komabe, aliyense wa inu azikonda mkazi wake ngati mmene amadzikondela yekha, komanso mkazi azilemekeza kwambili mwamuna wake.

6 Inu ana, muzimvela makolo anu mwa Ambuye, cifukwa kucita zimenezi n’koyenela. 2 “Muzilemekeza atate anu ndi amai anu.” Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Lonjezo lake ndi lakuti: 3 “Kuti zinthu zikuyendeleni bwino, ndiponso kuti mukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.” 4 Inu atate, musamakwiyitse ana anu, koma pitilizani kuwalela mwa kuwapatsa malangizo,* komanso kuwaphunzitsa malinga n’zimene Yehova amanena.

5 Inu akapolo, muzimvela ambuye anu. Muziwaopa ndi kuwalemekeza mocokela pansi pa mtima, ngati mmene mumacitila ndi Khristu. 6 Musacite zimenezi mwaciphamaso, cabe pofuna kukondweletsa anthu, koma ngati akapolo a Khristu amene akucita cifunilo ca Mulungu ndi mtima wonse. 7 Muzitumikila ambuye anu ndi mtima wonse ngati mukutumikila Yehova osati anthu, 8 popeza mukudziwa kuti ciliconse cimene munthu angacite, Yehova adzamupatsa mphoto, kaya munthuyo ndi kapolo kapena mfulu. 9 Inunso ambuye, muzicitila akapolo anu cimodzi-modzi. Musamawaopsyeze cifukwa mukudziwa kuti Ambuye wawo komanso wanu, ali kumwamba, ndipo alibe tsankho.

10 Pomaliza ndikuti, pitilizani kupeza mphamvu mwa Ambuye komanso mu nyonga zake zazikulu. 11 Bvalani zida zonse za nkhondo zocokela kwa Mulungu kuti musagonje polimbana ndi macenjela a* Mdyelekezi. 12 Pakuti sitikulimbana* ndi anthu a thupi la magazi ndi nyama ai. Koma tikulimbana ndi maboma, maulamulilo, olamulila dziko a mu mdimawu, komanso makamu a mizimu yoipa m’malo a kumwamba. 13 Pa cifukwa cimeneci, nyamulani zida zonse za nkhondo zocokela kwa Mulungu, kuti pa tsiku loipa musadzagonje, ndiponso kuti mukakwanitsa kucita zonse bwino-bwino, mudzathe kulimba.

14 Conco, khalani olimba, mutamanga kwambili coonadi m’ciuno mwanu ngati lamba, mutabvala codzitetezela pacifuwa cacilungamo, 15 komanso mutabvala nsapato kumapazi anu pokonzekela kulengeza uthenga wabwino wamtendele. 16 Kuonjezela apo, nyamulani cishango cacikulu cacikhulupililo, cimene mudzathe kuzimitsila naco mibvi yonse yoyaka moto ya woipayo. 17 Komanso bvalani cisoti ca cipulumutso, ndipo nyamulani lupanga la mzimu, lomwe ndi mau a Mulungu. 18 Pamene mukucita zimenezi, muzipemphela pa cocitika ciliconse mu mzimu, pogwilitsa nchito pemphelo ndi pembedzelo la mtundu uliwonse. Kuti zimenezi zitheke, khalani maso ndipo nthawi zonse muzipemphelela oyela onse mopembedzela. 19 Inenso muzindipemphelela kuti ndikayamba kulankhula, ndizipeza mau oyenelela kuti ndizitha kulankhula molimba mtima ndikamalalikila za cinsinsi copatulika ca uthenga wabwino, 20 umene ndine kazembe wake womangidwa ndi unyolo. Muzindipemphelela kuti ndizilankhula za uthengawo molimba mtima ngati mmene ndiyenela kucitila.

21 Tsopano kuti mudziwenso mmene zinthu zikuyendela pa umoyo wanga ndi mmene ndilili, Tukiko, m’bale wokondedwa ndiponso mtumiki wokhulupilika wa Ambuye, adzakufotokozelani zonse. 22 Ndi cimene ndamutumizila kwa inu kuti mudziwe za umoyo wathu, ndiponso kuti atonthoze mitima yanu.

23 Mtendele, cikondi, ndiponso cikhulupililo cocokela kwa Mulungu Atate ndi kwa Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu abale. 24 Cisomo cikhale pa onse amene ali ndi cikondi ceniceni pa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Kutanthauza Adamu ndi Hava asanayambe kukhala ndi ana.

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Kapena kuti, “Muziyenda ndi maganizo odzicepetsa.”

Kapena kuti, “olalikila uthenga wabwino.”

Kapena kuti, “kuphunzitsa.”

Kapena kuti, “nchito.”

Kapena kuti, “khalidwe locititsa manyazi.” M’Cigiriki a·sel′gei·a. OnaniMatanthauzo a Mau Ena.

Kapena kuti, “pa mphamvu yoyendetsa maganizo anu.” Kucokela ku Cigiriki, “pa mzimu wa maganizo anu.”

Kapena kuti, “malo.”

Ma Baibo ena amati, “anakukondelani.”

Ma Baibo ena amati, “inu”

M’Cigiriki, por·neiʹa. Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Onani Matanthauzo a Mau Ena, “Ciwelewele.”

Kapena kuti, “Conco musamaceze nao.”

Kapena kuti, “zadzudzulidwa.”

Kucokela ku Cigiriki, “Muzigula nthawi yoikidwilatu.”

Mau akuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambili. Angatanthauze malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.

Kapena kuti, “ndi ziwembu za.”

Kucokela ku Cigiriki, “sitikumenyana.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2026)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani