LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g21 na. 3 masa. 8-9
  • Zimene Asayansi Sangakwanitse Kutiuza

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zimene Asayansi Sangakwanitse Kutiuza
  • Galamuka!—2021
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Moyo Unayamba Bwanji?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Thandizani Ana Anu Kukhala na Cikhulupililo Colimba mwa Mlengi Wawo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Pendani Umboni
    Galamuka!—2021
Galamuka!—2021
g21 na. 3 masa. 8-9
Mphunzitsi wa sayansi akukambilana zinazake na ena mwa ana a m’kalasi yake.

Zimene Asayansi Sangakwanitse Kutiuza

Masiku ano, zimaoneka monga kuti asayansi anaphunzila za ciliconse m’cilengedwe. Komabe, pali mafunso ambili ofunika amene iwo sangakwanitse kuyankha.

Kodi asayansi amadziŵa mmene cilengedwe kuphatikizapo moyo zinayambila? Yankho lacidule n’lakuti ayi. Anthu ena amakamba kuti akatswili a sayansi ya zacilengedwe, angathe kufotokoza mmene cilengedwe cinayambila. Komabe, pulofesa wa maphunzilo a zakuthambo, dzina lake Marcelo Gleiser, wa pa Koleji ya Dartmouth, amenenso amakayikila za kukhalapo kwa Mulungu anati: “Sitinakwanitse kufotokoza mmene cilengedwe cinayambila.”

Mofananamo, pofotokoza za ciyambi ca moyo, nkhani ina m’magazini yochedwa Science News inati: “N’zovuta kudziŵa mmene moyo unayambila padziko lapansi. Zili conco cifukwa mathanthwe na zinthu zina zakale zimene zikanatithandiza kudziŵa zomwe zinacitika dziko litangokhalako kumene, zinatha kale-kale.” Mawu amenewa aonetsa kuti asayansi sanapeze yankho pa funso lakuti, Kodi cilengedwe conse kuphatikizapo moyo zinayamba bwanji?

Koma mwina mungafunse kuti, ‘Ngati zamoyo pano padziko lapansi zinacita kupangidwa, ndani anazipanga?’ Mwinanso munaganizilapo mafunso monga awa: ‘Ngati kulidi Mlengi wanzelu komanso wacikondi, n’cifukwa ciani amalola kuti anthufe tizivutika? N’cifukwa ciani amalola kuti pakhale zipembedzo zambili zosiyanasiyana? Nanga n’cifukwa ciani amalola anthu amene amati amamulambila kucita zinthu zambili zoipa?’

Sayansi singakwanitse kuyankha mafunso amenewa. Koma izi sizitanthauza kuti simungapeze mayankho okhutilitsa. Anthu ambili apeza mayankho okhutilitsa m’Baibo.

Ngati mufuna kudziŵa cifukwa cake asayansi ena amene anaphunzila Baibo amakhulupilila kuti kuli Mlengi, pitani pa jw.org. Pamenepo, fufuzani mawu akuti “ndemanga zokhudza ciyambi ca moyo.”

Sayansi na Baibo zinawathandiza kukhulupilila kuti kuli mlengi

Georgiy N. Koidan, katswili wa zamakemiko

“Nthawi zambili, nchito yanga imakhala ‘yophatikiza pamodzi’ makemiko kuti nipange mamolekyu. Umafunika kukonzekela pasadakhale zoyenela kucita. Ukangophonyetsa pamodzi, basi molekyu sipangika. Ngakhale kuti nchito yanga ni yofuna luso kwambili, ni yosavuta poyelekezela na zinthu zambili zogometsa zimene zimacitika mkati mwa maselo a zamoyo, kuti apange makemiko ocolowana. Izi zimanipangitsa kukhulupilila kuti kuli Katswili Wamkulu wa zamakemiko, amene ni Mlengi.

“Pamene n’nali kuphunzila Baibo, n’nazindikila kuti si buku wamba. Baibo inatha kulembedwa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, koma nimaona kuti malangizo ake ni othandiza kwambili ngakhale masiku ano. Zimene imakamba ponena za mmene tingathetsele mikangano m’banja, kunchito, komanso na anansi athu zimathandiza. Nimaona kuti palibe munthu angapeleke malangizo othandiza ngati amenewa, kupatulapo winawake wanzelu kwambili kuposa anthu.”

Yan-Der Hsuuw, katswili woona za mmene mwana amakulila asanabadwe

“Kuti mwana apangike m’mimba mwa mayi, maselo onse amacita zinthu mogwilizana kuti asinthe maselo ena kukhala mitsempha, minofu, mafupa, magazi, na ziwalo zina mpaka kupanga munthu. Mpaka pano sitimvetsa zimene zimacitika kuti munthu apangike. Mmene nimaonela ine, moyo unacita kupangidwa na winawake wanzelu.

“Zimene Baibo imakamba pa Salimo 139:15, 16, za mmene mwana amakulila m’mimba mwa mayi ake, n’zofanana kwambili na zimene asayansi atulukila m’zaka zaposacedwa. Popeza zimenezi zinalembedwa kale-kale, kodi wolembayo akanazidziŵa bwanji popanda kuuzidwa na Mlengi?”

Onelelani vidiyo yakuti Rocío Picado Herrero: Mphunzitsi wa Chemistry Akufotokoza za Chikhulupililo Chake. Fufuzani mutu wa vidiyoyi pa jw.org, ku Chichewa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani