Mawu Oyamba
Ulemu ni khalidwe losoŵa kwambili masiku ano, cakuti munthu akaonetsa khalidweli zimaoneka zacilendo.
Mwacitsanzo, anthu ambili salemekeza makolo awo, acikulile, apolisi, mabwana awo ku nchito, komanso aphunzitsi. Kuwonjezela apo, mawu onyoza akuculukila-culukila pa intaneti! Malinga na nkhani ina ya m’magazini yochedwa Harvard Business Review, kupanda ulemu “kukuwonjezekadi.” Magaziniyo inanenanso kuti malipoti a zocitika zoonetsa kupanda ulemu akuwonjezeka.