LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • yc phunzilo 12 masa. 26-27
  • Mwana wa Mlongo wa Paulo Anali Wolimba Mtima

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mwana wa Mlongo wa Paulo Anali Wolimba Mtima
  • Phunzitsani Ana Anu
  • Nkhani Zofanana
  • Limbani Mtima—Yehova Ndiye Mthandizi Wanu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Munthu Wopanda Mantha
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Phunzitsani Ana Anu
yc phunzilo 12 masa. 26-27
 Mwana wa mlongo wa Paulo alankhula kwa mkulu wa asilikali

PHUNZILO 12

Mwana wa Mlongo wa Paulo Anali Wolimba Mtima

Tiye tiphunzile za mnyamata amene anapulumutsa amalume ake. Amalume a mnyamatayu anali mtumwi Paulo. Dzina la mnyamata ameneyu sitilidziŵa, koma zimene tidziŵa ndi zakuti iye anacita zinthu molimba mtima. Kodi ungakonde kudziŵa zimene iye anacita?—

Paulo anali m’ndende ku Yerusalemu. Iye anaikidwa m’ndende cifukwa anali kulalikila za Yesu. Koma anthu ena oipa anadana naye Paulo, conco anakonza ciwembu. Iwo anati: ‘Tiyeni tipemphe mkulu wa asilikali kuti alamule asilikali ake kuti abweletse Paulo ku khoti. Ndiyeno ife tidzabisala panjila kuti pamene Paulo adutsa timuphe.’

Mtumwi Paulo womangidwa amvetsela uthenga kwa mwana wa mlongo wake

Mwana wa mlongo wa Paulo anauza Paulo ndi mkulu wa asilikali za ciwembu

Mwana wa mlongo wa Paulo anamva za ciwembu cimeneco. Kodi iye anacita ciani? Anapita kundende ndi kukauza Paulo za nkhani imeneyo. Nthawi imeneyo, Paulo anauza mnyamatayo kuti apite kukauza mkulu wa asilikali za ciwembu cimeneco. Kodi uganiza kuti cinali copepuka kwa mnyamatayo kuti akauze mkulu wa asilikali?— Iyai, cifukwa msilikali ameneyo anali wapamwamba kwambili. Koma mwana wa mlongo wa Paulo anali wolimba mtima, ndipo iye sanaope kuuza mkulu wa asilikali za nkhani imeneyo.

Mkulu wa asilikali anadziŵa zocita. Anatumiza asilikali pafupi-fupi 500 kuti ateteze Paulo. Iye anauza asilikaliwo kuti apelekeze Paulo ku Kaisareya usiku umenewo. Kodi Paulo anapulumuka ciwembu cimeneci?— Inde, anthu oipa amenewo analephela kumupha. Ciwembu cao sicinagwile nchito.

Kodi uphunzilapo ciani pankhani imeneyi?— Iwenso ungakhale wolimba mtima monga mwana wa mlongo wa Paulo. Pamene tiuza ena za Yehova, ifenso tiyenela kukhala olimba mtima. Kodi udzakhala wolimba mtima ndi kupitilizabe kulankhula za Yehova?— Ngati ucita zimenezo, udzapulumutsa anthu ena.

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO

  • Machitidwe 23:12-24

  • Mateyu 24:14; 28:18-20

  • 1 Timoteyo 4:16

MAFUNSO:

  • Kodi anthu oipa anapangana kuti amucite ciani Paulo?

  • Kodi mwana wa mlongo wa Paulo anacita ciani? N’cifukwa ciani kucita zimenezo kunali kulimba mtima?

  • Kodi ungakhale bwanji wolimba mtima monga mwana wa mlongo wa Paulo?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani