NYIMBO 89
Mvela Udalitsike
Yopulinta
1. Ngati timamveladi Yesu Khristu.
Tidzacita zimene anena.
Tikacita zimene tiphunzila,
Tidzakondwa tidzadalitsidwa.
(KOLASI)
Ukamvela Yehova,
Udzasangalaladi.
Ukacita zimene anena,
Udzadalitsidwadi.
2. Monga nyumba yomangidwa pathanthwe
Osati yomangidwa pamcenga.
Titsatile citsogozo ca Yesu,
Tidzalimba ndipo sitingagwe.
(KOLASI)
Ukamvela Yehova,
Udzasangalaladi.
Ukacita zimene anena,
Udzadalitsidwadi.
3. Mtengo wobyalidwa m’mbali mwa madzi
Umabala nthawi ikafika,
Tizimvela monga ana a M’lungu,
Ndipo Yehova ‘dzatidalitsa.
(KOLASI)
Ukamvela Yehova,
Udzasangalaladi.
Ukacita zimene anena,
Udzadalitsidwadi.
(Onaninso Deut. 28: 2, Sal. 1:3; Miy. 10:22; Mat. 7: 24-27; Luka 6:47-49.)