Baibulo Limasintha Anthu
Ndinamenya nkhondo yandekha kuti ndithetse kupanda cilungamo ndi nkhanza
CAKA COBADWA: 1960
DZIKO: LEBANON
MBILI YANGA: KATSWILI WOPONYA ZIBAKEL
KUKULA KWANGA:
Ndinakulila ku Rmaysh, ku malile a Israel ndi Lebanon. Nthawi imeneyi n’kuti nkhondo ya pa ciweniweni ili mkati. Ndimakumbukila bwino kuti anthu ambili osalakwa analemala cifukwa ca mabomba okwilila pansi. Moyo unali wovuta kwambili ndipo upandu ndi nkhanza zinafika pacimake.
Banja lathu linali kupemphela ku Chalichi ca Maronite, cimodzi mwa machalichi a Akatolika a ku m’maŵa. Tinali ana 12 ndipo atate anali ndi nchito yotidyetsa, pamene amai sanali kufuna ngakhale pang’ono kuti anafe tizilova ku chalichi. Patapita nthawi, ndinayamba kuona kuti chalichi mofanana ndi anthu ena onse, cinali kulephela kuthandiza anthu ovutika.
Ndili wacinyamata, ndinayamba kukonda masewela a zibakela. Ndinapita ku kosi ndipo ndinakhala ndi luso lomenya mbama ndi kuponya zibakela mwa kugwilitsila nchito njila zosiyanasiyana za makalate. Ndinali kuganiza kuti, ‘Ndingayeseko kuletsa anthu nkhanza koma osati nkhondo.’ Conco ndinali kucita kuti ndikaona anthu aŵili akumenyana, inenso ndinali kugwapo. Mwacibadwa ndinali wamtima wapacala, moti silinali vuto kukwiya msanga. Kum’mwela kwa Lebanon konse anthu anali kundiopa kwambili pamene ndinali kumenya nkhondo yanga yothetsa kupanda cilungamo ndi nkhanza.
Mu 1980, ndinakaloŵa m’kalabu ya oponya zibakela ku Beirut. Kumeneko mabomba ndi maloketi anali kungokhalila kuphulika. Ngakhale zinali conco, sindinasiye kupita ku kosi imeneyi. Ndinali kungokhalila kudya, kugona komanso kukhala ndi moyo ngati wa Bruce Lee, Mchaina wa ku America amene anali katswili pa masewela a zibakela. Ndinatengela kapesedwe kake ka tsitsi, kayendedwe kake ndi mmene anali kukuwila akamacita masewela oponya zibakela. Ndipo sindinali kumwetulila ngakhale pang’ono.
MMENE BAIBULO LINASINTHILA UMOYO WANGA:
Colinga canga cinali cakuti ndidzakhale katswili woponya zibakela ku China. Tsiku lina madzulo, ndinangomva kugogoda pacitseko apo ndili mkati kuyeselela kuponya zibakela pokonzekela ulendo wopita ku China. Mnzanga anali atabwela ndi Mboni za Yehova ziŵili. Ndili civalile zovala zanga zakuda zoseŵelela, thukuta lili kamukamu ndinauza Mbonizo kuti, “Ine Baibulo n’kumanzele.” Sindinali kudziŵa kuti nthawi imeneyo moyo wanga udzasinthilatu.
Mbonizo pogwilitsila nchito Baibulo, zinandionetsa cifukwa cake anthu sangakwanitse kuthetselatu kupanda cilungamo ndi nkhanza. Zinafotokozanso kuti Satana Mdyelekezi ndi amene amacititsa mavuto amenewo. (Chivumbulutso 12:12) Ndinacita cidwi kuona kuti Mbonizo zinalankhula ndi ine mwamtendele komanso ndi mtima wonse. Ndinakhudzidwanso kudziŵa kuti Mulungu ali ndi dzina. (Salimo 83:18) Mbonizo zinandionetsa lemba la 1 Timoteyo 4:8, limene limati: “Kucita maseŵela olimbitsa thupi ndi kopindulitsa pang’ono, koma kukhala wodzipeleka kwa Mulungu n’kopindulitsa m’zonse, cifukwa kumakhudza lonjezo la moyo uno ndi moyo umene ukubwelawo.” Mau amenewa anandikhudza kwambili.
Zinali zacisoni kuti sindinapezenso mpata woceza ndi Mboni za Yehova cifukwa a m’banja langa anauza Mbonizo kuti zisakabwelenso. Ngakhale zinali conco, ndinasankha kusiya masewela a zibakela kuti ndiyambe kuphunzila Baibulo. Koma abale anga sanasangalale ndi zimenezo. Ngakhale kuti io anatelo, ine ndinayesetsa kuti ndipezenso Mboni za Yehova kuti ziyambe kundiphunzitsa Baibulo.
Ndinapitiliza kufunafuna Mboni koma sindinazipeze. Panthawi imeneyi, ndinali wacisoni kwambili ndi kumwalila mwadzidzidzi kwa atate anga, ndiponso cifukwa ca mavuto ena apabanja lathu. Kenako ine ndinayamba kugwila nchito pa kampani ya zomangamanga. Tsiku lina Adel amene ndinali kugwila naye nchito anandiimitsa n’kundifunsa cifukwa cimene ndinali kuonekela wacisoni. Kenako, iye anayamba kundifotokozela zimene Baibulo limakamba zakuti akufa adzauka. Patapita miyezi 9, Mboni yacikondi ndi yokoma mtima imeneyi inayamba kundiphunzitsa Baibulo moleza mtima.
Phunzilo lija linapitiliza ndithu, ndipo ndinayamba kuona kuti ndifunika kusintha kwambili umunthu wanga. Zimenezi zinali zovuta. Ndinali ndi mtima wapacala. Kuphunzila Baibulo kunandithandiza kuti ndikhale wodziletsa ndi kupewa mtima wasontho. Mwacitsanzo, pa Mateyu 5:44 pali uphungu wa Yesu wonena kuti: “Pitilizani kukonda adani anu ndi kupemphelela amene akukuzunzani.” Ndipo lemba la Aroma 12:19 limaticenjeza kuti: “Musabwezele coipa, . . . pakuti malemba amati: ‘“Kubwezela ndi kwanga ndidzawabwezela ndine,’ watelo Yehova.” Malemba amenewa ndi malemba ena anandithandiza kuti pang’ono ndi pang’ono ndikhale munthu wamtendele.
MAPINDU AMENE NDAPEZA:
Ngakhale kuti poyamba banja lathu silinafune kuti ndiziphunzila ndi Mboni za Yehova, io tsopano amazilemekeza. Mmodzi wa abale anga anayamba kulambila Yehova, ndipo amai naonso mpaka nthawi imene anamwalila, anali kukamba zabwino za cipembedzo cathu akamaceza ndi ena.
Komanso Mulungu wandidalitsa ndapeza mkazi wabwino ndi wokhulupilika, dzina lake Anita. Ameneyu ndi mnzanga wapamtima amene ndimacita naye utumiki wa nthawi zonse. Kuyambila caka ca 2000 ine ndi Anita tikukhala m’mzinda wa Elkilstuna m’dziko la Sweden, kumene takhala tikuthandiza anthu olankhula Ciluya kuphunzila Baibulo.
Zimandikhudzabe ndikaona anthu akuvutika ndi nkhanza. Koma popeza kuti ndikudziŵa cifukwa cake, ndi kuti Mulungu adzathetsa nkhanza posacedwapa, mtima wanga umakhala pa mtendele ndipo ndimakondwela kwambili.—Salimo 37:29.
Ine ndi mkazi wanga timakondwela ndi utumiki. Timakonda kuphunzitsako ena za Yehova