N’cifukwa Ciani Yesu Anavutika Ndi Kutifela?
Na. 2 2016
CIKUMBUTSO CA IMFA YA YESU | PACITATU, MARCH 23, 2016
© 2016 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
MAGAZINI ya Nsanja ya Mlonda, imalemekeza Yehova Mulungu, amene ndi Wolamulila wa cilengedwe conse. Imalimbikitsa anthu ndi uthenga wabwino wakuti Ufumu wa Mulungu posacedwapa udzacotsa zoipa zonse ndi kusintha dziko lapansi kukhala paladaiso. Imalimbikitsa anthu kukhulupilila Yesu Kristu amene anatifela kuti tidzapeze moyo wosatha, ndipo panthawi ino iye akulamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Magaziniyi yakhala ikufalitsidwa kuyambila mu 1879 ndipo si yandale. Mfundo zake zonse n’zocokela m’Baibulo.
Magazini iyi si yogulitsa. Colinga cake ndi kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibulo imene imacitika padziko lonse lapansi. Zopeleka zaufulu n’zimene zimathandiza kupititsa patsogolo nchito imeneyi.
Kuti mucite copeleka, pitani pa webusati ya www.jw.org.
Baibulo limene taseŵenzetsa ndi Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika kusiyapo ngati taonetsa lina.