Kodi Baibo Ikali Yothandiza Masiku Ano?
Na. 2 2018
© 2017 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
Kodi mungakonde kudziŵa zambili kapena kuphunzila Baibo kunyumba kwanu mwaulele?
Magazini ino si yogulitsa. Colinga cake ni kuthandiza pa nchito yophunzitsa Baibo imene ikucitika padziko lonse lapansi. Zopeleka zaufulu n’zimene zimathandiza kupititsa patsogolo nchito imeneyi. Kuti mupeleke copeleka canu, yendani pa webusaiti ya www.pr2711.com. Baibo imene taseŵenzetsa ni Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika kusiyapo ngati taonetsa ina.
MAGAZINI ya Nsanja ya Mlonda, imalemekeza Yehova Mulungu, amene ni Wolamulila wa cilengedwe conse. Imalimbikitsa anthu ndi uthenga wabwino wakuti posacedwa Ufumu wa Mulungu udzacotsapo zoipa zonse, na kusintha dziko lapansi kukhala paradaiso. Imalimbikitsanso anthu kukhulupilila Yesu Khristu amene anatifela kuti tikapeze moyo wosatha. Ndipo panthawi ino, iye alamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Magazini ino yakhala ikufalitsidwa kuyambila mu 1879, ndipo siiloŵelela m’nkhani zandale. Mfundo zake zonse n’zocokela m’Baibo.