ZAMKATI
WIKI YA OCTOBER 1-7, 2018
3 Kodi Mudziŵa Bwino Zoona Zake?
WIKI YA OCTOBER 8-14, 2018
8 Musamaweluze Poona Maonekedwe Akunja
M’nkhani yoyamba, tidzakambilana zinthu zimene zingapangitse kuti cikhale covuta kudziŵa zoona zeni-zeni pa nkhani inayake imene tamva. Tidzakambilananso mfundo za m’Baibo zimene zingatithandize kukulitsa luso lopenda mosamala nkhani imene tamva kuti tidziŵe ngati ni ya zoona. M’nkhani yaciŵili, tidzakambilana zinthu zitatu zimene nthawi zambili anthu amaziona monga maziko oweluzila anzawo potengela maonekedwe akunja. Tidzakambilananso zimene zingatithandize kukulitsa mtima wopanda tsankho pocita zinthu na ena.
13 Mbili Yanga—N’natsimikiza Mtima Kuti Sinidzabwelela M’mbuyo
WIKI YA OCTOBER 15-21, 2018
18 Opatsa Mowoloŵa Manja Amakhala Acimwemwe
WIKI YA OCTOBER 22-28, 2018
23 Muziseŵenza na Yehova Tsiku Lililonse
Yehova analenga anthu kuti akhale na umoyo wabwino komanso wacimwemwe. Timakhala na umoyo wacimwemwe ngati tiseŵenza na Yehova tsiku lililonse pokwanilitsa cifunilo cake. M’nkhani ziŵili zimenezi, tidzakambilana mapindu amene timapeza tikamaonetsa kuolowa manja m’njila zosiyana-siyana.