ZA M’NKHOKWE YATHU
Kufesa Mbewu za Ufumu ku Portugal
TSIKU lina, M’bale George Young ananyamuka pa sitima ya pamadzi kucoka ku Brazil kupita ku Europe. Mkati mwa ulendowo, pamene mafunde a m’nyanja ya Atlantic anali kuwomba mwamphamvu sitimayo, m’baleyo anali kuganizila za nchito ya Ufumu imene anagwila ku Brazil.a Koma akali pa ulendowo, M’bale Young anayambanso kuganizila za ku Spain na ku Portugal kumene anatumizidwa kuti akatumikile. Ambili kumeneko anali asanamveleko coonadi. Iye anali kuganiza kuti akakafika kumeneko akapanga makonzedwe ogaŵila mathilakiti okwana 300,000, komanso makonzedwe akuti M’bale J. F. Rutherford adzakambe nkhani za Baibo.
M’bale George Young anayenda maulendo ambili a pa nyanja okalalikila
Mu 1925, M’bale Young atafika mumzinda wa Lisbon ku Portugal, anapeza kuti kuli mavuto azandale. Mu 1910, cipani cina ca ndale cinali citacotsapo ulamulilo wa mafumu, ndipo izi zinapangitsa kuti Chechi ya Katolika isakhalenso na mphamvu zoculuka m’dzikolo. Anthu anakhala na ufulu woculukilapo, koma mavuto azandale anapitilizabe m’dzikolo.
Pamene M’bale Young anali kupanga makonzedwe akuti M’bale Rutherford abwele kudzakamba nkhani, boma linakhazikitsa malamulo okhwima cifukwa anthu ena anafuna kulanda bomalo. Mlembi wa bungwe linalake lofalitsa ma Baibo (British and Foreign Bible Society) anacenjeza M’bale Young kuti adzakumana na citsutso cacikulu. Ngakhale zinali conco, iye anakapempha cilolezo ku boma kuti akaseŵenzetse holo ya zamaseŵela ya pa sukulu ya sekondale yochedwa Camões. Ndipo boma linavomeleza.
Tsiku lakuti M’bale Rutherford akambe nkhani yake linafika. Panali pa May 13. Anthu anali kuyembekezela mwacidwi kumvetsela nkhaniyo. Kunali vimapepa vomatika ku zipupa, komanso nkhani za m’manyuzipepa zolengeza nkhani ya anthu onse yakuti, “Zimene Mungacite Kuti Mukhale na Moyo pa Dziko Kwamuyaya.” Mwamsanga anthu acipembedzo otsutsa anafalitsa nkhani yocenjeza anthu awo za ise m’nyuzipepa yawo. Anali kukamba kuti kwabwela “aneneli onama.” Otsutsawo anakhala pa khomo loloŵela m’holoyo na kugaŵila tumabuku masauzande ambili tokamba mfundo zotsutsa nkhani ya M’bale Rutherford.
Olo zinali conco, anthu 2,000 analoŵa m’holoyo, ndipo enanso pafupi-fupi 2,000 anawabweza cifukwa ca kucepa kwa malo. Omvetsela ena acidwi anacita kukhala pa makwelelo a m’mbali mwa holoyo. Ena anakhala pamwamba pa zipangizo zocitila maseŵela olimbitsa thupi.
Koma panali zovuta zina. Otsutsa anali kukuwa na kuthyola mipando. Ngakhale zinali conco, M’bale Rutherford anakhalabe wodekha, ndipo anakwela pa thebulo kuti mau ake azimveka bwino kwa onse. Iye anatsiliza kukamba nkhaniyo ca pakati pa usiku, ndipo anthu acidwi oposa 1,200 analembetsa maina awo na kusiya ma adresi awo kuti azilandila mabuku ophunzilila Baibo. Tsiku lotsatila, nyuzipepa ya O Século inafalitsa zokhudza nkhani imene M’bale Rutherford anakamba.
Pofika mu September 1925, magazini ya Nsanja ya Mlonda inayamba kufalitsidwa m’Cipwitikizi ku Portugal (m’mbuyomo, magazini ya Cipwitikizi ya Nsanja inali itayamba kale kufalitsidwa ku Brazil.) Ca pa nthawi imeneyi, Wophunzila Baibo wina, dzina lake Virgílio Ferguson anapanga makonzedwe osamukila ku Portugal kuti akacilikize nchito ya Ufumu kumeneko. M’mbuyomo, iye anali atatumikilako na M’bale Young pa nthambi yaing’ono ya Ophunzila Baibo ku Brazil. Patapita nthawi yocepa, m’bale Ferguson ananyamuka na mkazi wake, Lizzie, kupita ku Portugal kumene kunali M’bale Young. Kubwela kwa M’bale Ferguson kunali kwa pa nthawi yake, cifukwa M’bale Young anali atatsala pang’ono kutumizidwa kuti akagwile nchito yolalikila ku maiko ena, kuphatikizapo ku Soviet Union.
Cilolezo coseŵenzetsa nyumba cimene M’bale Virgílio na mlongo Lizzie Ferguson, analandila mu 1928
Asilikali atalanda boma na kukhazikitsa ulamulilo wopondeleza ku Portugal, citsutso cinakula m’dzikolo. M’bale Ferguson sanacoke m’dzikolo. Ndipo anayesetsa kuteteza kagulu kocepa ka Ophunzila Baibo na kuwalimbikitsa kuwonjezela zocita mu utumiki wawo. Iye anapita kukapempha cilolezo ku boma kuti aziseŵenzetsa nyumba yake monga malo ocitilamo misonkhano. Mu October 1927, anapatsidwa cilolezoco.
M’caka coyamba ca ulamulilo wopondeleza umenewo, anthu pafupi-fupi 450 ku Portugal analembetsa kuti azilandila magazini ya Nsanja ya Mlonda. Kuwonjezela apo, cifukwa ca nchito yogaŵila mathilakiti na tumabuku, coonadi cinafalikila ku maiko na madela akutali amene anali kulamulidwa na Portugal, monga ku Angola, Azores, Cape Verde, East Timor, Goa, Madeira, na Mozambique.
Cakumapeto kwa m’ma 1920, mlimi wina wa ku Portugal dzina lake Manuel da Silva Jordão, amene anali kukhala ku Brazil, anabwela kudzakhala mu mzinda wa Lisbon. Pamene anali ku Brazil, iye anamvetselako nkhani yokambiwa na M’bale Young. Pa nthawiyo, Silva Jordão anazindikila kuti zimene anamva cinali coonadi, ndipo anali wofunitsitsa kuthandiza M’bale Ferguson kupititsa patsogolo nchito yolalikila. Conco, m’bale Manuel anayamba kutumikila monga kopotala, dzina la apainiya pa nthawiyo. Popeza nchito yopulinta na kufalitsa mabuku ophunzilila Baibo inayamba kuyenda bwino, mpingo wa ku Lisbon umene unali utangokhazikitsidwa kumene, unakula.
Mu 1934, M’bale na Mlongo Ferguson anabwelela ku Brazil. Komabe, mbeu za coonadi zimene anabyala ku Portugal zinali zitamela. M’nthawi ya mavuto aakulu ku Europe, monga m’nthawi ya nkhondo ya paciweniweni ku Spain, komanso Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse, kagulu kocepa ka abale amene anali ku Portugal kanakhalabe kokhulupilika. Kwa kanthawi, iwo anali cabe monga mbaula yofuka utsi. Koma mu 1947 cangu cawo cinayambanso kuyaka monga moto, pamene mmishonale woyamba, John Cooke, anafika. Kucokela nthawiyo, ciŵelengelo ca ofalitsa uthenga wa Ufumu cinapitilizabe kuwonjezeka. Ngakhale pamene boma linatseka cipembedzo ca Mboni za Yehova mu 1962, ciŵelengeloco cinapitilizabe kukwela. Mu December 1974, pamene Mboni za Yehova zinalandila ufulu wa kulambila, m’dzikolo munali ofalitsa oposa 13,000.
Masiku ano, ofalitsa Ufumu oposa 50,000 amalalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ku Portugal, komanso ku zisumbu zina kumene cipwitikizi cimakambidwa, monga ku Azores na ku Madeira. Pa ofalitsa amenewa, ena ni adzukulu a anthu amene anapezekapo pa nkhani yokhudza mtima imene M’bale Rutherford anakamba mu 1925.
Timam’yamikila kwambili Yehova, kuphatikizapo abale na alongo okhulupilika amene anatumikila molimba mtima ndi modzipeleka popititsa patsogolo nchito ya Ufumu, monga ‘anchito a Khristu Yesu, otumikila anthu a mitundu ina.’—Aroma 15:15, 16.—Za m’nkhokwe yathu ku Portugal.
a Onani nkhani yakuti “Ntchito Yokolola Idakalipo Yambiri” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2014, mape. 31-32.