LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w18 November tsa. 32
  • Ni Mphatso Yanji Imene Tingam’patse Yehova?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ni Mphatso Yanji Imene Tingam’patse Yehova?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • Nkhani Zofanana
  • “Okonzeka Kupeleka Mphatso kwa Yehova”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
  • Mphamvu ya ‘Tumakobili Tuŵili Twatung’ono’
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2020
  • Timayamika Yehova Cifukwa ca Cikondi Canu
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2021
  • ‘Muziika Kenakake Pambali’
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
w18 November tsa. 32
donate.jw.org

Ni Mphatso Yanji Imene Tingam’patse Yehova?

PA NTHAWI ina Yesu anati: “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Mac. 20:35) Mfundo imeneyi imagwilanso nchito pa ubwenzi wathu na Yehova. N’cifukwa ciani takamba conco? Yehova amatipatsa mphatso zambili zimene zimatipangitsa kukhala acimwemwe. Koma tingakhale na cimwemwe coculuka ngati na ise timam’patsako mphatso Yehova. Kodi ni mphatso yanji imene tingam’patse? Miyambo 3:9 imati: “Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.” ‘Zinthu zathu zamtengo wapatali’ ziphatikizapo, nthawi yathu, maluso, mphamvu, na cuma cathu. Ngati tiseŵenzetsa zinthu zimenezi popititsa patsogolo kulambila koona, ndiye kuti tikum’patsa mphatso Yehova. Ndipo kucita zimenezi, kumatibweletsela cimwemwe coculuka.

Kodi n’ciani cingatithandize kuti tisamanyalanyaze kupeleka cuma cathu monga mphatso kwa Yehova? Mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Korinto kuti “aziika kenakake pambali” monga copeleka. (1 Akor. 16:2) Kodi mungacite ciani ngati mufuna kudziŵa njila zocitila copeleka zimene zilipo ku dela lanu? Onani pansipa.

M’maiko ena, n’zosatheka kutumiza zopeleka kupitila pa Intaneti. Koma kuti mudziŵe njila zina zotumizila zopeleka, onani pa peji ya pa jw.org yotumizila zopeleka. M’maiko ena, pa peji imeneyi pali nkhani imene ili na mayankho pa mafunso amene anthu amakhala nawo pa nkhani ya zopeleka.

Njila Yosavuta Yotumizila Copeleka Canu pa Intaneti:

YOSAVUTA KUPEZA

  • Web browser

    Lembani mawu akuti donate.jw.org pa malo olembela adresi ya webusaiti

  • JW Library

    Pa peji yoyamba ya JW Library®, tinikani pa link yakuti “Donations”

YOSAVUTA KUSEŴENZETSA

Citani copeleka ca ulendo umodzi, kapena konzani zakuti muzicita copeleka ca nthawi zonse cothandiza pa:

  • Nchito ya pa Dziko Lonse

  • Mpingo Wanu

  • Msonkhano Wacigawo

  • Msonkhano Wadela

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani