Zocitika Zokhudza Ulaliki
Tinacita bwino kwambili m’caka ca 2012. M’mwezi wa April tinafika ciŵelengelo capamwamba ca ofalitsa okwanila 161,573. Ndipo n’zosangalatsa kudziŵa kuti m’mwezi wa March tinatsogoza maphunzilo okwanila 345,441. Tiyeni ticite zonse zimene tingathe kuiitanila anthu kudzalambila nafe ku Nyumba ya Ufumu ndi kuti aziyanjana ndi anthu a Mulungu. Tikukuyamikilani cifukwa cogwila nchito yolalikila mwakhama.