Zocitika Zokhudza Ulaliki
Ndife okondwa kwambili kudziŵa kuti apainiya apadela anacitila lipoti maulendo obwelelako pafupi-fupi 90 mwezi uliwonse. Atumiki akhama amenewa amatsogoza maphunzilo a Baibo ambili ndipo amapeleka cithandizo ku mipingo yosoŵa maka-maka imene ili kumidzi. Ndipo apainiya a nthawi zonse okwana 12,700, naonso adzipeleka kuti acite zambili potumikila Yehova. Conco, tiyeni tonse tiziwayamikila ndi kuwacilikiza apainiya amenewa.—km 11/10 tsa. 4.