Musatsale M’mbuyo
Woyang’anila dela amene atumikila ku Copperbelt anapeleka lipoti lakuti: “Kuyambila mwezi wa September 2012 colinga canga cinali kuthandiza mipingo m’dela kuti itsegulitse maakaunti pa webusaiti ya jw.org. Zotsatilapo zakhala zosangalatsa. M’dela limeneli muli mipingo 21 ndipo tsopano 18 mwa mipingoyo ikugwilitsila nchito webusaiti ya jw.org potumiza malipoti ndi kuitanitsa zofalitsa. Ngakhale mipingo imene ili kumidzi yatsegulitsa kale maakaunti yao. Ndayesetsa kuthandiza abale kuti nthawi zonse azigwilitsila nchito jw.org potumiza malipoti a mpingo a utumiki wakumunda a mwezi uliwonse. Ndine wotsimikiza kuti miyezi 6 imene ikubwela malipoti a mipingo yonse sadzayamba kusoŵa. Zikomo kwambili kaamba ka makonzedwe amenewa, Yehova apitilize kudalitsa khama lanu.” ‘Musatsale m’mbuyo’ igwilitsileni nchito webusaiti yathu.