‘Sonkhanitsani Anthu’
1. Kodi pali kufanana kotani pakati pa kusonkhana kumene Aisiraeli anacita atangotuluka mu Iguputo ndi misonkhano ya cigawo ndi ya maiko?
1 Aisiraeli atangotuluka mu Iguputo, Yehova anauza Mose kuti ‘asonkhanitse anthu’ pa phili la Sinai kuti amvele mau Ake, aphunzile kumuopa ndi kutinso aphunzitse ana ao njila Zake. (Deut. 4:10-13) Cimeneci ciyenela kuti cinali cocitika cosaiŵalika ndi colimbitsa cikhulupililo. Pa miyezi imene ikubwela, anthu a Yehova adzasonkhana pa msonkhano wa cigawo ndi wa maiko kuti adzaphunzitsidwe ndi Yehova. Ndiyeno tingatani kuti tikapindule mokwanila?
2. Tingacite ciani kuti tikonzekele msonkhano wathu?
2 “Khalani Wokonzeka”: Yehova analamula Aisiraeli kuti ‘akonzekele’ msonkhano wofunika wa pa phili la Sinai. (Eks. 19:10, 11) Mofananamo, aliyense amene adzapezeka pa misonkhanoyi kaya adzakhala m’pulogalamu kapena ayi, afunika kukonzekela bwino. Mwacitsanzo, ambili angafunike kutenga chuti ku nchito kwao. Mwina mkhalidwe wanu ndi wofanana ndi wa Nehemiya. Iye anafuna kusiya nchito yake monga wopelekela cikho wa mfumu Aritasasita, koma anadziŵa kuti mfumu sidzagwilizana nazo. Conco Nehemiya anapemphela kwa Mulungu ndiyeno molimba mtima ndiponso mosamala ananena pempho lakelo kwa Mfumu. Zotsatilapo zake, Mfumu inamulola kupita ndipo inapeleka thandizo pa nchito yomanga imeneyo. (Neh. 2:1-9) Kuonjezela pa kupempha chuti kwa abwana anu, mufunikanso kutsimikizila za makonzedwe a kayendedwe ndi malo ogona. Akulu adzasangalala kuthandiza amene adzafunika thandizo. Konzekelani kudzafika mofulumila pa cigawo ciliconse, ndipo mudzakhale ‘okonzeka kuganizila mozama kuposa nthawi zonse’ ku zinthu zimene mudzamva.—Aheb. 2:1.
3. N’ciani cingatithandize pokonzenkeletsa mtima wathu msonkhano usanacitike?
3 Mbali inanso yofunika kwambili pokonzekela ikuphatikizapo kukonzekeletsa mtima wathu ndi colinga cakuti tikamvetsele ndi kuphunzila. (Ezara 7:10) Pulogalamu ya msonkhano idzaikidwa pa Webusaiti ya jw.org kukali nthawi. Pulogalamu imeneyi idzaonetsa mitu ya nkhani zonse zimene zidzakambidwa pamodzi ndi lemba limodzi kapena aŵili oonetsa mfundo yaikulu. Zimenezi ndi mfundo zabwino kwambili zimene tingagwilitsile nchito pa kulambila kwathu kwa pabanja pa milungu imene tikuyembekezela msonkhano wathu. Ofalitsa ena amasindikiza pulogalamu ndi kukaigwilitsila nchito polemba manotsi pa msonkhano.
4. Kodi makolo angagwilitsile nchito bwanji mfundo za pa msonkhano pophunzitsa ana ao?
4 ‘Phunzitsani Ana Anu’: Colinga cimodzi ca msonkhano wa pa phili la Sinai cinali “kuphunzitsa ana ao.” (Deut. 4:10) Msonkhano umapatsa makolo mwai wabwino kwambili wocita cimodzimodzi. Makolo afunika kukhala pamodzi ndi ana ao pa pulogalamu yonse ndi kuwathandiza kuti azimvetsela. Mabanja angakambilane pulogalamu pa kutha kwa tsiku lililonse kapena pa nthawi ya kulambila kwao kwa pabanja.
5. Kodi tidzapindula motani tikadzapezeka pa msonkhano wa cigawo umene ukubwela?
5 Msonkhano wosaiŵalika wa pa Phili la Sinai unathandiza Aisiraeli kuyamikila mwai wao wapadela wokhala anthu a Mulungu. (Deut. 4:7, 8) Mofananamo, msonkhano umene ukubwela wakonzedwa n’colinga cimeneco. Kwa masiku atatu tidzacoka m’cipululu coipa ca dziko la Satana, ndipo tidzatsitsimulidwa mwa kuuzimu ndi maceza olimbikitsa mu paladaiso wathu wa kuuzimu. (Yes. 35:7-9) Tiyeni tisanyalanyaze mwai wosonkhana pamodzi kuti tilimbikitsane pamene tsiku la Yehova likuyandikila!—Aheb. 10:24, 25.