Zilengezo
◼ Cogaŵila ca mu July: Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu. August: Nchito yapadela yogaŵila kapepala kauthenga katsopano kotsatsa Webu saiti ya jw.org. September ndi October: Magazini ya Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani!
◼ Kuyambila ndi magazini ya November 2014, Nsanja ya Mlonda yophatikizidwa izipezeka m’cinenelo ca Cimambwe-Lungu. Mipingo ingayambe kuitanitsa magaziniwa. Mwezi uno tidzakhala ndi Nsanja ya Mlonda yophunzila yoyamba ya mu Cinyanja.