Zilengezo
◼ December: Gaŵilani buku la mutu wakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni kapena gaŵilani kalikonse ka tumapepala twauthenga utu: Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?, Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?, Kodi Cofunika N’ciani Kuti Banja Likhale Lamtendele?, Kodi Ndani Maka-maka Amene Akulamulila Dzikoli?, Kodi Mavuto Adzathadi?, ndi kakuti Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo? January ndi February: Gaŵilani kabuku kakuti, Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu. March: Gaŵilani magazini a Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani!
◼ Cikumbutso ca mu 2016 cidzacitika pa Citatu pa March 23, 2016.
◼ Kuyambila pa January 1, 2015, makonzedwe akuti mipingo iziyambitsa maphunzilo a Baibulo pa Ciŵelu coyamba ca mwezi adzatha. M’malomwake, ofalitsa adzayamba kugaŵila magazini monga mmene timacitila pa Ciŵelu ciliconse. Tingayambitse maphunzilo a Baibulo nthawi iliyonse m’mweziwo pogwilitsila nchito magazini kapena mabuku ena ogwilitsila nchito pophunzila.
◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:
Vidiyo yakuti Jehovahs Witnesses Organised to share the good news ndi yakuti Our Whole Association Of Brothers—Cimambwe-Lungu.
Buku Lapacaka la Mboni za Yehova la 2015—Cikikaonde