Zilengezo
◼ Zogaŵila mu September ndi October: Magazini a Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani! November ndi December: Buku lakuti, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni kapena kamodzi mwa tumapepala twa uthenga utu: Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?, Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?, Kodi Cofunika N’ciani Kuti Banja Likhale Lamtendele?, Kodi Ndani Maka-maka Amene Akulamulila Dzikoli?, Kodi Mavuto Adzathadi?, ndi Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?
◼ Nkhani yapadela pambuyo pa Cikumbutso ca 2016 idzakambidwa mlungu wa March 28. Mutu wa nkhani imeneyi tidzauzidwa mtsogolo. Mipingo imene idzakhala ndi woyang’anila dela kapena msonkhano wadela mlungu umenewo idzakhala ndi nkhaniyi mlungu wotsatila. Palibe mpingo umene uyenela kukhala ndi nkhani imeneyi mlungu wa March 28 usanafike.
◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:
Tumapepala twa Uthenga: Kodi Baibo Mumaiona Bwanji?, Kodi Zinthu Zidzakhala Bwanji Mtsogolo?, Kodi Cofunika N’ciani Kuti Banja Likhale Lamtendele?, Kodi Ndani Maka-maka Amene Akulamulila Dzikoli?, Kodi Mavuto Adzathadi?, Kodi N’zoona Kuti Akufa Angakhalenso ndi Moyo?, Kodi Ufumu wa Mulungu ndi Ciani?, Tingapeze Kuti Mayankho a Mafunso Ofunika Kwambili Onena za Umoyo?—Mungatumvetsele pa Webusaiti yathu ndi pa ma CD—m’Cilala ndi m’Cinenelo ca Manja ca mu Zambia
Tumabuku: N’zotheka Banja Lanu Kukhala la Cimwemwe ndi Phunzitsani Ana Anu—m’Cilenje. Tukupezekanso pa jw.org.