Zilengezo
◼ Zogaŵila mu October: Magazini a Nsanja ya Mlonda ndi Galamukani! November ndi December: Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni kapena kamodzi mwa tumapepala twauthenga utu: Kodi Baibo mumaiona bwanji?, Kodi zinthu zidzakhala bwanji mtsogolo?, Kodi cofunika n’ciani kuti banja likhale lamtendele?, Kodi ndani maka-maka amene akulamulila dzikoli?, Kodi mavuto adzathadi?, ndi Kodi n’zoona kuti akufa angakhalenso ndi moyo? January: Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu.
◼ Nsanja ya Mlonda yophunzila ya zilembo zazikulu ikupezeka m’Cinyanja (lp-CIN). Mungaode magazini amenewa kupitila pa JW.ORG.