LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb16 March tsa. 7
  • Ciukililo Cidzatheka Kupitila mu Nsembe ya Dipo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Ciukililo Cidzatheka Kupitila mu Nsembe ya Dipo
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Nkhani Zofanana
  • Ciyembekezo Cotsimikizilika Cakuti Okondedwa Athu Amene Anamwalila Adzauka
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • N’zotheka Okondedwa Anu Kudzakhalanso na Moyo!
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • “Ine Ndili Ndi Ciyembekezo mwa Mulungu”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Akufa Adzauka Ndithu—Sitikaika Konse!
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
mwb16 March tsa. 7

UMOYO WATHU WACIKRISTU

Ciukililo Cidzatheka Kupitila mu Nsembe ya Dipo

Acibale ndi mabwenzi akulila cifukwa ca imfa ya wokondedwa wao

Cikumbutso cimatipatsa mwai woganizila madalitso a mtsogolo amene adzatheka cifukwa ca nsembe ya dipo, monga ciukililo. Yehova sanafune kuti anthu azifa. N’cifukwa cake anthu amavutika ndi cisoni munthu amene amamukonda akamwalila. (1 Akor. 15:26) Yesu anamva cisoni ataona kuti ophunzila ake akulila cifukwa ca imfa ya Lazaro. (Yoh. 11:33-35) Popeza kuti Yesu ndi cifanizilo ca Atate wake, tingakhale otsimikiza kuti nayenso Yehova cimamuŵaŵa akaona kuti tikuvutika ndi cisoni kaamba ka imfa ya munthu amene timakonda. (Yoh. 14:7) Yehova amalakalaka nthawi imene adzaukitsa atumiki ake okhulupilika. Nafenso timalakalaka zimenezo.—Yobu 14:14, 15.

Popeza kuti Yehova ndi Mulungu wadongosolo, m’pomveka kukhulupilila kuti ciukililo cidzacitika mwadongosolo. (1 Akor. 14:33, 40) M’malo moika malilo, tizikalandila anthu amene adzaukitsidwa. Kodi mumaganizila mozama pa ciukililo, makamaka pa nthawi imene muli ndi cisoni? (2 Akor. 4:17, 18) Kodi mumayamikila Yehova kaamba kotipatsa nsembe ya dipo, ndi kutifotokozela m’Malemba kuti akufa adzakhalanso ndi moyo?—Akol. 3:15.

  • Ndi anzanu komanso acibale anu ati amene mufunitsitsa kudzawaonanso?

  • Ndi anthu ati ochulidwa m’Baibulo amene mufunitsitsa kudzaceza nao?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani