CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | SALIMO 11-18
Ndani Amene Angakhale Mlendo m’Cihema ca Yehova?
Kuti munthu akhale mlendo m’cihema ca Yehova afunika kukhala bwenzi la Mulungu, kumukhulupilila ndi kumumvela. Lemba la Salimo 15 limafotokoza zimene Yehova amafuna mwa bwenzi lake.
MLENDO WA YEHOVA AYENELA . . .
kukhala wokhulupilika
kulankhula zoona mumtima mwake
kulemekeza atumiki a Yehova
kusunga mau ake zivute zitani
kuthandiza osoŵa popanda kuyembekezela kuti naonso adzamuthandiza
MLENDO WA YEHOVA AMAPEWA . . .
misece ndi kunama
kucitila mnzake zoipa
kudyela masuku pamutu Akristu anzake
kugwilizana ndi anthu amene satumikila Yehova
kulandila ciphuphu