January 9-15
YESAYA 29-33
Nyimbo 123 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Mfumu Idzalamulila Mwacilungamo”: (10 min.)
Yes. 32:1—Mfumu imene idzalamulila mwacilungamo ni Yesu Khiristu (w14 2/01 peji 11 pala. 13; ip-1 peji 329 pala. 3)
Yes. 32:2—Yesu, amene ni mfumu, waika akalonga osamalila gulu la nkhosa (w16.5 peji 25 pala. 9; w14 2/01 peji 12 pala. 17; ip-1 peji 330-334 pala. 5-9)
Yes. 32:3, 4—Anthu a Yehova amalandila maphunzilo na malangizo amene amawathandiza kucita zinthu mwacilungamo (ip-1 peji 334-335 pala. 10-11)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yes. 30:21—Ni njila ziti zimene Yehova amaseŵenzetsa popeleka malangizo kwa atumiki ake? (w14 8/15 peji 21 pala. 2)
Yes. 33:22—Ni motani, ndipo ni liti pamene Yehova anakhala Woweluza, Wopatsa Malamulo, komanso Mfumu ya Aisiraeli? (w14 10/15 peji 14 pala. 4)
Kodi ine pacanga, kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno zimene ine pacanga ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. kapena zocepelapo) Yes. 30:22-33
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 min. kapena zocepelapo) wp17.1 nkhani ya pacikuto—Kuyankha mwininyumba waukali.
Ulendo Wobwelelako: (4 min. kapena zocepelapo) wp17.1 nkhani ya pacikuto—Ŵelengelani malemba pa tabuleti kapena pa foni.
Phunzilo la Baibo: (6 min. kapena zocepelapo) lv peji 31-32 pala. 12-13—Onetsani mmene tingam’fikile pamtima.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
“Malo Obisalilapo Mphepo” (Yes. 32:2): (9 min.) Tambitsani vidiyo (Yendani ku mavidiyo pa MISONKHANO NA UTUMIKI WATHU).
“Muzimvetsela mwachelu pa Misonkhano”: (6 min.) Tambitsani vidiyo Muzimvetsela mwachelu pa Misonkhano (Yendani ku mavidiyo pa MISONKHANO NA UTUMIKI WATHU). Pambuyo pake, itanilani ana angapo ku pulatifomu na kuwafunsa kuti: N’ciani cingakulepheletseni kumvetsela pa misonkhano? N’ciani cikanacitika ngati Nowa sanamvetsele pamene Yehova anali kumuuza momangila cingalawa? N’cifukwa ciani ana onse afunika kumvetsela mwachelu pa misonkhano?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 6 pala. 16-24, bokosi lobwelelamo papeji 67
Kubwelelamo ndi Kuchulako za Mlungu Wotsatila (3 min.)
Nyimbo 40 na Pemphelo