June 5-11
YEREMIYA 51-52
Nyimbo 37 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Mau Onse a Yehova Amakwanilitsika”: (10 min.)
Yer. 51:11, 28—Yehova anakambilatu amene adzagonjetsa Babulo (it-2 peji 360 mapa. 2-3)
Yer. 51:30—Yehova anakambilatu kuti Babulo sadzadziteteza pogonjetsedwa (it-2 peji 459 pala. 4)
Yer. 51:37, 62—Yehova anakambilatu za kuwonongeka kothelatu kwa Babulo (it-1 peji 237 pala. 1)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Yer. 51:25—N’cifukwa ciani Babulo amamucha kuti “phili lowononga”? (it-2 peji 444 pala. 9)
Yer. 51:42—Kodi mau akuti “Nyanja yasefukila ndi kumiza Babulo” atanthauza ciani? (it-2 peji 882 pala. 3)
Kodi imwe pacanu kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Yer. 51:1-11
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (15 min.) Kukambilana “Maulaliki a Citsanzo.” Tambitsani vidiyo imodzi-imodzi ndipo kambilanani zimene mwaphunzilapo. Limbikitsani ofalitsa kuonetsa mwininyumba zili pa jw.org ku Chichewa polemba kuti ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA > MALANGIZO OTHANDIZA BANJA LONSE.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kodi Cikhulupililo Canu m’Malonjezo a Yehova N’colimba Bwanji?”: (15 min.) Mafunso na mayankho. Limbikitsani onse kuti nthawi ndi nthawi azikambilana maulosi a m’Baibo na okhulupilila anzawo n’colinga colimbikitsana cikhulupililo.—Aroma 1:11, 12.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 13 mapa. 24-32
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 49 na Pemphelo