LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb17 June tsa. 7
  • Muzitsatila Miyezo ya Yehova ya Makhalidwe Abwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muzitsatila Miyezo ya Yehova ya Makhalidwe Abwino
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Nkhani Zofanana
  • Cifukwa Cake Tiyenela Kusamala na Mavalidwe Komanso Maonekedwe Athu
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Mavalidwe Anu Amalemekeza Mulungu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Kodi Muli na Mtima wa Mnofu?
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Kodi Inu Mudzatsatila Malangizo a Ndani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila) —2024
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
mwb17 June tsa. 7

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Muzitsatila Miyezo ya Yehova ya Makhalidwe Abwino

Yehova Mulungu Anaika miyezo ya makhalidwe abwino. Mwacitsanzo, anaika lamulo lakuti cikwati ni m’gwilizano wokhalitsa wa pakati pa mwamuna na mkazi. (Mat. 19:4-6, 9) Iye amadana na ciwelewele ca mtundu uliwonse. (1 Akor. 6:9, 10) Anaika mfundo zokhudza mavalidwe na kudzikonza zimene zimasiyanitsa anthu ake.—Deut. 22:5; 1 Tim. 2:9, 10.

Masiku ano, anthu ambili amakana kutsatila miyezo ya Yehova. (Aroma 1:18-32) Iwo amayendela maganizo a anthu pa nkhani ya mavalidwe, kudzikonza na makhalidwe. Ambili amanyadila makhalidwe awo oipa, ndipo amasuliza anthu amene amayendela mfundo zosiyanako na zawo.—1 Pet. 4:3, 4.

Monga Mboni za Yehova, tifunika kutsatila mfundo za makhalidwe abwino a Mulungu molimba mtima. (Aroma 12:9) Motani? Tiyenela kuuza ena mwanzelu cimene cili covomelezeka kwa iye. Kuonjezela apo, tiyenela kutsatilabe miyezo yake ya makhalidwe abwino mu umoyo wathu. Mwacitsanzo, posankha zovala ndi kudzikonza tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi zosankha zanga zimaonetsa kuti nimatsatila miyezo ya Yehova kapena ya dziko?’ Nanga mavalidwe na kudzikonza kwanga zimaonetsa kuti ndine Mkhristu woopa Mulungu? Posankha pulogilamu ina yake kapena filimu yotamba, tingadzifunse kuti: ‘Kodi Yehova amavomeleza pulogilamuyi? Nanga ilimbikitsa mfundo za makhalidwe andani? Kodi zosangulutsa zimene nimakonda zinganisonkhezele kucita zoipa? (Sal. 101:3) Kodi zingakhumudwitse a m’banja langa ndi anzanga?’—1 Akor. 10:31-33.

N’cifukwa ciani mpofunika kwambili kuti tizitsatila miyezo ya Yehova ya makhalidwe abwino? Posacedwapa Khristu Yesu adzawononga mitundu ya anthu na kuipa konse. (Ezek. 9:4-7) Amene akucita cifunilo ca Mulungu ni okhawo amene adzakhalapo. (1 Yoh. 2:15-17) Conco, tiyeni tipitilize kutsatila miyezo ya Yehova ya makhalidwe abwino kuti anthu amene akucitila umboni za makhalidwe athu abwino atamande Mulungu.—1 Pet. 2:11, 12.

Mzimayi asankha zovala

Kodi mavalidwe na kudzikonza kwanga zimaonetsa kuti nimayendela miyezo yabwanji?

TAMBANI VIDIYO YAKUTI KHALA BWENZI LA YEHOVA—MWAMUNA M’MODZI, MKAZI M’MODZI, NDIYENO KAMBILANANI MAFUNSO AYA:

  • N’cifukwa ciani n’cinthu ca nzelu kutsatila miyezo ya Yehova?

  • N’cifukwa ciani makolo ayenela kuyamba kuphunzitsa ana awo mfundo za makhalidwe abwino akali aang’ono?

  • Kodi acicepele ndi acikulile omwe angathandize bwanji anthu kupindula na ubwino wa Mulungu?

MUNGAKAMBE CIANI NGATI WINA WAKUUZANI KUTI . . .

  • “Mumaona bwanji nkhani ya kugonana kwa amuna kapena akazi okha-okha?”

  • “Zimene Baibo imakamba pa nkhani za anthu ogonana ndi amuna kapena akazi anzawo n’zacikale!”

  • “Anthu amene amagonana ndi amuna kapena akazi anzawo sangasinthe khalidwe lawo cifukwa ni mmene anabadwila.”

(yp1 mutu 23; yp2 mutu 28)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani