August 28–September 3
EZEKIELI 39-41
Nyimbo 107 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 mineti kapena kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Mmene Masomphenya a Ezekieli a Kacisi Amakukhudzilani”: (10 min.)
Ezek. 40:2—Kulambila Yehova n’kokwezeka kwambili kuposa kulambila kwina kulikonse (w99 3/1 peji 11 pala. 16)
Ezek. 40:3, 5—Mosakaikila, Yehova adzakwanilitsa cifunilo cake cokhudza kulambila koyela (w07 8/1 peji 10 pala. 2)
Ezek. 40:10, 14, 16—Tifunika kutsatila miyezo ya Yehova yapamwamba ndi yolungama kuti kulambila kwathu kukhale kovomelezeka (w07 8/1 peji 11 pala. 4)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Ezek. 39:7—N’cifukwa ciani tingati anthu akamaimba Mulungu mlandu cifukwa ca zopanda cilungamo zimene zicitika, ndiye kuti akudetsa dzina lake? (w12 9/1 peji 21 pala. 2)
Ezek. 39:9—Pambuyo pa Aramagedo, n’ciani cidzacitikila zida zomenyela nkhondo zimene anthu adzasiya? (w89 8/15 peji 14 pala. 20)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 mineti kapena kucepelapo) Ezek. 40:32-47
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 mineti kapena kucepelapo) fg phunzilo 1 pala. 1—Chulani za vidiyo yakuti Kodi Mungakonde Kumvelako Uthenga Wabwino? (koma musawatambitse) na kugaŵila kabuku.
Ulendo Wobwelelako: (4 mineti kapena kucepelapo) fg phunzilo 1 pala. 2—Yalani maziko a ulendo wotsatila.
Phunzilo la Baibo: (6 mineti kapena kucepelapo) fg phunzilo 1 mapa. 3-4
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Ni Liti Pamene Ningadzacitekonso Upainiya Wothandiza?”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyo yakuti Cifukwa ca Thandizo la Yehova Ningakwanitse Kucita Ciliconse.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 17 mapa. 1-9
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 92 na Pemphelo