December 4-10
ZEFANIYA 1–HAGAI 2
Nyimbo 27 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Funani Yehova Tsiku la Mkwiyo Wake Lisanafike”: (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Zefaniya.]
Zef. 2:2, 3—Funani Yehova, funani cilungamo, funani cifatso (w01 2/15 peji 18-19 mapa. 5-7)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Hagai.]
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Zef. 1:8—Kodi pavesili tipezapo cenjezo lanji? (w07 11/15 peji 11 pala. 3)
Hag. 2:9—Kodi ulemelelo wa kacisi wa Zerubabele unaposa bwanji uja wa kacisi wa Solomo? (w07 12/1 peji 9 pala. 3)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Hag. 2:1-14
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (15 min.) Kukambilana “Maulaliki a Citsanzo.” Tambitsani na kukambilana mavidiyowo payokha-payokha. Limbikitsani ofalitsa kuti akagaŵile kwa anthu ambili Galamukani! Na. 6 2017. Popeza colinga cathu ndi kukambilana na anthu mwacindunji, tisamasiye magaziniyi panyumba imene palibe anthu.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zofunikila za Mpingo: (5 min.)
Cinenelo Coyela Cimalimbikitsa Mtendele na Mgwilizano (Zef. 3:9): (10 min.) Kukambilana kozikidwa pa Nsanja ya August 15, 2012, peji 12, pala. 4. Tambitsani vidiyo yakuti Anthu Amene Kale Anali Kuzondana Akhala Mabwenzi.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) kr nkhani 22 mapa. 8-16
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 22 na Pemphelo