August 13-19
LUKA 19-20
Nyimbo 84 na Pemphelo
Mau Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Phunzilamponi Kanthu pa Fanizo la Ndalama 10 za Mina”: (10 min.)
Luka 19:12, 13—“Munthu wina wa m’banja lacifumu” anauza akapolo ake kuti acite malonda mpaka iye atabwela (jy peji 232 mapa. 2-4)
Luka 19:16-19—Akapolo okhulupilika anali na maluso osiyana, koma aliyense wa iwo analandila mphoto (jy peji 232 pala. 7)
Luka 19:20-24—Kapolo woipa analephela kuseŵenza ndipo zinthu sizinamuyendele bwino (jy peji 233 pala. 1)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Luka 19:43—Kodi mau a Yesu amenewa anakwanilitsika bwanji? (“mpanda wazisonga” nwtsty mfundo younikila)
Luka 20:38—Kodi mau a Yesu amalimbitsa bwanji cikhulupililo cathu cakuti akufa adzauka? (“pakuti kwa iye onsewa ndi amoyo” nwtsty mfundo younikila)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Luka 19:11-27
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo.
Vidiyo ya Kubwelelako Koyamba: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
Nkhani: (6 min. olo kucepelapo) w14 8/15 mape. 29-30—Mutu: Kodi Yesu pa Luka 20:34-36 Anali Kukamba za Ciukililo ca Padziko Lapansi?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Webusaiti Yathu ya JW.ORG”: (15 min.) Kukambilana. Tambitsani vidiyoyi.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 33
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 116 na Pemphelo