November 12-18
MACHITIDWE 1-3
Nyimbo 104 na Pemphelo
Mawu Oyamba (3 min. olo kucepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mzimu Woyela Unatsanulidwa pa Mpingo Wacikhristu”: (10 min.)
[Tambitsani vidiyo yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Machitidwe.]
Mac. 2:1-8, 14, 37, 38, 41—Ophunzila a Yesu atalandila mzimu woyela analalikila uthenga wabwino. Zimenezi zinapangitsa kuti anthu pafupi-fupi 3,000 abatizike
Mac. 2:42-47—Ophunzila a Yesu anaonetsa khalidwe la kuwolowa manja komanso kuceleza kwakukulu. Izi zinathandiza kuti amene anali atangobatizika kumene akhalitseko ku Yerusalemu na kuti cikhulupililo cawo cilimbe.(w86 12/1 peji 29 mapa. 4-5, 7)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (8 min.)
Mac. 3:15—N’cifukwa ciani Yesu akuchedwa “Mtumiki Wamkulu wa moyo”?(it-2 peji 61 pala. 1)
Mac. 3:19—Kodi vesiyi ionetsa kuti Yehova amawakhululukila bwanji ocimwa amene alapa? (cl peji 265 pala. 14)
Kodi imwe pacanu, kuŵelenga Baibo kwa wiki ino kwakuphunzitsani ciani za Yehova?
Ni cuma ca kuuzimu cina citi cimene mwapeza pa kuŵelenga Baibo kwa wiki ino?
Kuŵelenga Baibo: (4 min. olo kucepelapo) Mac. 2:1-21
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (2 min. olo kucepelapo) Seŵenzetsani makambilano acitsanzo.
Vidiyo ya Kubwelelako Koyamba: (5 min.) Tambitsani na kukambilana vidiyoyi.
Nkhani: (6 min. olo kucepelapo) it-1 peji 129 mapa. 2-3—Mutu: N’cifukwa Ciani Yudasi Analoŵedwa M’malo Pamene Atumwi Ena Amene Anamwalila Ali Okhulupilika Sanaloŵedwe M’malo?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kugwilizana Polalikila M’gawo la Vitundu Vosiyana-siyana”: (15 min.) Nkhani yokambilana yokambiwa na woyang’anila utumiki. Tambitsani na kukambilana vidiyoyi. Fotokozani makonzedwe amene alipo a mmene mudzalalikilila gawo la anthu okamba vitundu vosiyana-siyana.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 43 mapa. 1-7
Kubwelelamo na Kuchulako za Wiki Yotsatila (3 min.)
Nyimbo 68 na Pemphelo