CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 7-9
Umbeta ni Mphatso
Kwa zaka zambili, Akhristu ambili amakamba kuti kukhala mbeta kuli na maubwino apadela. Kumawathandiza kuwonjezela utumiki, kupeza mabwenzi osiyana-siyana, komanso kuyandikila kwambili Yehova.
Ali pa ulendo wokalalikila ku Australia, mu 1937; Wotsiliza sukulu ya Giliyadi afika ku Mexico, kumene anatumizidwa, mu 1947
Alalikila ku Brazil; kilasi ya Sukulu ya Alengezi a Ufumu ku Malawi
ZOFUNIKA KUSINKHA-SINKHA: Ngati ndinu mbeta, mungacite ciani kuti umbeta wanu ukhale waphindu?
Kodi anthu mu mpingo angacite ciani kuti alimbikitse na kuthandiza aja amene ni mbeta?